Chisilamu
kubwerera

42. Ash-Shura

1Ha Mim

2Ain Sin Qaf

3Motero Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru amatumiza chivumbulutso kwa iwe monga anali kuvumbulutsira kwa iwo amene adalipo iwe usanabadwe

4Iye ndiye Mwini wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndipo Iye ndi wapamwamba, ndiponso wamkulu

5Kumwamba kumafuna kuphulika chifukwa cha ulemerero wake ndipo angelo amaimba mayamiko a Ambuye wawo ndipo amapempha chikhululukiro cha zolengedwa zonse za padziko lapansi. Ndithudi, Mulungu, ndiye amene amakhululukira ndipo ndi Mwini chisoni chosatha

6Ndipo iwo amene amasankha ena ake kukhala atetezi awo m’malo mwake, Mulungu amawayang’anira ndipo iwe ulibe ulamuliro pa iwo

7Kotero tavumbulutsa kwa iwe Buku la Korani m’Chiarabu, kuti ukhoza kuchenjeza make wa Mizinda ndi iyo youzungulira. Ndipo kuti uchenjeze za tsiku la chiweruzo limene mosakayika lidzadza pamene gulu lina lidzakhala ku Paradiso ndi gulu linzake lidzakhala kumoto

8Ndipo ngati Mulungu akadafuna, akadawapanga onse kukhala mtundu umodzi koma Iye amasankha amene wamufuna kulandira chisomo chake ndipo onse osalungama sadzapeza mtetezi kapena wowathandiza

9Kodi kapena iwo asankha kuti aziwapembedza atetezi ena m’malo mwake? Koma Mulungu ndiye Mtetezi. Ndipo ndiye amene amapereka moyo kwa akufa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

10Ndipo pa chilichonse chimene mumatsutsana, chiweruzo chake chili ndiMulunguMwiniwake.AmeneyondiMulunguweniweni, Ambuye wanga ndipo mwa Iye ine ndimakhulupirira ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa machimo anga

11Namalenga wakumwamba ndi dziko lapansi. Iye adalenga anzanu kuchokera pakati panu ndi anzawo kuchokera ku nyama. Mwanjira imeneyi Iye amakulengani inu. Palibe chilichonse chofanana naye ndipo Iye ndi wakumva ndi woona

12Iye ndiye amene ali ndi makiyi a kumwamba ndi a pa dziko lapansi. Iye amachulukitsa kapena kuchepetsa chakudya cha aliyense amene wamufuna. Ndithudi Iye amadziwa bwino za chinthu china chilichonse

13Iye wakukhazikitsirani chipembedzo chimene adakhazikitsira Nowa kuti atsatire, ndi chimene tavumbulutsa kwa iwe, ndi chimene tidakhazikitsira Abrahamu ndi Mose ndi Yesu powauza kuti inu mukhazikitse chipembedzo ndipo musapatukane. Ndi kovuta kuti anthu osakhulupirira atsatire zimene iwe uwaitanira. Mulungu amasankha yekha onse amene wawafuna ndipo amatsogolera onse amene amagonja kwa Iye

14Koma iwo adapatukana pamene nzeru zidadza kwa iwo ndipo anali kuchitirana mwano. Koma kukadakhala kuti padalibe mawu amene adanenedwa kale kuchokera kwa Ambuye wako wokhudza chimaliziro, chiweruzo chikadadza kale pa iwo. Ndipo, ndithudi, iwo amene adalandira Buku pambuyo pawo, ndithudi, ali ndi chikayiko chachikulu pa icho

15Kotero pitiriza kuwaitana ndipo limbikira potsatira njira yoyenera monga momwe walamulidwira. Iwe usatsatire zilakolako zawo zachabe, ndipo nena, “Ine ndimakhulupirira mawu onse a Mulungu amene wavumbulutsa mu Buku lake, ndipo ine ndalamulidwa kuonetsa chilungamo pakati panu. Mulungu ndi Ambuye wathu ndiponso Ambuye wanu. Kwa ife ntchito zathu ndipo kwa inu ntchito. Ndipo palibe mkangano pakati pa ife ndi inu. Mulungu adzatisonkhanitsa tonse ndipo ndi kwa Iye kumene tonse tidzabwerera.”

16Ndipo iwo amene amatsutsa za Mulungu atavomereza kale kuti adzamumvera, mitsutso yawo siidzakhala yomveka kwa Ambuye wawo ndipo mkwiyo wake udzadza pa iwo ndipo iwo adzalangidwa kwambiri

17Ndi Mulungu amene watumiza Buku mwachoonadi ndi muyeso. Kodi ndi chiyani chimene chingakudziwitseni inu kuti mwina ola lachiweruzo lili pafupi

18okhawo amene sakhulupilira amafuna kuti ola lidze msanga pamene onse amene amakhulupirira amaliopa ilo chifukwa amadziwa kuti ndi loonadi. Ndithudi onse amene amakana za olali ndi otayika kwambiri

19Mulungu ndi wachifundo ndi wachisoni kwa akapolo ake. Iye amapereka chakudya kwa aliyense amene wamufuna. Ndipo Iye ndi wamphamvu ndi Mwini mphamvu zonse

20Aliyense amene afuna zabwino za m’moyo umene uli nkudza, Ife tidzamupatsa zambiri ndipo wina aliyense amene afuna zabwino za m’moyo uno tidzamupatsa koma iye sadzakhala ndi gawo lina m’moyo umene uli nkudza

21Kodi kapena iwo ali ndi anzawo amene akhazikitsa chipembedzo china popanda chilolezo cha Mulungu? Ndipo pakadapanda kuti mawu adanenedwa kale, chiweruzo chikadafika kale pakati pawo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzalandira chilango chowawa kwambiri

22Iwe udzawaona anthu ochimwa ali ndi mantha chifukwa cha ntchito zawo ndipo ndithudi mazunzo adzadza pa iwo pamene iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzakhala ku Paradiso. Iwo adzalandira, kuchokera kwa Ambuye wawo zonse zimene adzafuna. Chimenechi ndicho chisomo chachikulu

23Imeneyi ndi nkhani yabwino imene Mulungu ali kuwauza akapolo ake amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Nena, “Ine sindili kukupemphani malipiro ayi kupatula kuti muzionetsa chikondi kwa ine chifukwa cha ubale wanga ndi inu.” Ndipo aliyense amene alandira chabwino, tidzamuonjezera zabwino zambiri mofanana ndi izo. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wokonzeka kulipira

24Kapena iwo akuti, “Iye wapeka yekha bodza lokhudza Mulungu?” Ngati Mulungu akadafuna akadatseka mtima wako. Ndipo Mulungu amafafaniza bodza ndi kukhazikitsa choonadi ndi mawu ake. Ndithudi Iye amadziwa zinsinsi zonse zimene zili m’mtima

25Ndiye amene amavomera kulapa kwa akapolo ake ndipo Iye amawakhululukira machimo awo ndipo Iye amadziwa zonse zimene mumachita

26Ndipo Iye amayankha onse amene amakukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndipo amawapatsa zambiri kuchokera ku chisomo chake. Akakhala anthu osakhulupirira iwo adzalandira chilango chowawa

27Ndipo ngati Mulungu akadaonjezera zabwino kwa akapolo ake, ndithudi, iwo akadaswa malamulo mopyola muyeso pa dziko lonse. Koma Iye amatumiza atayesa mwachifuniro chake. Ndithudi Iye amalemekeza akapolo ake, amadziwa zonse ndipo amayang’anitsitsa akapolo ake

28Ndipo ndiye amene amagwetsa mvula pa nthawi imene iwo ataya chikhulupiriro ndipo amaonetsa chifundo chake ponseponse. Ndipo Iye ndiye Mtetezi wamphamvu ndi Woyenera kulemekezeka

29Ndipo pakati pa zizindikiro zake, pali kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi zolengedwa zamoyo zimene adazimwaza monsemu. Ndipo Iye ali ndi mphamvu yozisonkhanitsa zonse pamodzi pamene Iye wafuna

30Ndipo mavuto onse amene amagwa pa inu amadza chifukwa cha ntchito zanu. Komabe Iye amakukhululukirani zolakwa zanu zambiri

31Ndipo inu simungathe kuthawa padziko lapansi ndipo inu mulibe wina aliyense kupatula Mulungu amene angakutetezeni kapena kukuthandizani

32Ndipo pakati pa zizindikiro zake pali zombo zonga mapiri zimene zimayenda pa nyanja

33Ngati Iye afuna, Iye amaimitsamphepondipoiwoamaimaosayendapamwamba pa nyanja. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa aliyense amene amapirira ndipo amayamika

34Kapena akhoza kuwaononga chifukwa cha zolakwa zimene iwo adachita. Koma Iye amawakhululukira zolakwa zambiri

35Onse amene amakana chivumbulutso chathu ayenera kudziwa kuti alibe malo othawirako

36Motero chilichonse chimene mwapatsidwa padziko lapansindichongosangalatsacham’moyounokomachimene chilindi Mulungundichabwinondiponsochosathakwaiwo amene amakhulupirira ndipo amaika chikhulupiriro chawo mwa Ambuye wawo

37Ndi iwo amene amapewa kuchita machimo aakuluakulu ndi zinthu zochititsa manyazi ndipo pamene akwiya amakhululuka

38Iwo amene amamvera kuitana kwa Ambuye wawo ndipo amapemphera panthawi yake amachita zinthu zawo atakambirana ndiponso amapereka kuchokera ku zinthu zimene tawapatsa iwo

39Ndiiwoameneakaponderezedwa,amabwezera

40Ndipo kubwezera kwa ntchito zoipa ndi choipa cholingana ndi ntchitozo ngati munthu akhululukira mnzake ndi kusintha maganizo ake, iye adzalandira mphotho yake kuchokera kwa Mulungu. Ndithudi Iye sakonda anthu osalungama

41Ndipo aliyense amene amabwezera ataponderezedwa, iye sadzakhala ndi mlandu wina uliwonse

42Mlandu uli pa iwo amene amapondereza anthu pochita zoipa ndipo mwamwano amaswa malamulo mopyola muyeso padziko. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chowawa kwambiri

43Ndipo, ndithudi, aliyense amene aonetsa kupirira ndi chikhululukiro, chimenechi ndi chimodzi cha zinthu zimene zimayamikidwa ndi Mulungu

44Kwa aliyense amene Mulungu amusocheretsa, kulibe wina amene angamuteteze. Ndipo iwe udzawaona anthu ochita zoipa pamene iwo adzaona chilango ali kunena kuti, “Kodi pali njira yoti tingathe kubwerera?”

45Ndipo iwe udzawaona ali kubweretsedwa kuchilango monyozedwa ndipo ali ndi nkhope zachisoni. Ndipo iwo amene amakhulupirira adzati, “Ndithudi otayika ndi anthu amene adzitaya ndi owatsatira awo patsiku lachiweruzo. Ndithudi anthu ochita zoipa adzakhala ku chilango chosatha.”

46Ndipo iwo sadzakhala ndi abwenzi oti awathandize kupatula Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu wamusocheza alibe wina womutsogolera

47Kotero bwererani kwa Ambuye wanu mwamsanga tsiku limene simungathe kubwerera lisanadze. Inu simudzakhala ndi kothawira pa tsiku limeneli ndipo inu simudzakhala ndi mwayi wokana

48Koma ngati iwo akana, Ife sitidakutumize iwe ngati owayang’anira iwo. Udindo wako ndi kungopereka uthenga. Ndipo, ndithudi, ngati Ife timupanga munthu kulawa chisomo chathu, iye amasangalala kwambiri chifukwa cha chisomocho koma ngati vuto lidza pa iwo chifukwa cha zolakwa zawo zimene adachita, ndithudi munthu amakhala osayamika

49Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi Mwini wake ndi Mulungu. Ndipo Iye amalenga chimene wafuna. Iye amapereka ana aakazi kwa amene Iye wamufuna ndipo amapereka ana aamuna kwa amene wamufuna

50Kapena amawapatsa, ana aamuna ndi ana aakazi, ndipo amapanga amene wamufuna kuti akhale chumba. Ndithudi iye amadziwa zonse ndipo amatha kuchita chilichonse

51Si koyenera kuti Mulungu ayankhule ndi munthu kupatula kudzera m’chivumbulutso kapena kuchokera kumalo obisika kapena potumiza Mtumwi kudzawauza, chimene Mulungu afuna ndi chilolezo chake. Ndithudi Iye ndi wapamwamba ndi wanzeru zosatha

52Kotero, mwaulamuliro wathu, tatumiza chivumbulutso chathu kwa iwe. Iwe siumadziwa kuti chivumbulutso chidali chiyani kapena kuti chikhulupiriro chidali chiyani. Koma Ife tachipanga icho kukhala muuni umene timatsogolera nawo akapolo athu mwachifuniro chathu. Ndithudi iwe umalangiza anthu ku njira yoyenera

53Njira ya Mulungu amene ali Mwini wake wa chilichonse chimene chili mlengalenga ndi chilichonse chimene chili pa dziko lapansi. Ndithudi kwa Mulungu zinthu zonse zimabwerera

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath