88. Al-Ghaashiya
1Kodi wamva za chinthu chachikulu chimene chili nkudza
2Nkhope zina, patsiku limeneli, zidzachititsidwa manyazi
3Pogwira ntchito zotopetsa
4Iwo adzalowa kumoto woyaka
5Iwo adzapatsidwa madzi oti amwe kuchokera kuchitsime cha moto
6Sadzakhala ndi chakudya china koma chiphe cha mtengo waminga
7Chimene sichidzawapatsa thanzi kapena kuthetsa njala
8Nkhope zina, pa tsikuli, zidzakhala zosangalala
9Adzakondwa chifukwa cha ntchito zawo
10Atakhala m’minda ya pamwamba
11Kumene iwo sadzamva zoononga kapena za bodza
12Mudzakhala kasupe wa madzi oyenda
13Ndi mipando yonyamuka ya wofowofo
14Ndi zikho zomwera zitaikidwa pambali pake
15Ndi makushoni yoikidwa m’mizere
16Ndi mikeka yoyalidwa bwino pansi pake
17Kodi iwo saona mmene ngamira zidalengedwera
18Ndi Kumwamba mmene kudakwezedwera
19Ndi mapiri mmene adalengedwera mokhazikika
20Ndi dziko mmene adalitambasulira
21Motero akumbutse, chifukwa udindo wako ndi wowakumbutsa
22Iwe sindiwe munthu wowakakamiza ayi
23Kupatula iye Al Fajr 651 amene abwerera m’mbuyo ndi kuyamba kusakhulupirira
24Motero Mulungu adzamulanga chilango chachikulu
25Ndithudi onse adzabwerera kwa Ife
26Ndipo, ndithudi, chiwerengero cha zochita zawo chidzakhala kwa Ife
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath