71. Ayi
1Ndithudi tidatumiza Nowa kwa anthu ake: “Chenjeza anthu ako chilango chowawa chisadafike pa iwo.”
2Iye adati: “oh inu anthu anga! Ndithudi ine, ndine Mchenjezi wooneka kwa inu.”
3“Kuti muzipembedza Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo mundimvere ine.”
4“Iye adzakukhululukirani machimo anu ndi kukusungani bwino mpaka nthawi ya imfa yanu. Ndithudi nthawi ya Mulungu ikakwana, palibe wina aliyense amene angaibwezere m’mbuyo inu mukadadziwa.”
5Iye adati: “oh Ambuye! Ndithudi usana ndi usiku ndakhala ndiri kuwaitana anthu anga.”
6“Koma kuitana kwanga kwangoonjezera kusamvera kwawo.”
7“Ndipo, ndithudi, nthawi yonse imene ndiitana kuti Inu muwakhululukire, iwo amatenga zala zawo ndi kutseka m’makutu mwawo ndipo amatenga mikhanjo yawo ndi kufunditsa kumutu kwawo ndipo amapitirirabe kuchita zoipa monyada.”
8“Ndipo, ndithudi, ine ndidalalikira mokweza kwa iwo.”
9“Ndipo, ndithudi, ndidawalankhula pagulu ndi mwamseri.”
10Ndidawauza: “Funsani chikhululukiro cha Ambuye wanu. Ndithudi Iye amakhululukira nthawi zonse.”
11“Iye adzakutumizirani Nuh 621 mvula yochuluka.”
12“Ndikukupatsani inu chuma, ana, minda ndi mitsinje.”
13Kodi mwatani, inu simuyembekeza mphotho
14Pamene Iye adakulengani inu m’nthawi zosiyana siyana
15Kodi inu simuona mmene Mulungu adalengera miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake
16Ndipo anapanga mwezi ngati muuni ndi dzuwa ngati nyali
17Mulungu adakulengani inu kuchokera ku nthaka
18Ndipo ku nthaka komweko adzakubwezerani inu ndi kukudzutsaninso
19Ndipo Mulungu adalenga dziko kukhala lalikulu kwa inu
20Kuti muziyenda m’njira zambiri za zikuluzikulu
21Nowa adati: “oh Ambuye! Anthu anga sali kundimvera ine koma mmalo mwake ali kutsatira amene sangawaonjezere chuma ndi ana koma mavuto.”
22Ndipo iwo akonza chiwembu champhamvu
23Ndipo ati: “Mwanjira ina iliyonse inu musaleke kupembedza milungu yanu. Musaleke kupembedza Wadd, Suwa, Yaghuth, Yauq kapena Nasr.”
24“Ndipo, ndithudi, iwo asocheza anthu ambiri. Ndipo Inu musaonjeze china chili chonse kwa anthu ochita zoipa chifukwa apitirizabe kuchita zoipa.”
25Chifukwa cha machimo awo iwo anamizidwa ndipo adaponyedwa ku moto ndipo iwo sanapeze wina aliyense kuti awathandize, m’malo mwa Mulungu
26Ndipo Nowa adati: Ambuye wanga! Musasiye munthu aliyense padziko lapansi mwa anthu osakhulupirira
27“Ngati Inu muwasiya iwo adzasocheretsa akapolo anu okhulupirira ndipo iwo adzabereka anthu ochita zoipa ndi osakhulupirira.”
28“Ambuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi iye amene alowa mnyumba yanga ngati wokhulupirira ndiponso okhulupirira onse amuna ndi akazi. Ndipo kwa anthu osakhulupilira, Inu musawaonjezere china koma chionongeko
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath