89. Al-Fajr
1Pali m’mbandakucha
2Ndi pali usiku khumi
3Pali chofanana ndi chosiyana
4Pali usiku pamene uli nkutha
5Ndithudi m’menemu muli umboni wokwanira kwa anthu a nzeru
6Kodi iwe siudaone mmene Ambuye wako adakhaulitsira anthu a Aad
7Amene anali atali atali ngati nsanamila zitali zitali
8wolingana nawo amene sanalengedwepo padziko
9Ndi anthu a Thamoud, amene ankakumba nyumba zawo m’miyala ya m’dambo
10Ndi Farao, amene anali ndi zichiri
11Amene anali kuphwanya malamulo paliponse m’dziko
12Ndipo adachulukitsa chisokonezo
13Motero Ambuye wako adabweretsa chilango chosiyana siyana chowawa pa iwo
14Ndithudi Ambuye wako amaona
15Ndipo nthawi zonse munthu, pamene Ambuye wake amuyesa pomukweza ndi kumuonetsera chifundo chake, iye amati: “Ambuye wanga wandilemekeza ine.”
16Koma akamuyesa pomumana zinthu, iye amati: “Ambuye wanga ali kundizunza ine.”
17Iyayi! Koma inu simuonetsa chifundo kwa ana a masiye
18Ndi kuuzana kuti mudzidyetsa anthu osauka
19Inu mumalanda chuma cha anthu opanda mphamvu chifukwa cha umbombo
20Ndipo mumakonda chuma ndi mitima yanu yonse
21Iyayi! Koma pamene dziko lidzasinjidwa kukhala ufa
22Ndipo Ambuye wanu adzadza pamodzi ndi angelo ali pa mizere
23Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi patsikuli. Ndipo patsikuli munthu adzakumbukira. Koma, kodi chikumbumtima chake chidzamuthandiza motani
24Iye adzanena kuti: “Kalanga ine! Ndikanakhala ndinali kuchita zabwino pamene ndinali ndi moyo.”
25Motero patsikuli, palibe wina amene adzalanga monga momwe Iye adzalangire
26Ndipo palibe wina amene adzamanga monga ngati momwe Iye adzamangire
27oh! Iwe wokhutitsidwa
28Bwerera kwa Ambuye wako mosangalala ndi Iye, ndi Iye mosangalala ndi iwe
29Lowa m’gulu la akapolo anga wolemekezeka
30Ndipo lowa mu Paradiso yanga
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath