84. Al-Inshiqaaq
1Pamene thambo lidzang’ambika
2Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
3Pamene nthaka idzatambasulidwa
4Ndi kutulutsa zonse zimene zinakwiriridwa m’kati mwake ndi kukhala yopanda kanthu
5Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
6oh iwe munthu! Ndithudi iwe uli kubwerera kupita kwa Ambuye wako ndi ntchito zako. Kubwerera kotsimikizidwa. Motero udzakumana nazo
7Koma Iye amene adzapatsidwa Buku lake m’dzanja lamanja
8Adzawerengedwa mosavuta
9Ndipo adzabwerera kwa anthu ake ndi chisangalalo
10Koma iye amene adzapatsidwa buku lake kumbuyo kwake
11Iye adzalira
12Ndipo akalowa ku moto walawi – lawi ku Gahena
13Ndithudi iye adali wansangala pakati pa anthu ake
14Ndithudi iye anali kuganiza kuti sadzabwerera kwa Mulungu
15Inde! Ndithudi Ambuye wake anali kuona zonse zimene iye ankachita
16Ine ndilumbira pali kufiira kwa kulowa kwa dzuwa
17Ndi pali usiku ndi zonse zimene umabweretsa mu mdima
18Ndi pali mwezi pamene ufika pa chimake penipeni
19Ndipo inu, ndithudi, mudzayenda kupita kutsogolo, kuchoka apa ndi kufika apo
20Kodi ndi chifukwa chiyani choti iwo alibe chikhulupiriro
21Ndipo pamene Korani ili kuwerengedwa kwa iwo sagwa pansi. Al-Buruj
22Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amalikana
23Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zimene amasonkhanitsa
24Choncho auze iwo za chilango chowawa
25Kupatula okhawo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, chifukwa iwo ali ndi malipiro opanda malire
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath