Chisilamu
kubwerera

77. Al-Mursalaat

1Pali mphepo imene imatsatana pafupipafupi

2Pali mphepo ya mkuntho

3Pali mphepo imene imamwaza mitambo ndi mvula

4Pali mavesi amene amasiyanitsa chabwino

5Pali angelo amene amabweretsa chivumbulutso kwa Atumwi

6Kuthetsa kukangana kapena kuwachenjeza

7Ndithudi zonse zimene mwalonjezedwa zidzachitika

8Pamene nyenyezi zidetsedwa

9Ndi pamene thambo la kumwamba ling’ambika pakati

10Ndi pamene mapiri aphwanyika kukhala fumbi

11Ndi pamene Atumwi onse asonkhanitsidwa kukhala pamalo amodzi

12Kodi ndi tsiku liti limene izi zidzachitike

13Lidzakhala tsiku la chiweruzo

14Kodi ndi chiyani chidzakudziwitse zatsiku la chiweruzo

15Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira

16Kodi Ife sitinaononge anthu a makedzana

17Kotero tidzaipanga mibadwo yotsatira kuti ione zomwezo

18Mmenemu ndi mmene timakhaulitsira anthu ochita zoipa

19Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

20Kodi sitidakulengeni inu kuchokera ku madzi onyozeka

21Amene tidasunga pamalo okhazikika

22Mpaka nthawi yake itakwana

23Motero Ife tinayesa ndipo Ife wodziwa kuyesa

24Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

25Kodi Ife sitinapange nthaka ngati malo okumaniranamo

26Amoyo ndi akufa

27Ndipo tidalenga Al Mursalat 635 mapiri atali pa dziko ndi kukupatsani madzi okoma kuti muzimwa

28Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

29(Zidzanenedwa kuti): “Pitani ku chilango chimene munkati sichidzabwera!”

30Pitani inu mu chithunzi, mu magulu atatu

31Opanda mthunzi kapena pokhala pokutetezani ku malawi a moto

32Ndithudi! Umatulutsa malawi ake akulu akulu ngati nyumba zachifumu

33Ndipo ooneka ngati ngamira ya chikasu

34Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira

35Patsiku limeneli iwo sadzatha kulankhula

36Ndipo sadzaloledwa kuti apereke chidandaulo

37Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira

38Limeneli ndilo tsiku la chiweruzo. Ife takusonkhanitsani nonse pamodzi ndi anthu a makedzana

39Tsopano ngati inu muli ndi chiwembu, chitani chiwembu chanu kwa Ine

40Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira

41Ndithudi anthu angwiro adzakhala mu mthunzi wozizira ndi pa akasupe

42Ndi zipatso zimene afuna kukhosi kwawo

43Idyani ndipo imwani mosangalala chifukwa cha zimene mudachita

44Ndithudi, mmenemo ndi mmene timalipirira anthu angwiro

45Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

46Idyani ndipo musangalale kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu oipa kwambiri

47Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

48Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Weramani.” Iwo amakana kutero

49Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira

50Kodi ndi Uthenga uti woposa uwu umene adzaukhulupirire

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath