Chisilamu
kubwerera

96. Al-Alaq

1Werenga! M’dzina la Ambuye wako amene analenga

2Yemwe adalenga munthu kuchokera ku kadontho kamagazi oundana

3werenga! Ndipo Ambuye wako ndiye wopereka mowoolowa manja

4Amene anaphunzitsa ndi cholembera

5Anaphunzitsa munthu chimene sanali kuchidziwa

6Iyayi! Ndithudi, munthu amalakwa mopyola muyeso

7Chifukwa amaganiza kuti iye ndi oima payekha

8Ndithudi! Nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu

9Kodi mwamuona munthu amene amaletsa

10Kapolo pamene akupemphera

11Kodi mwamuona ngati iye alikutsatira chilangizo chabwino

12Kapena kulamulira machitidwe abwino

13Ndiuze ngati iye akana choonadi ndipo salabadira

14Kodi iye sadziwa kuti Mulungu amaona zinthu zonse

15Iyayi! Ngati iye sasiya, Ife tidzamududuluza pogwira tsitsi la pa mphumi pake

16Mphumi yabodza ndi yochimwa

17Ndipo mulekeni iye aitane anzake oti amuthandize

18Ife tidzaitana osunga Gahena

19Iyayi! Usamumvere iye. Gunditsa mphumi yako pansi ndipo idza pafupi ndi Mulungu

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath