92. Al-Lail
1Paliusikupamenemdimaumayamba
2Ndimasanapamene kumayera
3Ndi pali Iye amene adalenga chachimuna ndi chachikazi
4Ndithudi zochita zanu zonse zili ndi mapeto osiyana
5Akakhala iye amene amapereka chaulere ndipo amamuopa Mulungu
6Ndipo amakhulupirira pochita zinthu zabwino
7Ife tidzamusalazira njira yake ya ku chipulumutso
8Koma iye amene sapereka chaulere ndipo amaganiza kuti ndi woima payekha
9Sakhulupirira ndipo sachita ntchito zabwino
10Tidzamusalazira njira yake ya ku chionongeko
11Kodi chuma chake chidzamuthandiza chiani pamene iye azidzazunzika
12Ndithudi ndi udindo wathu kupereka chilangizo
13Ndipo, ndithudi, zonse za m’moyo umene uli nkudza ndi za m’moyo uno ndi zathu
14Motero ndakuchenjezani za moto wa lawilawi
15Kulibe Al-Dhuha 655 munthu amene akapsye nawo kupatula munthu wochita zoipa
16Amene amakana choonadi ndipo safuna kumvera chenjezo
17Koma anthu onse olungama, adzatalikirana nawo
18Amene amapereka chaulere chake poonjezera kudziyeretsa
19Osati chifukwa chakuti afuna kupezako cholowa ayi
20Kupatula ndi cholinga chopeza chisomo cha Ambuye wake, wapamwamba mwamba
21Ndithudi iye adzasangalala
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath