70. Al-Ma'aarij
1Wofunsa adafunsa za chilango chimene chichitike
2Pa anthu onse osakhulupirira, chimene wina sangachiletse
3Kuchokera kwa Ambuye, Mwini njira zokwerera kumwamba
4Angelo ndi Mzimu amakwera kupita kwa Iye mtsiku limodzi limene lingafanizidwe ndi zaka zikwi makumi asanu
5Kotero pirira kupilira kwabwino
6Ndithudi! Iwo amaona kuti ili patali
7Koma Ife tili kuliona lili pafupi
8Tsiku limene kumwamba kudzaoneka ngati mkuwa wachiphalaphala
9Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya wouluka
10Ndipo palibe bwenzi amene adzafunse za bwenzi lake
11Iwo azidzawaona iwo. Munthu wochita zoipa adzafunitsitsa kuti mwina akhoza kudzipulumutsa ku chilango cha tsikuli popereka ana ake
12Ndi mkazi wake ndi m’bale wake
13Ndi anansi ake amene adamusunga
14Ndipo zonse zimene zili padziko lapansi kuti mwina zikhoza kumupulumutsa
15Kosatheka! Ndithudi udzakhala moto wa lawilawi wa ku Gahena
16wotentha mutu wonse
17Udzaitana aliyense amene amakana choonadi
18Ndipo amangopanga chuma ndi kuchisunga
19Ndithudi Munthu adalengedwa kukhala wosapirira
20Amakhala modandaula ngati mavuto amupeza
21Ndipo amachita mwano ngati apeza zabwino
22Kupatula okhawo amene amapemphera Al Ma’arij 619 nthawi zonse
23Iwo amene amapemphera mowirikiza
24Ndi iwo amene m’chuma chawo muli gawo limene amasiya padera
25Kuti apereke kwa anthu opempha ndi amene ali pa mavuto
26Ndi iwo amene amakhulupirira kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo
27Ndi iwo amene amachita mantha ndi chilango cha Ambuye wawo
28Ndithudi chilango cha Ambuye ndi chosatetezeka
29Ndi iwo amene amadzisunga
30Kupatula akazi awo ndi akapolo awo chifukwa iwo sadzadzudzulidwa
31Koma aliyense amene afuna kuposa awa, ndi wophwanya malamulo
32Ndi iwo amene amasunga malonjezo ndi malamulo awo
33Ndi iwo amene amapereka umboni woona nthawi zonse
34Ndi iwo amene amalabadira mapemphero awo
35Awa ndiwo amene adzalemekezeka m’minda ya Paradiso
36Kodi chachitika ndi chiyani kwa anthu osakhulupirira kuti azibwera mwaliwiro kudza kwa iwe
37Kuchokera kumbali ya dzanja lamanja ndi mbali yakumanzere mu unyinji wawo
38Kodi aliyense wa iwo amayembekeza kukalowa m’munda wa chisangalalo
39Kosatheka! Ndithudi Ife tawalenga kuchokera ku chinthu chimene sachidziwa
40Motero, Ine ndilumbira pa Ambuye wa malo onse a kum’mawa ndi kumadzulo kuti Ife tikhoza
41Kuika anthu ena abwino m’malo mwawo ndipo palibe chinthu chimene chingatiletse kutero
42Motero asiye ayambe adzinyenga ndi chisangalalo mpaka pamene adzakumana ndi tsiku lawo limene adalonjezedwa
43Tsiku limene adzatuluka mwansanga m’manda mwawo ngati anthu a pa mpikisano umene amalandirirapo mphotho
44Atayang’ana maso awo pansi ndipo adzachititsidwa manyazi. Limeneli ndilo tsiku limene analonjezedwa
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath