Chisilamu
kubwerera

81. At-Takwir

1Pamene dzuwa lidzavundikiridwa

2Ndi pamene nyenyezi zidzagwa pansi

3Ndi pamene mapiri adzachotsedwa

4Ndi pamene ngamila zabele zizakhala zosasamalidwa

5Ndi nyama za m’tchire zidzasonkhanitsidwa pamodzi

6Ndi pamene nyanja zidzayatsidwa moto kapena zidzasefukira

7Ndi pamene mizimu idzakumanitsidwa ndi matupi awo

8Ndi pamene mwana wa mkazi wa mng’ono, amene adaundilidwa wa moyo adzafunsidwa

9Chifukwa chimene anamuphera

10Ndi pamene mabuku olembamo ntchito za munthu aliyense adzatulutsidwa

11Ndi pamene kumwamba kudzafafanizidwa ndi kuchotsedwa ku malo ake

12Ndi pamene Gahena idzatenthetsedwa kwambiri

13Ndi pamene Paradiso idzafikitsidwa pafupi

14Ndithudi munthu aliyense adzadziwa chimene adachita

15Motero, ndithudi, Ine ndili kulumbira pali nyenyezi zimene zimalowa

16Ndi pali maiko zimene zimayenda mofulumira ndi kudzibisa okha

17Ndi pali usiku pamene uchoka

18Ndipalim’mawapamenekulikucha

19Ndithudi awa ndi Mau a Mtumwi wolemekezeka

20Mwini mphamvu amene amalemekezedwa ndi Ambuye, Mwini Mpando wa Chifumu

21Amamveredwa ndi wokhulupirika

22Ndipo m’bale wanu uyu si wa misala ayi

23Ndipo, ndithudi, iye adamuona iye mu mlengalenga

24Iye sabisa zinthu zosaoneka

25Ndipo zimene alankhula sizochokera kwa Satana wotembereredwa

26Kodi inu muli kupita kuti

27Ndithudi ichi si china chilichonse ayi koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse

28Kwa aliyense wa inu amene afuna kuyenda moongoka

29Koma inu simungathe kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath