Chisilamu
kubwerera

76. Al-Insaan

1Kodi sipadali nthawi imene munthu sanali kanthu kena kali konse kodziwika

2Ndithudi Ife tidamulenga munthu kuchokera ku madontho a umuna umene unasakanizidwa ndi ukazi ndi cholinga chomuyesa motero Ife tidamupanga iye kukhala wakumva ndi woona

3Ndithudi Ife tamulangiza njira yabwino kaya iye akhala wothokoza kapena wosathokoza

4Ndithudi tawakonzera anthu osakhulupirira unyolo ndi magoli ndi moto wa lawilawi

5Ndithudi anthu onse angwiro adzamwa chakumwa chosakanizidwa ndi madzi ochokera pa kasupe wa ku Paradiso chotchedwa Kafur

6Kasupe amene akapolo a Mulungu adzamwapo, amene amatumphutsa madzi ochuluka

7Iwo amene amakwaniritsa malonjezo awo ndipo amakhala ndi mantha ndi tsiku limene zoipa zidzasefukira ponseponse

8Ndipo amapereka chakudya chifukwa cha chikondi cha Mulungu, kwa anthu aumphawi, amasiye ndi kwa akaidi

9Ife tili kukudyetsani chifukwa cha Mulungu basi. Ife sitifuna malipiro kapena mayamiko kuchokera kwa inu

10Ndithudi ife tiopa tsiku loopsa ndi laululu limene lidzasanduliza nkhope kuoneka monyasa, limene lili nkudza kuchokera kwa Ambuye wathu

11Motero Mulungu awapulumutsa iwo ku zoipa za tsiku limeneli ndi kuwapatsa nyali yokongola kuti akhale mosavutika ndi mwachisangalalo

12Ndipo mphotho yawo idzakhala munda wa Paradiso ndi zovala za silika chifukwa chopirira kwawo

13Ali kukhala m’Paradiso, pamipando yawofowofo, iwo sadzamva kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira kwambiri

14Ndipo mithunzi idzakhala pafupi ndi iwo ndipo zipatso zidzalendewera mu matsanzi kuti asamavutike pothyola

15Ndipo pakati pawo padzaperekedwa zikho zozungulira za siliva ndi matambula a magalasi

16Matambula oonetsa zinthu zomwe zili m’kati mwake, opangidwa kuchokera ku siliva. Iwo adzathiramo chakumwa molingana ndi chilakolako chawo

17Ndipo iwo adzapatsidwa chakumwa kuchokera mu zikho zodzala ndi madzi osakaniza ndi Zanjabil

18Kasupe amene ali komweko wotchedwa Salsabil

19Ndipo adzazunguliridwa ndi ana owatumikira a misinkhu yofanana. Ndipo ngati iwe utawaona ukhoza kuganiza kuti ndi ndolo zomwazikamwazika

20Ndipo pamene iwe uona kumeneko, udzaona madalitso ndi ufumu waukulu

21Iwo adzavala nsalu zokongola za silika zooneka ngati msipu zopetedwa ndi golide. Iwo adzavala zibangiri za siliva ndipo Ambuye wawo adzawapatsa chakumwa chabwino

22Ndithudi iyi ndi mphotho yanu ndipo kupirira kwanu kwalandiridwa

23Ndithudi ndife amene tavumbulutsa kwa iwe pang’ono pang’ono, Buku lolemekezeka la Korani

24Motero pirira ndipo tsatira malamulo a Ambuye wako ndipo usamvere zonena za munthu wochimwa kapena wosakhulupirira amene ali pakati pawo

25Ndipo uzilemekeza dzina la Ambuye wako m’mawa ndi madzulo

26Ndi m’gawo lina la usiku, uzimupembedza Iye ndipo uzimulemekeza Iye usiku wonse

27Ndithudi! Awa amakonda kwambiri moyo wa msanga msanga wa masiku ano, ndipo amaiwala tsiku limenelidzakhalalovuta

28Ndifeamenetidawalengandipo tinaika mphamvu m’ziwalo zawo. Koma ngati Ife titafuna, tikhoza kulenga anthu ena kuti alowe m’malo mwawo

29Ndithudi! Ili ndi chenjezo motero aliyense amene afuna, mulekeni kuti atsatire njira yoyenera yopita kwa Ambuye wake

30Koma inu simudzatha kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu. Ndithudi Mulungu ndiye Mwini kudziwa ndi Mwini nzeru

31Iye adzaonetsa chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma anthu ochimwa, Iye wawakonzera iwo chilango chowawa

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath