Chisilamu
kubwerera

90. Al-Balad

1Ine ndili kulumbira pali Mzinda uwu

2Ndipo iwe uli ndi ufulu mu Mzinda uwu

3Ndi pali wobereka ndi chimene adabereka

4Ndithudi Ife tidamulenga munthu m’mavuto

5Kodi amaganiza kuti palibe wina aliyense amene ali ndi mphamvu pa iye

6Iye amanena monyada kuti: “Ine Al-Shams 653 ndaononga chuma chambiri.”

7Kodi iye amaganiza kuti palibe wina amene ali kumuona

8Kodi Ife sitidamupatse maso awiri

9Ndi lirime ndi milomo iwiri

10Ndi kumulangiza iye njira ziwiri

11Koma sayerekeza kutsata njira yozyolika

12Kodi chidzakuuza ndi chiani za njira yozyolika

13Ndi kumasula kapolo

14Kapena kupereka chakudya nthawi ya njala

15Kwa wamasiye amene ndi wachinansi

16Kapena munthu wosauka, wofuna chithandizo

17Ndipo iye anakhala mmodzi wa anthu amene akhulupirira, ndipo analangizana wina ndi mzake kupilira, kumva chisoni ndi kuonetsa chifundo

18Iwo ndiwo amene adzakhala kudzanja lamanja

19Koma iwo amene anakana chivumbulutso chathu, adzaima ku dzanja lamanzere

20Ndipo moto wa ku Gahena udzawakuta iwo

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath