68. Al-Qalam
1Nun. Pali cholembera ndi zimene amalemba
2Mwachisomo cha Ambuye wako, sindiwe wamisala ayi
3Ndithudi iwe udzalandira mphotho yosatha
4Ndithudi iwe uli ndi makhalidwe abwino
5Iwe udzaona ndipo nawo adzaona
6Kuti ndani wa inu amene ndi wamisala
7Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwino amene wasochera ku njira yake ndipo amadziwa bwino amene amayenda m’njira yoyenera
8Motero usatsatire zochita za anthu osakhulupirira
9Iwo afuna utagwirizana nawo kuti nawonso agwirizane nawe
10Ndipo usamvere zonena za munthu wotukwana amene alibe phindu
11Woononga mbiri ya anzake ponena Al Qalam 613 za bodza
12Woletsa ntchito zachilungamo, wophwanya malamulo ndi wochita zoipa
13woipa mtima ndipo wobadwa mosalongosoka
14Chifukwa iye ali ndi chuma ndi ana
15Pamene chivumbulutso chathu chilakatulidwa kwa iye, amati: “Ndi nkhani za anthu a makedzana.”
16Ife tidzaika chizindikiro pa mphuno pake
17Ndithudi Ife tidawayesa iwo monga momwe tidawayesera eni ake a munda, amene adalumbira kuti adzakolola mbewu zawo m’mawa mwake
18Osaonjezera mawu oti: “Ngati Mulungu alola.”
19Kotero kudadutsa china chake chochokera kwa Ambuye wako nthawi ya usiku ndi kuwotcha pamene iwo anali kugona
20Ndipo m’mawa, munda udasanduka wakuda monga mdima wa usiku
21Ndipo mmawa iwo adaitanizana wina ndi mnzake
22Nati: “Mulawirire ku munda ngati mufuna kukakolola.”
23Ndipo iwo adapita, namanong’onezana wina ndi mnzake
24“Palibe munthu wosauka amene adzaloledwa kulowa m’mundamo kudzapempha”
25Ndipo m’mawa, onse adapita ndi mphamvu zotchinjirizira anthu osauka
26Koma pamene iwo adaona zimene zidachitika, onse adati: “Ndithudi ife talakwa.”
27“Iai! Ndithudi ife tapwetekeka.”
28wangwiro amene anali pakati pawo adati: “Kodi ine sindidakuuzeni kuti bwanji inu simunena kuti: Ngati Mulungu alola?”
29“Iwo adati ulemerero ukhale kwa Ambuye wathu! Ndithudi ife ndife olakwa.”
30Ndipo iwo adayamba kudzudzulana kuti wina adali wolakwa
31Iwo adati: “Tsoka kwa ife! Ndithudi Ife tidali ophwanya malamulo.”
32“Mwina kuti Ambuye wathu adzatipatsa munda wina wabwino m’malo mwa uwu. Ndithudi ndi kwa Iye kumene timapempha modzichepetsa.”
33Chimenechi ndicho chilango koma ndithudi chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chowawa kwambiri, iwo akadadziwa
34Ndithudi anthu onse angwiro adzalandira minda ya madalitso imene ili ndi Ambuye wawo
35Kodi Ife tidzasamala anthu angwiro chimodzimodzi ndi anthu ochimwa
36Kodi mwatani? Kodi inu mumaweruza bwanji
37Kapena kodi muli ndi Buku limene mumawerengamo
38Kuti inu mudzapeza m’menemo chilichonse chimene mukufuna
39Kapena inu mwalandira kuchokera kwa Ife, lonjezo lotsimikizika mpaka pa tsiku louka kwa akufa kuti, ndithudi, inu mudzapeza zimene mukufuna
40Tawafunsa ngati wina wa iwo angachitire umboni za lonjezolo
41Kapena, kodi iwo ali ndi milungu ina? Aleke abweretse milungu yawo ngati iwo anena zoona
42Ndipatsikulimenechinthuchoopsachidzachitika, iwo adzaitanidwa kuti apembedze, koma adzalephera kutero
43Maso awo adzayang’ana pansi ndipo adzanyozedwa kwambiri chifukwa iwo adauzidwa kupembedza pamene adali pa mtendere
44Kotero ndisiyire aliyense amene akutsutsana ndi chenjezo ili. Ife tidzawalanga pang’onopang’ono m’njira imene iwo saizindikira
45Ndipo Ine ndidzalekerera pa kanthawi! Ndithudi chikonzero changa ndi champhamvu
46Kapena kodi iwe uli kuwafunsa malipiro moti iwo ali ndi ngongole yambiri
47Kapena kodi iwo amadziwa za Buku lobisika kuti iwo akhoza kulemba
48Motero pirira podikilira chiweruzo cha Ambuye wako ndipo usakhale ngati amene adamezedwa ndi nsomba pamene adalira kupempha chithandizo iye ali m’mavuto
49Ngati Ambuye wake akadapanda kumuonetsa chisomo chake, ndithudi iye akadakhalabe koma iye adaponyedwa pa mtunda pamene anali wolakwa
50Koma Ambuye wake adamusankha ndipo adamuchititsa kukhala wabwino
51Ndipo, ndithudi, iwo onse osakhulupirira akadakusokeretsa ndi maso awo pamene amakumbutsidwa ndipo amati: “Ndithudi uyu ndi Wamisala.”
52Koma ichi si china koma chikumbutso kwa zolengedwa zonse
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath