87. Al-A'laa
1Lemekeza dzina la Ambuye wako wapamwambamwamba
2Amene adalenga zonse ndi kuzikonza bwinobwino
3Amene adalamula tsogolo lawo ndi kuwatsogolera
4Amene amameretsa msipu
5Ndipo amausanduliza kukhala udzu ouma
6Tidzakuphunzitsa kulakatula chivumbulutso chathu ndipo sudzaiwala
7Kupatula chokhacho chimene Mulungu amafuna. Ndithudi Iye amadziwa chilichonse chooneka ndi chobisika
8Ndipo Ife tidzakufupikitsira, m’njira yaifupi
9Motero kumbutsa mwina chikumbutso chingawathandize
10Chikumbutso chidzalandiridwa ndi iye amene amaopa Mulungu
11Koma munthu wochimwa adzachisiya
12Amene adzaponyedwa mu ng’anjo yamoto ndi kulawa ululu wake
13Mmene iye sadzafa kapena kukhala ndi moyo
14Zoonadi iye amene adziyeretsa adzakhala wopambana
15Amene amakumbukira dzina la Ambuye wake ndipo amapemphera panthawi yake
16Iyayi, koma inu mumasangalala ndi zinthu za m’moyo uno
17Ndipo moyo umene uli nkudza ndi wabwino ndi wosatha
18Ndithudi! Zonsezi zidalembedwa mu Mabuku akale a Mulungu
19Mabuku a Abrahamu ndi Mose
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath