Chisilamu
kubwerera

91. Ash-Shams

1Pali dzuwa ndi kuwala kwake

2Ndi pali mwezi umene umatuluka dzuwa litalowa

3Ndi masana pamene kumayera

4Ndi pali usiku umene umabisa

5Ndi pali Kumwamba ndi Iye amene adakulenga

6Ndi pali dziko lapansi ndi Iye amene analitambasula

7Ndi pali mzimu ndi Iye amene adaulenga

8Ndi kumupatsa iye nzeru zodziwa choipa ndi chabwino

9Ndithudi wopambana ndi amene amadziyeretsa

10Ndipo wolephera ndiye amene wadzidetsa

11Anthu a Thamoud adakana Mtumwi wawo poukiramoyerekedwa

12Pamenemunthuolakwakwambiri adayambitsa chipolowe

13Ndipo Mthenga wa Mulungu anati kwa iwo: “Samalirani ngamira ya ikazi ya Mulungu ndi tsiku lake lomwa madzi!”

14Iwo sadakhulupirire ayi ndipo ngamirayo adaipha. Motero Ambuye wawo adawaononga chifukwa cha machimo awo ndipo adafafaniza onse mosasankha

15Iye sadaope chotsatira chake

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath