82. Al-Infitaar
1Pamene thambo lidzang’ambika
2Pamene nyenyezi zidzagwa ndi kubalalitsidwa
3Ndi pamene nyanja zikuluzikulu zidzaphulika
4Pamene manda adzatseguka
5Pamenepo Mzimu uliwonse udzadziwa chimene udatumiza ndi chimene udasiya m’mbuyo
6oh Iwe munthu! Kodi ndi chiyani chikukunamiza kuti usiye kutsatira malamulo a Ambuye wako Wolemekezeka
7Amene adakulenga iwe ndi kukukonza kuti uzioneka bwino monga mmene uonekeramu
8Ndi nkhope ina iliyonse imene idamukondweretsa anakulenga iwe
9Iyayi! Koma inu mukukana kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo
10Koma pakati panu pali ena amene ali kukuyang’anirani
11Olemekezeka ndi odziwa kulemba
12Iwo amadziwa chilichonse chimene mumachita
13Ndithudi anthu onse angwiro adzakhala mu mtendere
14Ndipo, ndithudi, anthu onse oipa adzakhala ku Gahena
15Imene iwo adzalowako ndi kulawa malawi ake patsiku lachiweruzo
16Iwo sadzatha kuthawa ayi
17Kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo
18Tinenanso kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo
19Ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzatha kuthandiza wina aliyense ndipo Mulungu yekha ndiye amene adzaweruza
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath