72. Al-Jinn
1Nena: “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la majini lidamvera chivumbulutso cha Mulungu ndipo lidati: Ndithudi ife tamva mawu odabwitsa.”
2“Amene apereka dongosolo la kunjira yoyenera ndipo ife takhulupirira zonse zimene zinali kunenedwa ndipo ife sitidzalambira wina aliyense kupatula Ambuye wathu.”
3‘Ulemerero ukhale kwa Ambuye wathu. Iye sadakwatire kapena kubereka ana
4‘Ndipo kuti anthu opusa amene ali pakati pathu akhala ali kumanenera Mulungu zinthu zonyasa kwambiri
5‘Ndipo, ndithudi, ife timaganiza kuti kulibe munthu kapena majini amene angakanene chinthu chabodza chokhudza Mulungu
6‘Ndipo, ndithudi, padali anthu pakati pa mtundu wa anthu amene amapeza chitetezo kuchokera kwa anthu a mtundu wa majinn. Koma iwo adangoonjezera kuchita zoipa ndi kusakhulupilira
7‘Ndipo iwo adayamba kuganiza monga momwe inu mumaganizira, kuti Mulungu sadzadzutsa wina aliyense
8‘Ndipo ife tidafuna kupita kuthambo la pamwamba zedi ndipo tidaona kuti linali lodzadzidwa ndi ogwira ntchito a mphamvu ndi nyenyezi za moto
9‘Ndithudi ife tinali Al Jinn 623 kukhala m’menemo kumvetsera koma amene azimvetsera tsopano, adzapeza malawi a moto uli kumudikira
10‘Ife sitidziwa ngati akuwafunira mavuto anthu awo amene ali padziko lapansi kapena kuti Ambuye wawo ali ndi cholinga choti awatsogolere
11‘Alipo ena pakati pathu amene ndi angwiro pamene ena ndi ochimwa. Ife ndife magulu otsatira njira zosiyanasiyana
12‘Ndipo ife timaganiza kuti sitingathawe Mulungu padziko lapansi ndiponso sitingathawe pothamangitsidwa
13‘Ndipo, ndithudi, pamene tidamva ulangizi wake, ife tidakhulupirira ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Ambuye wake sakhala ndi mantha otaya zake kapena kuponderezedwa
14‘Ndipo pakati pathu pali ena amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndi ena amene amachita zoipa. Iwo amene adzipereka kwa Mulungu amatsatira njira yoyenera.”
15Ndipo iwo amene amachita zoipa adzakhala nkhuni za ku Gahena
16Ngati iwo akanakhulupirira ndi kutsatira njira yoyenera, Ife, ndithudi, tikadawapatsa mvula yambiri
17Kuti tikhoza kuwayesa ndi izo. Ndi aliyense amene samvera chenjezo la Ambuye wake. Iye adzakonza kuti alandire chilango chowawa zedi
18Ndipo Mizikiti ndi ya Mulungu yekha. Motero musapembedze mulungu wina pambali pa Mulungu m’modzi yekha
19Ndipo pamene kapolo wa Mulungu anaima kupempha kwa Iye, iwo adamuzungulira mu unyinji wawo mopanikizana
20Nena: “Ine ndimapempha kwa Ambuye wanga ndipo sindimufanizira Iye ndi wina aliyense.”
21Nena: “Ine ndilibe mphamvu yobweretsa pa inu chinthu choipa kapena kukubweretsani ku njira yoyenera.”
22Nena: “Palibe wina aliyense amene anganditeteze ine kwa Mulungu ndipo ine sindingapeze kothawira kwina kulikonse kupatula kwa Iye yekha.”
23“Udindo wanga ndi kukuuzani choonadi chimene ndalandira kuchokera kwa Mulungu ndi Uthenga wake, ndipo aliyense amene amanyoza Mulungu ndi Mtumwi wake adzakhala ku moto wa ku Gahena nthawi zonse.”
24Mpaka pamene iwo ataona kuopsa kwa chilango chimene chidalonjezedwa kuti chidzafika pa iwo, pamenepo ndipo pamene adzadziwa mbali imene wopanda mphamvu ali ndipo kuti ndi ayani amene anali wochepa m’chiwerengero
25Nena: “Ine sindidziwa ngati chimene mwalonjezedwa chidzafika msanga kapena kuti Ambuye wangaadachiikapatali.”
26Iyeyekhandiyeameneamadziwa zonse zobisika ndipo zinsinsi zake saululira wina aliyense ayi
27Kupatula kwa Atumwi ake amene Iye amawasankha yekha. Ndipo Iye amatumiza gulu la Atetezi amene amayenda patsogolo ndi pambuyo pawo
28Amawateteza mpaka pamene aona kuti iwo apereka uthenga wochokera kwa Ambuye wawo. Ndipo Iye amadziwa chili chonse chimene ali nacho ndipo Iye amasunga chiwerengero cha chinthu chili chonse
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath