38. Saad
1Suad. Pali Korani yodzadza ndi chikumbutso
2Iyayi! anthu osakhulupirira ali kungodzikundikira ndi kumangotsutsa
3Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaononga iwo asanadze ndipo iyo idalira poona kuti padalibe nthawi yothawa
4Ndipo iwo ali kudabwa kuti Mtumwi wadza kwa iwo kuchokera pakati pawo. Ndipo anthu osakhulupirira amati, “Uyu ndi munthu wamatsenga ndiponso wabodza!”
5“Kodi iye wapanga milungu yonse kukhala Mulungu mmodzi? Ndithudi ichi ndi chinthu chachilendo.”
6Ndipo atsogoleri awo amachoka monyinyirika nati, “Pitirizani inu ndipo mudzipereke kwathunthu kwa milungu yanu! Ndithudi ichi ndi chinthu choti chikusokonezani.”
7“Ife sitidamvepo zimenezi pakati pa anthu akale. Ichi si china koma nkhani zopeka chabe.”
8“Kodi uthenga wavumbulutsidwa kwa iye yekha pakati pathu?” Iyayi! Koma iwo ali kukayika za uthenga wanga. Iyayi! Iwo sadalawepo chilango changa
9Kapena iwo ndi nkhokwe za chifundo cha Ambuye wako, Mwini Mphamvu zonse, Mwini kupereka zabwino zonse
10Kapena iwo ali ndi ulamuliro kumwamba ndi padziko ndi kuti zonse zimene zili m’menemo ndi zawo? Ngati nditero, alekeni iwo kuti akwere mothandizidwa
11Iwo adzagonjetsedwa monga magulu akale
12Asanadze iwo, panali ena amene adakana Atumwi. Anthu a Nowa, a Aad, ndi a Farawo, mfumu ya zisonga
13Thamoud ndi anthu a Loti ndi anthu okhala m’nkhalango, onsewa adali wothandizana
14Panalibe mmodzi amene sadanene kuti Atumwi adali abodza, motero chilango changa chinali chowayenera
15Ndipo awa ali kungodikira kulira kumodzi kokha kumene kuchitike mosachedwa
16Iwo amati, “Ambuye wathu, bweretsani msanga kwa ife Buku la ntchito zathu ngakhale nthawi yake siinakwane.”
17Khala wopirira pa zimene ali kunena ndipo uzikumbukira kapolo wathu Davide, munthu wamphamvu. Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse
18Ndithudi Ife tidauza mapiri kuti aziyimba pamodzi ndi iye mayamiko athu nthawi ya madzulo ndi m’mbandakucha
19Ndipo mbalame zidasonkhana, zonse pamodzi ndi iye zidalemekeza Mulungu
20Tidalimbikitsa Ufumu wake ndipo tidamupatsa nzeru ndi kuweruza kwabwino m’manenedwe ndi m’chiweruzo
21Kodi nkhani ya anthu okangana yakupeza iwe? Pamene, iwo adakwera chipupa cha nyumba ndi kulowa mnyumba ya padera
22Pamene adalowa kwa Davide, iye adachita mantha ndi iwo ndipo iwo adati, “Usaope. Ife ndife anthu okangana, ndipo wina wa ife wachimwira mnzake motero weruza mwachilungamo ndipo usatiweruze opanda chilungamo koma titsogolere ku njira yoyenera.”
23“Ndithudi uyu ndi m’bale wanga ndipo ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi kudza mphambu zisanu ndi zinayi pamene ine ndili ndi nkhosa imodzi yokha basi. Komabe iye akuti, ‘Undipatse ine nkhosayo’ ndipo iye adandipambana mu zonena zake.”
24Iye adati, “Ndithudi iye wakulakwira kwambiri pokupempha kuti nkhosa yako imodzi yokha iperekedwe kwa iye kuonjezera pa zimene ali nazo.” Ndithudi anthu ambiri ochitira pamodzi malonda ndi amene akulakwirana wina ndi mnzake. Koma izi sizichitika ndi anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndipo anthu otere ndi ochepa. Ndipo Davide adazindikira kuti Ife tidamuyesa iye ndipo adapempha chikhululukiro kwa Ambuye wake ndipo iye adagwa nagunditsa mphumi yake pansi ndi kudza molapa
25Kotero Ife tidamukhululukira ndipo ndithudi adali kufupi ndi Ife ndipo ali ndi malo okongola pa nthawi yobwerera
26Iwe Davide! Ndithudi Ife takukhazika iwe kukhala Kazembe padziko lapansi motero weruza pakati pa anthu mwachilungamo, ndipo usatsatire zilakolako za mtima wako chifukwa zidzakusocheretsa ku njira ya Mulungu. Ndithudi iwo amene asochera ku njira ya Mulungu adzalangidwa kwambiri chifukwa iwo amaiwala za tsiku lachiweruzo
27Si kuti tidasowa chochita polenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’kati mwake! Amenewo adali maganizo a anthu osakhulupirira! Ndipo tsoka kwa anthu osakhulupirira lochokera ku moto
28Kodi Ife tingasamale mofanana anthu okhulupirira ndi ochita ntchito zabwino ndi iwo amene amadzetsa chisokonezo pa dziko? Kapena Ife tingasamalire anthu amene amalewa zoipa chimodzimodzi ndi iwo amene amachita zoipa
29Ili ndi Buku limene Ife tatumiza kwa iwe, lodzala ndi madalitso kuti akhoza kuganiza mofatsa pa mavesi ake ndi kuti anthu ozindikira akhoza kukumbukira
30Kwa Davide Ife tidamupatsa Solomoni. Kapolo wabwino zedi! Ndithudi iye anali kudzalapa kwa Ife
31Ndipo pamene adadza nazo kwa iye, nthawi ya madzulo, Hatchi zophunzitsidwa bwino zamphamvu ndi zoberekedwa bwino
32Ndipo iye adati, “Ndithudi ine ndidakonda chuma kuposa kukumbukira Ambuye wanga. Mpaka pamene nthawi idatha ndipo dzuwa lidalowa mu mdima.”
33Ndipo iye adati “Bweretsani mahatchi kwa ine.” Ndipo iye adayamba kuzisisita miyendo ndi makosi awo
34Ndipo, ndithudi, Ife tidamuyesa Solomoni ndipo Ife tidaika Satana pa mpando wake wachifumu koma iye adadza kwa Ife modzipereka ndi molapa
35Iye adati, “Ambuye wanga! Khululukireni ndipo ndipatseni ufumu umene simudzapatsanso wina pambuyo panga chifukwa inu mumapereka zokoma zanu mopanda muyeso.”
36Ndipo Ife tidamuchepetsera mphamvu yakuti mphepo imvere malamulo ake kuti iziyenda potsatira malamulo ake amene iye adalamula
37Ndiponso a Satana ochokera kwa majini ndi m’misiri aliyense womanga nyumba ndi wodziwa kusambira pa madzi
38Ndi ena omwe ndi omangidwa ku magoli
39Iyi ndi mphatso yathu yaulere, kotero pereka mowolowa manja kapena kuisunga. Iwe siudzaimbidwa mlandu
40Ndipo ndithudi iye adali pafupi ndi Ife, ndi kubwera ku malo abwino
41Ndipo kumbukira kapolo wathu Yobu pamene adapempha kwa Ambuye wake kuti, “Satana wandikundikira mavuto ndi masautso.”
42“Menya nthaka ndi phazi lako. Uyu ndi kasupe wa madzi oti usambe, ozizira ndi okoma pakumwa.”
43Ndipo Ife tidamubwezera banja lake ndi kuonjezera chiwerengero chawo ngati chisomo chochokera kwa Ife ndiponso chikumbutso kwa anthu ozindikira
44Ndipo nyamula m’manja mwako mtolo wa udzu ochepa ndipo mumenye nawo koma usaphwanye lonjezo lako. Ndithudi! Ife tidamupeza ali wopirira kwambiri ndi okhazikika. Ndithudi iye adali Mtumwi wabwino! Ndithudi iye anali kulapa nthawi zonse
45Ndipo kumbukira akapolo athu Abrahamu, Isake, Yakobo ameneadaliodzalandimphamvundiponsoomvetsa zinthu za chipembedzo
46Ndithudi tidawasankha iwo ndi kuwapatsa chikumbumtima chamoyo umene uli nkudza
47Ndipo iwo timawaona. Ndithudi ali m’gulu la anthu odziwika ndi abwino
48Ndipo kumbukira Ishimayeli, Elisa, ndi Dhul-Kifl onse adali m’gulu la anthu ochita zabwino
49Ichi ndi chikumbutso, ndithudi, kwa anthu olungama awo ndi malo abwino
50Minda yosatha imene makomo ake adzakhalaotsekulidwakwaiwonthawizonse
51M’menemo iwo adzakhala mwamtendere ndiponso m’menemo iwo adzaitanitsa zipatso zochuluka ndi zakumwa zokoma
52Ndipo pambali pawo padzakhala a namwali angwiro ongoyang’ana maso awo pa amuna ofanana nawo zaka
53Limeneli ndi lonjezo limene lapatsidwa kwa inu lokhudza tsiku lachiweruzo
54Ndithudi zimenezi ndi zokoma zathu kwa inu ndipo sizidzatha ayi
55Izi zili choncho. Ndipo zoonadi anthu ochita zoipa adzakhala ku malo oipa kupitako
56Gahena! Ndi kumene iwo adzalowa ndipo ndi malo oipa kukhalamo
57Izi zili choncho! Kotero alekeni iwo alawe madzi owira ndi mafinya
58Ndi zilango zina zofanana zawo ndi zina zosiyanasiyana
59Ili ndi gulu la nkhondo limene lili kulowa ndi inu! Palibe kulandiridwa kwabwino kwa iwo! Ndithudi iwo adzalowa kumoto
60Iwo adzati, “Iyayi! Inunso. Simulandiridwa ayi. Ndinu amene mudatinyenga ife, kotero awa ndiwo malo oipa kwambiri kukhalako.”
61Iwo adzati, “Ambuye wathu! Aliyense amene adachititsa kuti zimenezi zidze kwa ife muonjezereni kawiri chilango chake cha kumoto.”
62Ndipo iwo adzati, “Kodi zachitika bwanji kuti ife sitili kuona anthu amene tinkawawerenga pakati pa anthu ochita choipa?”
63Kodi ife timangowanyoza kapena maso athu alephera kuwaona bwinobwino
64Ndithudi zimenezi ndi zoona. Zokangana za anthu a ku moto
65Nena, “Ndithudi ine ndine mchenjezi basi ndipo kulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha, wopambama ndi wofunika.”
66“Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo. Iye ndi wamphamvu zambiri ndi wokhululukira nthawi zonse.”
67Nena, “Uwu ndi uthenga wofunika kwambiri.”
68“Umeneinumulikuukana.”
69“Inesindidziwazamafumu olemekezeka pamene amatsutsana ndi kukambirana.”
70“Koma akuti ichi chavumbulutsidwa kwa ine kuti ndine opereka chenjezo lomveka ndiponso poyera.”
71Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa Angelo, “Ndithudi Ine ndidzalenga munthu kuchokera ku dothi.”
72Ndipo ndikatha kumulenga iye ndi kumupumira mzimu wanga kotero igwani nonse ndi kumulambira iye
73Kotero Angelo onse pamodzi adamulambira
74Kupatula Satana, iye anali ndi mwano ndipo iye anali mmodzi wa osakhulupirira
75Mulungu adati, “Iwe Satana! Chakuletsa ndi chiyani kulambira munthu amene ndalenga ndi manja anga? Kodi ndiwe wamwano? Kodi kapena iwe ndiwe mmodzi wa apamwamba?”
76Iye adati, “Ine ndine wopambana kuposa iye. Inu mudandilenga ine kuchokera kumoto pamene iye mudamulenga kuchokera ku dothi.”
77Mulungu adati, “Kotero choka pamaso panga chifukwa iwe ndiwe okanidwa ndi otembereredwa.”
78“Ndipo ndithudi matemberero anga adzakhala pa iwe mpaka pa tsiku lachiweruzo.”
79Satana adati, “Ambuye wanga! Ndipatseni mpata mpaka patsiku louka kwa akufa.”
80Mulungu adati, “Mpata waperekedwa kwa iwe.”
81“Mpaka pa nthawi yomwe idakhazikitsidwa.”
82Satana adati, “Kotero kudzera ku mphamvu zanu, ine ndidzawasocheretsa.”
83“Kupatula akapolo anu osankhidwa amene ali pakati pawo.”
84Mulungu adati, “Ichi ndi choonadi ndipo choonadi ndicho chimene ndimanena.”
85“Kuti ndidzadzadza Gahena ndi iwe ndiponso onse amene amakutsatira iwe.”
86Nena “Ine sindili kukufunsani malipiro chifukwa cha ichi ndiponso ine sindine wodziyenereza.”
87“Ichi si china koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse.”
88“Ndithudi nonse mudzadziwa choonadi chake nthawi ina.”
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath