Chisilamu
kubwerera

36. Yaseen

1Ya seen

2Ndili kulumbira pali Buku la nzeru la Korani

3Ndithudi iwe ndiwe mmodzi mwa amene adatumizidwa

4Pa njira yoyenera

5Ichi ndi chivumbulutso cha Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni

6Kuti uwachenjeze anthu amene makolo awo sadachenjezedwe, kotero iwo ndi osamvera

7Ndithudi liwu la chilango latsimikizidwa kwa ambiri a iwo koma iwo sali okhulupirira

8Ife taika magoli m’makosi mwawo, amene afika m’zigama ndipo mitu yawo yanyamulidwa

9Ife taika chotchinga kutsogolo kwawo ndiponso kumbuyo kwawo ndipo tawakuta maso awo kuti asaone

10Ndi chimodzimodzi kaya uwachenjeza kapena ayi ndipo iwo sadzakhulupirira

11Ukhoza kumuchenjeza yekhayo amene watsatira chikumbutso ndi kuopa Mwini Chisoni ngakhale kuti iye sangamuone. Kwa iye umuuze nkhani yabwino ya chikhululukiro ndi mphotho yopambana

12Ndife amene tidzadzutsa anthu akufa ndi kulemba ntchito zonse za anthu ndi zizindikiro zimene asiya m’mbuyo: Talemba zonse mooneka bwino kwambiri m’buku

13Apatse chitsanzo cha anthu a mu mzinda umene mudadza Atumwi

14Pamene Ife tidawatumizira iwo awiri, iwo adawakana. Motero Ife tidatumizanso wina wachitatu, ndipo iwo adati, “Ndithudi ife tatumizidwa kwa inu.”

15Iwo adati, “Inu ndinu anthu ngati ife tomwe. Mwini chisoni sadavumbulutse china chilichonse! Inu muli kunama basi.”

16Iwo adati, “Ambuye wathu akudziwa kuti ife tatumidwa.”

17“Udindo wathu ndi wongokuchenjezani basi.”

18Anthu adati, “Tili kuona malodza. Ngati mupitiriza tikuponyani miyala ndipo chilango chowawa chizadza pa inu.”

19Iwo adati, “Malodza anu akhale ndi inu! Kodi chifukwa chakuti mwachenjezedwa? Iyayi koma inu ndinu anthu ochimwa kwambiri

20Nthawi yomweyo munthu wina adadza ali kuthamanga kuchokera kumbali ina ya mzinda. Iye adati, “Anthu anga! Tsatirani iwo amene atumidwa ndi Mulungu.”

21“Atsatireni iwo amene safuna malipiro kuchokera kwa inu pokukumbutsani mawu a Mulungu ndipo ndi otsogozedwa bwino.”

22“Kodi pali chifukwa chotani chimene chingandilepheretse ine kuti ndim’pembedze Iye amene adandilenga popeza ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera?”

23“Kodi ine ndizipembedza milungu ina osati Iyeyo? Ngati ndi chifuniro cha Mwini chisoni kundizunza, kukhala pakati kwawo sikudzandithandiza ndipo iwo sadzandipulumutsa ayi.”

24“Ndithudi ine ndikadatero, ndikadakhala mu chisokonezo choonekeratu.”

25Ndithudi ine ndakhulupirira mwa Ambuye wanu choncho ndimvereni.”

26Kudanenedwa kwa iye kuti, “Lowa mu Paradiso.” Iye adafuula kuti, “Akadakhala kuti anthu anga adadziwa.”

27“Mmene Ambuye wanga wandionetsera chifundo chake kundiika mugulu la olemekezeka.”

28Ndipo Ife sitidatumize padziko lapansi, kwa anthu ake, gulu lochokera kumwamba kuti lilimbane nawo ndipo sikudali koyenera kuti Ife tichite choncho

29Udali mkuwo umodzi ndipo Oh! Onse adaonongedwa

30Kalanga akapolo anga! Iwo amaseka pofuna kunyoza Mtumwi aliyense amene adadza kwa iwo

31Kodi iwo sadaone mibadwo yakale imene tidaiononga zaka zikwizikwi iwo asanabadwe? Ndipo iwo sadzabwereranso

32onse, popanda opatuka, adzadza kwa Ife

33Chizindikiro kwa iwo ndi nthaka yakufa imene tidaidzutsa ndipo timatulutsa m’nthakamo nthangala zomwe iwo amadya

34Taika m’nthakamo minda ya mitengo ya tende ndi ya mphesa ndipo timathirira ndi madzi a m’kasupe

35Moti akhoza kumadya zipatso zake. Si manja awo amene adapanga zimenezi ayi. Kodi sangathokoze

36Ulemerero ukhale kwa Iye amene adalenga zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi) zimene zimamera m’nthaka ndi zina za mtundu wawo ndi zinanso zimene sazidziwa

37Chizindikiro cha kwa iwo ndi usiku. Kuchokera ku iwo timachotsa usana ndipo iwo amakhala mu mdima

38Dzuwa limayenda mofulumira kupita kumalo ake okapuma. Umenewu ndiwo ulamuliro wa Mwini Mphamvu zonse ndiponso Wodziwa chilichonse

39Ndipo mwezi tidaulamulira kuti uyende mumsewu wake mpaka pamene ukamabwerera ngati nthawi yoyamba m’maonekedwe

40Dzuwa sililoledwa kupitirira mwezi ndipo usiku siupyola usana. Chilichonse chimayenda mumsewu wake

41Ndipo chizindikiro china kwa iwo ndi chakuti tidanyamula makolo awo mu chombo chonyamula katundu

42Tidalenga zombo za mtundu umenewu kuti iwo azikweramo

43Timawamiza tikafuna ndipo palibe amene angawathandize ndipo sangathe kupulumutsidwa

44Kupatula kudzera m’chifundo chathu ndi kuwapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa

45Pamene zinenedwa kwa iwo kuti, “Opani chinthu chimene chili patsogolo panu ndi pambuyo panu kuti mwina Mulungu angakuonetsereni chifundo” ndipo iwo samvera ayi

46Ndithudi palibe chizindikiro chochokera kwa Ambuye wawo chimene iwo amachivomera. Ndipo iwo salabadira

47Ndipo pamene auzidwa kuti, “Perekani gawo la chopereka chaulere pa zinthu zimene Mulungu wakupatsani.” Anthu osakhulupirira amanena kwa anthu okhulupirira kuti, “Kodi ife tizidyetsa iwo amene Mulungu atafuna akhoza kuwadyetsa? Ndithudi inu ndi osochera kwambiri.”

48Iwo amanenanso kuti, “Kodi lonjezo limeneli la tsiku lachiweruzo lidzatsimikizidwa liti, ngati zimene uli kunenazi ndi zoona?”

49Angodikira mkokomo umodzi wokha basi umene udzadza pa nthawi imene iwo ali kutsutsana

50Iwo sadzakhala ndi mwayi wosiya mawu kapena kubwerera kwa abale awo

51Pamene lipenga lidzamveka, taona, kuchokera ku manda, anthu adzathamanga kupita kwa Ambuye wawo

52“Tsoka kwa ife!” Iwo adzatero. “Ndani amene watidzutsa kuchokera kumalo athu a mpumulo?” Ichi ndi chimene Ambuye wachifundo adalonjeza. “Atumwi adanenadi zoona!”

53Ndithudi ndi mfuwu umodzi wokha, onse panthawiyo, adzasonkhanitsidwa kwa Ife

54Patsiku limeneli sipadzakhala mzimu umene siudzaweruzidwa ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu

55Pa tsiku limeneli anthu okhala ku Paradiso adzakhala osangalala kwambiri

56Iwo pamodzi ndi akazi awo, adzakhala m’mithunzi ya nkhalango, pa mipando yawofowofo

57Iwo adzapeza m’menemo zipatso ndi zina zonse zimene adzafuna

58“Mtendere” ndiwo mawu amene adzachokere kwa Mulungu, Mwini Chisoni

59Ndipo Iye adzati, “Khalani kutali inu oipa tsiku lalero?”

60“Kodi Ine sindidakuchenjezeni, inu ana a Adamu, kuti musamagwadire Satana, chifukwa iyeyu ndi mdani wanu woonekeratu?”

61“Ndi kuti muzindipembedza Ine? Ndithudi imeneyo ndiyo njira yoyenera.”

62Koma iye adasocheretsa anthu ambiri. Kodi mudalibe nzeru

63Imeneyi ndiyo Gahena imene munali kulonjezedwa

64Lowani m’menemo tsiku lalero ngati chilango, chifukwa chakusakhulupirira kwanu

65Lero, Ife titseka pakamwa pawo, ndipo manja awo ndi amene ayankhule ndi Ife ndiponso miyendo yawo ichitira umboni pa ntchito zoipa zimene anali kuchita

66Chikadakhala cholinga chathu, tikadawachititsa khungu kuti azivutika poyenda. Nanga akadaona bwanji machimo awo

67Chikadakhala cholinga chathu, tikadawasintha kuti asanduke china chake pamalo pamene adaimirira, kuti asapite patsogolo kapena kubwerera m’mbuyo

68Aliyense amene timamukalambitsa, timam’bwezera ku ubwana. Kodi iwo sangazindikire chimenechi

69Ife sitidamuphunzitse iye ndakatulo ayi ndiponso si koyenera kuti akhale mlakatuli. Ichi si china koma chikumbutso ndi dongosolo la Korani

70Limene lichenjeza anthu a moyo ndi kupereka chiweruzo kwa anthu osakhulupirira

71Kodi iwo saona kuti pakati pa zinthu zimene tidalenga ndi manja athu tidawalengera nyama zimene iwo amazilamulira

72Tidalamula zimenezi kuti zizimvera malamulo awo kuti akhoza kumakwera ndi zina zoti azidya

73Ndipo amapezanso phindu lina lolekana. Iwo amamwa mkaka kuchokera ku izo. Kodi iwo sangathokoze

74Iwo akhazikitsa milungu ina powonjezera pa Mulungu weniweni, poganiza kuti mwina akhoza kuthandizidwa

75Milunguyo siingawathandize. Iwo adzatengedwa mwankhondo kunka ku chilango

76Usalole kuti mawu awo akumvetse chisoni. Ife tikudziwa zonse zimene azibisa ndi zonse zimene akuzionetsa

77Kodi munthu, sadziwa kuti tidamulenga kuchokera ku dontho la umuna? Koma iye ndi otsutsana ndi Ife poyera

78Iye amatifanizira Ife ndi zina zake ndipo amaiwala za chilengedwe chake. Iye amafunsa kuti, “Kodi ndani amene adzapereka moyo ku mafupa oola?”

79Nena “Iye amene adawalenga poyamba adzawapatsa moyo. Iye amadziwa chilichonse cha zolengedwa zake.”

80Iye amene amakupatsani moto kuchokera ku mtengo wauwisi umene inu mumawunikira

81Kodi Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, alibe mphamvu zolenga china chake chofanana nazo? Ndithudi ali nazo. Iye ndi Mlengi amene amadziwa chinthu china chilichonse

82Ndithudi pamene Iye afuna chinthu amangonena kuti, “Chikhale” ndipo chimakhaladi

83Ulemerero ukhale kwa Iye amene ali ndi ulamuliro pa chinthu china chilichonse; ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzabwerera

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath