Chisilamu
kubwerera

83. Al-Mutaffifin

1Tsoka kwa iwo onse amene amagulitsa malonda awo monyenga

2Iwo amene amati ena akamawayesera zinthu amafuna kuti zikwanire muyeso wake

3Koma pamene iwo ayesa kapena awayesera anthu ena amawanyenga

4Kodi iwo saganiza kuti adzaukitsidwa kwa akufa

5Patsiku lalikulu

6Tsiku limene anthu a mitundu yonse adzaima pamaso pa Ambuye wa zolengedwa zonse

7Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu onse oipa chili mu Sijjin

8Kodi udzadziwa bwanji Sijjin ndi chiyani

9Ili ndi Buku lolembedwa

10Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

11Iwo amene amakana kuti kuli tsiku lachiweruzo

12Palibe wina amene amalikana tsikuli kupatula munthu wogona m’machimo

13Pamene chivumbulutso chathu chinenedwa kwa iye, iye amati: “Izi ndizo nthano za anthu akale.”

14Iyayi! Koma m’mitima mwawo ndi mokutidwa ndi zintchito zimene amachita

15Iyayi! Ndithudi iwo sadzaloledwa kuona Ambuye wawo pa tsikuli

16Ndipo iwo adzalowa ndi kulawa moto ku Gahena

17Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti: “Chimenechi ndicho chilango chija munkachinena kuti sichidzakhalako.”

18Iyayi! Ndithudi chiwerengero cha anthu olungama chimasungidwa mu Illiyyun

19Kodi mudzadziwa bwanji kuti Illiyin wapamwambayo ndi chiyani

20Ndi Al Mutaffifin 645 Buku lochita kulembedwa

21Limene limaonedwa ndi iwo okhawo amene ali kufupi ndi zofuna za Mulungu

22Ndithudi anthu onse olungama adzakhala ku malo a mtendere

23Atakhala pa mipando ya wofowofo ndipo ali kuyang’ana uku ndi uku

24Ndipo udzaona chisangalalo pa nkhope zawo

25Iwo adzapatsidwa kuti amwe vinyo weniweni amene sanatsegulidwepo

26Womaliza wake adzakhala ndi fungo labwino ndipo pachifukwa cha ichi, aleke onse amene afuna kulimbikira kuti alimbike

27Wosakanizidwa ndi madzi a Tasnim

28Kasupe amene anthu odala adzakhala ali kumwa

29Ndithudi! Anthu amene amachita zoipa, anali kuwaseka anthu amene anakhulupirira

30Ndi kumacheulana iwo akamadutsa pakati pawo

31Ndipo iwo amati akabwerera kwa anthu awo amabwera ali kunyoza

32Ndipo amati akawaona iwo amati: “Ndithudi awa ndiwo anthu osochera.”

33Pamene iwo sadalamulidwe kuti akhale owayang’anira

34Koma pa tsikuli anthu okhulupirira adzaseka anthu osakhulupirira

35Ali pa mipando yawofowofo ndi kumayang’ana

36Kodi anthu osakhulupirira, sanalipidwe mphotho yawo molingana ndi ntchito zawo

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath