93. Ad-Dhuhaa
1Pali usana
2Ndi pali usiku pamene ulipo
3Ambuye wako sadakutaye iwe ndiponso sakudana nawe ayi
4Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa moyo uno
5Ndithudi Ambuye wako adzakupatsa, ndipo iwe chidzakukondweretsa
6Kodi sadakupeze iwe uli wa masiye ndipo adakupatsa malo okhala
7Kodi sadakupeze uli wosochera ndipo Iye adakutsogolera
8Kodi sadakupeze iwe waumphawi ndipo adakulemeretsa
9Motero iwe usapondereze pansi mwana wa masiye
10Ndipo usapirikitse munthu wopempha
11Koma lengeza chisomo cha a Ambuye wako
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath