Chisilamu
kubwerera

80. Abasa

1Iye anachita matsinya ndi kuyang’ana kumbali

2Chifukwa munthu wakhungu anadza kwa iye

3Ndipo iwe ungadziwe bwanji kuti mwina angadziyeretse

4Kapena iye adzalandira chenjezo ndipo chenjezo likanamupindulira kanthu kena

5Koma iye amene amadziyesa kuti sasowa kanthu

6Ameneyo ndiye amene uli naye ndi chidwi

7Kodi uli nazo chiani ngati iye sadziyeretsa

8Koma kwa iye amene amakuthamangira

9Ndipo iye amaopa

10Iwe siudamulabadire ayi

11Iyayi! Ndithudi chimenechi ndi chikumbutso

12Muloleni aliyense amene afuna kuti achilabadire

13Ichi chidalembedwa m’Buku la Mulungu lolemekezeka

14Loyeretsedwa ndi losungidwa bwino ndi loyera

15M’manja mwa Alembi

16Wolemekezeka ndipo womvera

17Atembereredwe munthu! Kodi ndi chiani chili kumuletsa kuthokoza

18Kodi Iye adamulenga kuchokera ku chiyani

19Kuchokera ku dontho la umuna, Iye adamulenga ndipo adamukonza bwino

20Ndipo Iye adamukonzera iye njira yapafupi

21Ndipo amamupha ndi kumusunga m’manda

22Ndithudi Iye adzamudzutsa monga momwe afunira

23Iyayi, koma munthu sanachite zimene Iye adamulamulira

24Mulekeni munthu kuti aganize za chakudya chake

25Kuti Ife timagwetsa mvula yambiri

26Ndipo timaphwanya nthaka

27Ndipo Ife Al-Takwir 641 timameretsa njere

28Mphesa ndi Msipu

29Mitengo ya mafuta, ndi mitengo ya tende

30Ndi minda imene ili ndi mitengo yambiri

31Ndi mitengo ya zipatso ndi msipu

32Chakudya cha inu ndi ziweto zanu

33Koma pamene kulira kogonthetsa mkhutu kudzamveka

34Patsiku limene munthu adzakana m’bale wake

35Amai ake ndi bambo ake

36Mkazi wake ndi ana ake

37Chifukwa aliyense patsiku limeneli, adzakhala otangwanika ndi mavuto ake

38Patsiku limeneli padzakhala nkhope zambiri zowala

39Zosekerera ndi zachimwemwe chifukwa cha nkhani yabwino

40Ndipo pa tsikuli padzakhala nkhope zina zokutidwa ndi fumbi

41M’dima udzakuta iwo

42Awa adzakhala anthu osakhulupirira ndi ochita zoipa

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath