Chisilamu
kubwerera

74. Al-Muddaththir

1ohiweamenewakutidwa

2Dzukandikuperekachenjezo

3Ndipo lemekeza Ambuye wako

4Ndipo yeretsa zovala zako

5Ndipo pewa zonse za mafano

6Ndipo usapereke thandizo ndi cholinga chopezamo cholowa

7Ndipo khala wopirira chifukwa cha Ambuye wako

8Ndipo pamene lipenga lidzalira

9Ndithudi limeneli lidzakhala tsiku loopsa

10Tsiku lamavuto kwa anthu onse osakhulupirira

11Ndisiye ndekha kuthana ndi munthu amene ndidamulenga ndekha

12Ndipo ndidamupatsa chuma chosawerengeka

13Ndi ana okhala pambali pake

14Ndipo Ine ndidamuchitira zonse kuti zikhale zolongosoka ndi zapafupi

15Koma nthawi zonse amafuna kuti ndizimupatsabe zinthu zambiri

16Kosatheka! Ndithudi iye wakhala ali kuchitira mwano chivumbulutso chathu

17Ine ndidzamukhaulitsa pomupatsa chilango chowawa

18Ndithudi iye adaganiza ndipo adakonza chiwembu

19Ndipo ayenera kutembererewa chifukwa cha chiwembu chake

20Motero iye ayenera kutembereredwa chifukwa cha chiwembu chake

21Ndipo iye anayang’ana

22Ndipo iye adachita matsinya ndipo anaonetsa kuipidwa

23Kenaka adatembenukira kumbali modzikweza

24Ndipo iye adati: “Ichi sichina koma matsenga a anthu a amakedzana!”

25“Ichi sichina koma mawu a munthu chabe.”

26Ine ndidzamuponya iye ku Gahena

27Kodi chidzakudziwitsa kuti moto wa ku Gahena ndi chiani

28Iwo susunga kapena kusiya

29Umatentha matupi

30Umasamalidwandiangelokhumindiasanundianayi

31Ife sitidasankhe wina aliyense koma angelo kuti aziyang’anira moto ndipo tinakhazikitsa chiwerengero chawo ngati mayesero kwa anthu osakhulupirira, kuti iwo onse amene alandira mawu a Mulungu akhulupirire ndi kuti anthu okhulupirira m’choonadi apitirize chikhulupiriro chawo; kuti iwo amene adalandira kale mawu a Mulungu ndiponso anthu onse okhulupirira moona asakhale ndi chikaiko china chilichonse; ndipo kuti onse amene m’mitima mwawo muli matenda pamodzi ndi anthu osakhulupirira anganene kuti: “Kodi Mulungu afuna kutanthauza chiyani pa chitsanzo chotere?” Mmenemo ndi mmene Mulungu amasokeretsera munthu aliyense amene Iye wamufuna ndi kutsogolera aliyense amene Iye wamufuna. Palibe munthu amene amadziwa asirikali a Ambuye wako kupatula Iye mwini. Ichi si china chilichonse koma chikumbutso kwa anthu onse

32Iyayi, ndilumbira pali mwezi

33Ndi pali usiku pamene uli n’kutha

34Ndi pali m’mbandakucha pamene uli n’kudza

35Ndithudi ili ndi limodzi la masoka akuluakulu

36Ndi chenjezo kwa anthu onse

37Kwa yense wa inu amene afuna kupitirirabe mtsogolo kapena afuna kutsalira m’mbuyo

38Munthu aliyense adzafunsidwa molingana ndi ntchito zake

39Kupatula iwo amene adzakhala kudzanja lamanja

40M’minda, iwo azidzafunsana wina ndi mnzake. Qiyamah

41Za anthu ochimwa kuti

42Kodi ndi chiyani chimene chakulowetsani inu ku moto

43Iwo adzayankha nati: “Ife sitimapemphera.”

44Ndiponso sitimadyetsa anthu a njala

45Ife timangotsutsa zinthu mwaumbuli

46Ndipo tidali kunena kuti kulibe tsiku lachiweruzo

47Mpaka pamene imfa idatipeza

48Motero palibe chidandaulo chochokera kwa wina aliyense chimene chidzamveka

49Kodindichifukwachiyaniiwoalikuthawachikumbutso ichi

50Monga abulu odzidzimutsidwa

51omwe anali kuthawa Mlenje, Mkango kapena nyama ina yoopsya

52Iai! Aliyense wa iwo afuna kuti apatsidwe masamba a Buku otambasula

53Ndikosatheka! Koma iwo alibe mantha ndi zimene zili nkudza

54Iyayi. Ndithudi ili ndi chenjezo

55Motero musiyeni amene afuna kuti awerenge ndi kulandira chenjezo

56Ndipo iwo sadzalandira chenjezo pokha pokha ngati Mulungu afuna. Iye ndiye Ambuye wofunika kuti anthu onse azichita mantha ndi Iye, ndipo Iye ndi Ambuye wokhululukira

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath