Chisilamu
kubwerera

69. Al-Haaqqa

1Choonadi chenicheni

2Kodi choonadi chenicheni ndi chiyani

3Kodi ndi chiyani chimene chingakupangitse kuti udziwe kuti choonadi chenicheni ndi chiti

4Mtundu wa Thamoud ndi Ad adakana ola la chionongeko

5Ndipo anthu a Thamoud adaonongeka ndi mfuwu woopsya

6Ndipo anthu a Aad adaonongeka ndi chimphepo cha mkuntho

7Chimene Mulungu adachilamulira kuti chikunthe pa iwo usiku usanu ndi uwiri ndi usana usanu ndi utatu mosalekeza. Moti iwe ukadawaona anthu atagonagona ukadayesa kuti ndi mitengo ya migwalangwa yakugwa

8Kodi uli kuona wina wa iwo opulumuka

9Ndipo Farao ndi anthu amene adalipo iye asadabadwe, ndi a mizinda imene idaonongeka anali kuchita zoipa

10Ndipo iwo sanamvere Mtumwi wochokera kwa Ambuye wawo ndipo Iye adawalanga ndi chilango chowawa zedi

11Ndithudi!Pamenemadzianasefukira,Ifetidakunyamulani inu m’chombo

12Kuti tikhoza kuchipanga icho kukhala chikumbutso ndi kuti khutu la kumva limve

13Ndipo pamene lipenga lidzaimbidwa kamodzi

14Ndipo nthaka ndi mapiri anyamulidwa pamodzi ndi kuponyedwa pansi mwamphamvu kamodzi

15Patsiku limeneli chinthu choopsa chidzachitika

16Ndipo thambo lidzaphwanyika ndipo lidzakhala lopanda mphamvu

17Ndipo Angelo adzaima mbali zonse ndipo angelo asanu ndi atatu pa tsikuli adzanyamula Mpando wa Chifumu wa Ambuye wako

18Patsiku limeneli mudzaweruzidwa ndipo palibe chinthu chachinsinsi chimene chidzabisika

19Ndipo yense amene adzapatsidwa Buku lake kudzanja lamanja adzati: “Ah taonani! Werengani Buku langa!”

20Ndithudi, ine ndidakhululupira kuti tsiku lina zochita zanga zidzaweruzidwa

21Kotero iye adzakhala ndi moyo wa chisangalalo

22M’munda wapamwamba

23Wa zipatso zokoma zimene zili pafupi

24Idyani ndipo imwani mmene mufunire chifukwa cha ntchito zanu zabwino zimene mudatumiza patsogolo panu m’masiku apitawo

25Koma iye amene adzapatsidwe buku lake m’dzanja lamanzere, adzati: “Kukadakhala bwino ngati Buku langa likadakhala losaperekedwa kwa ine.”

26“Ndipo sindikadziwa kuti zochita zanga zachuluka bwanji.”

27“Ikadakhala bwino imfa ikadangodza pa ine.”

28“Chuma changa sichidandithandize chilichonse.”

29“Ulamuliro wanga wonse wachoka kwa ine.”

30“Mugwireni ndipo mumumange.”

31“Ndipo m’ponyeni M’ng’anjo ya moto.”

32“Ndipo mumangeni ndi unyolo wotalika malipande makumi asanu ndi awiri.”

33Ndithudi, iye samakhulupirira mwa Mulungu wamkulu

34Ndipo sadali kuthandiza kudyetsa anthu osowa

35Motero lero iye sadzakhala ndi bwenzi aliyense

36Kapena chakudya china chilichonse kupatula zonyasa zochoka pa zilonda

37Palibe amene adzachidya kupatula ochimwa ndi osakhulupilira

38Motero Ine ndilumbira pali chilichonse chimene uli nkuona

39Ndi chimene chili chobisika

40Kuti ndithudi awa ndi mawu a Mtumwi wolemekezeka

41Ndipo si mawu a Mlakatuli ayi ndipo chikhulupiriro chanu ndi chochepa

42Ndipo si mawu a munthu wa maula ayi, ndipo ndi zochepa zimene inu mukumbukira

43Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse

44Ndipo iye akanapeka nkhani yokhudza Ife

45Ndithudi Ife tikadagwira dzanja lake lamanja

46Ndipo, ndithudi, Ifetikadadulamtsemphawakewamoyo

47Ndipo palibe, wina wa inu, amene akadatiletsa Ife kumugwira

48Ndipo, ndithudi, Korani iyi ndi chikumbutso kwa iwo amene amapewa zoipa

49Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa kuti alipo ena a inu amene amaikana

50Ndipo, ndithudi, ilo lidzakhala lomvetsa chisoni kwa anthu osakhulupirira

51Ndipo, ndithudi, ichi ndi choonadi chokhachokha

52Motero lemekeza dzina la Ambuye wako, Wamkulu kulu

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath