Chisilamu
kubwerera

79. An-Naazi'aat

1Pali iwo amene amalanda mwankhanza

2Ndi pali iwo amene amachotsa mwaufulu

3Ndi pali iwo amene amauluka

4Ndi pali iwo amene amathamanga ngati ali pa liwiro loopsya

5Ndi pali angelo amene amakwaniritsa kuchita malamulo a Ambuye wawo

6Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri

7Ndi kulira kwa lipenga kawiri

8Mitima, patsiku limeneli, idzafumuka ndi kuda nkhawa

9Maso awo atagwetsa pansi

10Iwo amanena kuti: “Kodi ife tidzabwerera monga momwe tinali poyamba?”

11“Angakhale mafupa athu ataola?”

12Iwo amati: “Kubwerera kotero ndi kopanda phindu.”

13Koma udzakhala mfuwu umodzi okha

14Pamene, taona, iwo adzadzipeza okha ali pamwamba pa nthaka ali ndi moyo

15Kodiinumudaimvankhaniya Mose

16PameneAmbuye wake adamuitana mu dambo lodalitsika la Tuwa

17“Pita kwa Farao; Ndithudi iye waphwanya malamulo mopyola muyezo.”

18“Ndipo ukamuuze kuti: Kodi ungadziyeretse wekha?”

19“Ndi kuti ine ndikulondolere kwa Ambuye wako kuti uzimuopa Iye?”

20Kotero iye adamuonetsa chizindikiro cha chikulu

21Koma iye adachikana ndipo sanamvere

22Iye adapitirizabe kuchita zoipa

23Ndipo iye adaitana anthu ake onse ndipo anafuula mokweza

24Nati: “Ine ndine Ambuye wanu wapamwamba mwamba.” Al-Naziat

25Motero Mulungu adamugwetsera iye chilango chifukwa cha mau ake omaliza ndi oyamba

26Ndithudi mu izi muli phunziro lomveka kwa anthu oopa Mulungu

27Kodi inu ndinu ovuta kulenga kapena thambo la mlengalenga limene Mulungu adalilenga

28Iye analikweza m’mwamba ndi kulikonza bwino

29Usiku wake amaukuta ndi m’dima ndipo masana ake amatulutsa kuwala

30Ndipo pambuyo pake adalikulitsa dziko

31Ndipo anatulutsa madzi ndi msipu

32Ndipo adazika mapiri molimbika

33Chakudya cha phindu kwa inu ndi kwa zoweta zanu

34Koma pamene mavuto akulu akudza

35Tsiku limene munthu adzayamba kuganiza ntchito zake zonse

36Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi kuti aliyense aione

37Ndipo kwa iye ophwanya malamulo

38Ndipo anasankha moyo wapadziko lino

39Ndithudi malo ake okhala ndi ku Gahena

40Koma kwa iwo amene amaopa kukaima pamaso pa Ambuye wake ndi machimo ndipo anali kudziletsa kuchita chifuniro chopanda pake

41Ndithudi adzakhala ku Paradiso

42Amakufunsa za nthawi imene chigumula chidzabwere

43Iwe siudziwa zoti unene china chili chonse

44Ndi Ambuye wako yekha amene amadziwa tsiku

45Iwe ndiwe mchenjezi chabe kwa iwo amene ali kuliopa tsikuli

46Patsiku limene iwo adzachiona chigumula, kudzakhala ngati kuti iwo sanakhale padziko lapansi nthawi yaitali koma usiku umodzi kapena usana wokha

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath