Chisilamu
kubwerera

86. At-Taariq

1Pali kumwamba ndi pali Nyenyezi yowala

2Kodi chidzakudziwitsa kuti Nyenyezi yowala ndi chiani

3Ndi Nyenyezi yowala kothobwetsa maso

4Ndithudi moyo uliwonse uli ndi mtetezi wake

5Tamulekani munthu kuti aganize kuti adalengedwa kuchokera ku chiyani

6Iye adalengedwa kuchokera ku madzi otuluka

7Amene amatuluka kuchokera pakati pa pfupa la munsana ndi nthiti

8Ndithudi Iye ali ndi mphamvu zomudzutsa

9Pa tsiku limene zinthu zobisika zidzayesedwa

10Ndipo adzakhala wopanda mphamvu kapena womuthandiza

11Pali mtambo umene umapereka mvula kawiri kawiri

12Ndi pali dziko lapansi limene limang’ambika

13Ndithudi! Awa ndi mawu amene amasiyanitsa

14Si nthabwala ayi

15Ndithudi iwo Al-A’la 649 ali kukonza chiwembu

16Ndipo Inenso ndili kukonza chiwembu

17Motero apatse nthawi anthu osakhulupirira. Ndipo chita nawo mwamtendere pa kanthawi kochepa

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath