73. Al-Muzzammil
1Oh iwe amene wadzikulunga m’chovala
2Dzuka usiku onse kupatula kwanthawi kochepa
3Theka la usikuwo kapena kanthawi kocheperako
4Kapena kwa kanthawi kochulukirapo ndipo lakatula Korani modekha ndi modukizadukiza monga mmene umayenera kuchitikira
5Ndithudi, Ife tidzakutumizira Mawu a mphamvu
6Ndithudi kuuka nthawi ya usiku ndi kovuta, ndipo mau amatchulidwa bwino
7Ndithudi, iwe masana umatangwanika kwambiri
8Ndipo uzikumbukira dzina la Ambuye wako ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye
9Iye ndiye Ambuye wa kum’mawa ndi wa kumadzulo. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mulandire Iye kuti akhale Mtetezi wako
10Pirira pa zonse zimene ali kunena ndipo siyana nawo mwaulemu
11Undisiyire Ine onse amene amakana choonadi nthawi zonse ndipo pirira ndi iwo pakanthawi kochepa
12Ife, ndithudi, tili ndi unyolo ndipo tawasungira moto wosatha kuuzima
13Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa
14Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri ndipo mapiri adzakhala mulu wa mchenga wotaika umene umatuluka kupansi
15Ndithudi Ife tatumiza Mtumwi kukhala umboni wokutsutsani monga momwe tidatumizira Mtumwi kwa Farao
16Koma Farao sadamumvere Mtumwi ndipo Ife tidamulanga ndi chilango choopsa
17Kodi ngati inu simukhulupirira, mudzalithawa bwanji tsiku limene lidzachititsa ana anu a ang’ono kukhala ndi imvi
18Tsiku limene thambo la kumwamba lidzang’ambika pakati. Ndithudi lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa
19Ndithudi ili ndi chenjezo chabe, motero musiyeni aliyense amene afuna kuti atsatire njira yoyenera yonka kwa Ambuye wake kuti aitsatire
20NdithudiAmbuye wako amadziwa kuti nthawi zina iwe umakhala tcheru mphindi ziwiri pakati pa mphindi zitatu za usiku, mwina theka la usiku ndipo nthawi zina mphindi imodzi pakati pa mphindi zitatu za usiku, monga momwe gulu lina la anthu amene ali nawe. Ndipo Mulungu ndiye amene amasiyanitsa usiku ndi usana. Iye amadziwa kuti siungathe kupemphera mphindi zonse ndipo wakuyang’ana mwachisoni. Kotero lakatula magawo ena a Korani amene angakhale apafupi kwa iwe. Iye amadziwa kuti pakati panu pali anthu odwala ndi ena amene ali kupita uku ndi uku padziko kufunafuna zokoma za Mulungu ndi ena amene ali kumenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Motero lakatula, mawu a m’Korani, amene ungathe kulakatula, ndipo pitiriza kupemphera ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo kongoza ngongole yabwino kwa Mulungu ndipo chabwino chilichonse chimene muli kutsogoza, mudzachipeza kwa Mulungu, chitasungidwa bwino ndipo mudzalandira mphotho ya mtengo wapatali kuchokera kwa Iye. Ndipo pempha chikhululukiro kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath