Chisilamu
kubwerera

98. Al-Bayyina

1Iwo amene sakhulupirira a m’gulu la anthu a m’Buku ndi anthu opembedza mafano, sadzasiya kusakhulupilira mpaka pamene zizindikiro zooneka zitaperekedwa kwa iwo

2Mtumwi wochokera kwa Mulungu amene ali kuwerenga kuchokera pa Masamba oyera

3Amene ali ndi malamulo angwiro ndi omveka bwino ochokera kwa Mulungu

4Ndipo anthu okhulupirira Buku sanayambe kugawikana pakati pawo mpaka pamene zizindikiro zooneka zidaperekedwa kwa iwo

5Ndipo Al-Zalzala 659 iwo sadalamulidwe koma kuti azipembedza Mulungu ndipo kuti asapembedze wina aliyense koma Iye yekha ndipo kuti adzipemphera pa nthawi yake ndi kupereka msonkho wothandiza anthu osauka. Ndipo chimenechi ndicho chipembedzo chabwino

6Ndithudi iwo amene sakhulupirira amene ali pakati pa anthu a m’Buku, ndi anthu opembedza mafano, adzakhala ku moto wa ku Gahena. Iwo ndiwo oipa zedi pa zolengedwa zonse

7Ndithudi iwo amene atsatira chikhulupiriro choonadi ndipo amachita ntchito zabwino ndiwo olemekezeka pa zolengedwa zonse

8Mphotho yawo imene ili ndi Ambuye wawo ndi kuwaika m’minda imene imathiriridwa ndi madzi ya m’mitsinje pansi pake, kumene adzakhalako nthawi zonse. Mulungu ndi wosangalala ndi iwo ndipo nawonso ndi osangalala ndi Iye. M’menemo ndi m’mene munthu oopa Mulungu adzalandirire mphotho yake

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath