44. Ad-Dukhaan
1Ha Mim
2Ndilumbira pali Buku limene limanena zoona
3Ife tidalivumbulutsa ilo mu usiku wodalitsika. Ndithudi Ife tili kupitirizabe kuchenjeza
4Mu umenewu, ntchito iliyonse ili kuonetsedwa poyera
5Lamulo lochokera kwa Ife, ndithudi Ife timatumiza
6Chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa
7Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni
8Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale
9Iyayi! Iwo amakayika, amasewerera
10Motero dikirani tsiku limene kumwamba kudzatsitsa utsi wooneka
11Umene udzazungulira anthu ndipo chimenechi ndi chilango chowawa
12Iwo adzati, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango ichi chifukwa tsopano takhulupirira.”
13Kodi iwo angachenjezedwe bwanji pamene kunadza kale Mtumwi amene anali kuwauza choonadi
14Iwo adamutembenukira ndi kumati, “Munthu wophunzitsidwa ndi anthu ena, munthu wamisala.”
15Ndithudi Ife tidzachotsa chilango pa kanthawi kochepa koma ndithudi inu mudzabwerera
16Patsiku limene Ife tidzakugwirani mwamphamvu. Ndithudi tidzawabwezera chilango choyenera
17Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka
18Naati “Bweretsani kwa ine akapolo a Mulungu.” “Ndithudi ine ndine Mtumwi wokhulupirika kwa inu.”
19“Ndipo musachitire mwano Mulungu. Ndithudi ine ndadza kwa inu ndi ulamuliro wooneka.”
20“Ndipo ndithudi ine ndapempha chitetezo cha Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti musandiononge.”
21“Koma ngati inu simundikhulupirira ine, ndiye mundisiye ndekha.”
22Ndipo iye anati kwa Ambuye wake, “Anthu awa ndi ochimwa.”
23Choka iwe ndi akapolo anga nthawi yausiku. Ndithudi iwe udzalondoledwa
24“Ileke nyanja kukhala monga mmene ili. Ndithudi iwo ndi anthu amene adzamizidwa.”
25Kodi ndi minda ingati ndiponso a kasupe angati amene iwo adasiya
26Ndi minda ya chimanga ndi malo olemekezeka
27Ndi zinthu zabwino zimene amasangalala nazo
28Kotero zinali choncho. Ndipo Ife tidawasankha anthu ena kuti atenge zinthu zawo
29Kumwamba kapena dziko lapansi silidakhetse msozi chifukwa cha iwo ndipo iwo sadapatsidwe mpumulo
30Ndithudi tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango chochititsa manyazi
31Chimene chidaperekedwa ndi Farawo. Ndithudi iye adali wamwano ndi mmodzi wa anthu oswa malamulo
32Ndithudi tidawasankha iwo kuti akhale ndi nzeru kuposa mitundu ina
33Ndipo tidawapatsa chivumbulutso chimene chidali ndi mayesero ooneka
34Ndithudi iwo akuti
35“Palibe china chilichonse kupatula imfa yathu yoyamba ndipo ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.”
36“Kotero bweretsa makolo athu ngati zimene ukunena ndi zoona!”
37Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa
38Ndipo ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo mwamasewera
39Ife sitidazilenge zonsezi kupatula mwachoonadi ndipo ambiri a iwo sadziwa
40Ndithudi tsiku lachimaliziro ndi tsiku lomaliza kwa iwo onse
41Ndi tsiku limene bwenzi sadzakumbukira bwenzi ake ndipo sadzalandira chithandizo
42Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha
43Ndithudi mtengo wa Zaqqum
44Udzakhala chakudya cha anthu ochimwa
45Monga mafuta owira, chidzabwata m’mimba mwawo
46Monga ngati madzi ogaduka
47“Mugwire iye ndipo mududuzireni m’kati mwa Gahena.”
48Ndipo thirani pamutu pake chilango cha madzi owira
49“Lawani ichi! Ndithudi inu munali amphamvu ndi aulemu.”
50“Ndithudi! Ichi ndicho chimene munali kukayika.”
51“Ndithudi! Iwo amene amalewa zoipa adzakhala kumalo otetezedwa.”
52Pakati pa minda ndi a kasupe
53Iwo atavala Silika wokhuthala ndi wokongola, atakhala moyang’anizana
54Kotero zidzakhala choncho ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa akazi a maso aakuluakulu okongola
55Iwo adzaitanitsa chipatso cha mtundu uliwonse mwamtendere ndi mokhazikika
56Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena
57Chisomo chochokera kwa Ambuye wako! Chimenechi chidzakhala chinthu chopambana kwambiri
58Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira
59Kotero iwe dikira chifukwa nawonso ali kudikira
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath