67. Al-Mulk
1wodalitsika ndiye amene mmanja mwake muli Ufumu ndipo ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
2Iye amene adalenga imfa ndi moyo kuti akhoza kukuyesani inu kuti ndani wa inu amene wasunga malamulo onse mwaubwino. Ndipo Iye ndi Wamphamvu ndi Wokhululukira
3Iye ndi amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake. Inu simungaone cholakwa china chilichonse mu chilengedwe cha Mwini chisoni chosatha. Tapenyetsetsani! Kodi inu mungaone cholakwika china chilichonse
4Tapenyetsetsaninso! Ndipo mawonekedwe anu adzakubwererani pamene ali osokonezeka ndi otopa
5Ndithudi Ife takongoletsa thambo loyamba ndi nyali ndipo tazipanga nyalizo ngati mipaliro yothamangitsira Satana ndipo tawakonzera iwo chilango chamoto woyaka
6Ndipo iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo, kuli chilango cha kumoto ndipo chimaliziro chawo chidzakhala choipa
7Ndipo pamene iwo adzaponyedwa m’moto, iwo adzaumva uli kuyaka ndi kubwata
8Pafupifupi kuphulika chifukwa cha kukwiya. Ndipo nthawi zonse pamene gulu liponyedwamo, amene amayang’anira moto adzafunsa kuti: “Kodi panalibe wina aliyense amene adadza kwa inu kudzakuchenjezani?”
9Ndipo iwo adzati: “Inde. Ndithudi Mchenjezi adadza kwa ife koma tidamukana ndipo tinkati: Mulungu sadavumbulutse china chilichonse ndipo iwe ndiwe wosokoneza kwambiri.”
10Ndipo iwo adzati: “Tikadakhala kuti tidamvera kapena kuganiza bwino, ife sitikadakhala m’gulu la anthu opita ku moto.”
11Motero iwo adzabvomera machimo awo. Motero apite kutali anthu a ku moto
12Ndithudi! Iwo amene amaopa Ambuye wawo ngakhale samuona, ndithudi, iwo adzawakhululukira machimo awo ndipo adzalandira mphotho ya mtengo wapatali
13Ndipo kaya mubisa mawu anu kapena muulula, Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwanu
14Kodi Iye amene adalenga zinthu zonse asadziwe? Ndithudi Iye ndi wa Chisoni chosatha ndi Mwini kudziwa chili chonse
15Iye ndiye amene anakukonzerani dziko, motero pitani paliponse mu ilo, ndipo idyani zokoma zake zimene wakupatsanindipondikwaIyekumenezonsezidzabwerera
16Kodi inu mumaganiza kuti ndinu wokhazikika moti Iye amene ali pamwamba pa kumwamba sangathe kung’amba nthaka imene ili pansi panu kuti ikumezeni? Taonani! Ili kugwedezeka
17Kapena mumaganiza kuti inu ndinu okhazikika kuposa zimene zili kumwamba kuti Iye sangathe kukutumizirani mphepo ya mkuntho? Kotero inu mudzadziwa kuopsa kwa chenjezo langa
18Ndithudi iwo amene adalipo kale anakana. Kodi chilango changa chinali bwanji
19Kodiiwosaonambalamezimenezimaulukapamwamba pawo, zikutambasula ndi kutseka mapiko awo? Palibe chimene chimazigwira kupatula Mwini chisoni chosatha. Ndithudi Iye amaona chilichonse
20Kodi ndani amene angakuthandizeni inu kupatula Mwini chisoni chosatha? Anthu onse osakhulupirira ndi olakwa
21Kodi ndani amene angakupatseni chisamaliro ngati Iye atakaniza chisamaliro chake? Koma iwo amapitiriza kuchita mtudzu ndi kugalukira
22Kodi iye amene amayenda osaona ndi ofanana ndi amene walangizidwa kapena amene amayenda mu njira yoyenera
23Nena: “Ndiye amene adakulengani inu ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Inu simuthokoza kawirikawiri.”
24Nena: “Ndiye amene anakulengani inu kuchokera ku doti ndipo kwa Iye nonse mudzasonkhanitsidwa.”
25Iwo amati: “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene ulikunena ndi zoona?”
26Nena: “Mulungu yekha ndiye amene adziwa nthawi yake. Ntchito yanga ndikungokuchenjezani basi.”
27Koma pamene iwo adzachiona chili nkudza pafupi, nkhope za anthu osakhulupirira zidzakhala za chisoni ndipo kudzanenedwa kuti: “Ichi ndi chimaliziro chimene munkafunsa kuti chidzafika liti?”
28Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati Mulungu atandiononga ine pamodzi ndi iwo amene ali nane, ngakhale kuti Iye adzaonetsa chifundo pa ife, ndani amene angateteze anthu osakhulupirira ku chilango chowawa?”
29Nena: “Iye ndi Mwini chifundo chosatha, mwa Iye ife timakhulupirira ndipo mwa Iye ife timaika chikhulupiriro chathu. Kotero inu mudzadziwa posachedwapa kuti ndani amene ali wochimwa.”
30Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati madzi anu ataphwa, ndani amene angakupatseni inu madzi oyenda?”
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath