66. At-Tahrim
1Oh iwe Mtumwi! Bwanji ukudziletsa zinthu zimene Mulungu adakuloleza kuti uchite ndipo iwe ufuna kukondweretsa akazi ako? Ndipo Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse, Mwini chisoni chosatha
2Mulungu wakulolezani kuti mukhoza kumasula malonjezo anu. Ndipo Mulungu ndiye Mtetezi wanu, ndipo ndi wodziwa ndi Mwini nzeru zonse
3Ndi pamene Mtumwi anamuuza nkhani ya chinsinsi wina wa akazi ake ndipo iye adaulula kwa mnzake wina ndipo Mulungu adamuuza iye za izo, Iye anamuuza gawo la nkhani ndipo anasiya gawo lina. Ndipo pamene iye adamuuza mkaziyo za izo, iye adati: “Ndani wakuuzani izi?” Iye adati: “Wandiuza ndi amene amadziwa chilichonse ndi Mwini kuzindikira.”
4Ngati inu awiri mulapa machimo anu kwa Mulungu ndipo mitima yanu itsimikiza kutero, koma ngati inu mugwirizana kulimbana naye, ndithudi, Mulungu ndiye Mtetezi wake, ndi Gabriele ndipo aliyense wolungama amene ali pakati pa anthu amene akhulupirira ndi angelo. Onse ndi omuthandiza iye
5Zingatheke kuti pamene iye akusudzulani inu, Mulungu adzamupatsa m’malo mwanu, akazi ena abwino oposa inu amene amadzipereka kwa Mulungu, amene ali okhulupirira, opirira, olapa kwa Mulungu, opembedza modzichepetsa, osala zifuniro zawo, kapena obwera amene anakwatiwapo kale kapena a namwali
6oh inu okhulupirira! Dzitetezeni nokha ndi mabanja anu ku moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala ndipo oyang’anira ake ndi angelo a mphamvu a maonekedwe oopsa amene sakana kumvera malamulo amene amalandira kuchokera kwa Mulungu ndipo amachita, mwamsanga, chilichonse chimene Mulungu wawalamula
7oh inu osakhulupirira! Musawiringule lero! Inu muli kulandira mphotho yolingana ndi zimene mudachita
8oh inu anthu okhulupirira! Lapani kwa Mulungu mwachoonadi! Mwina Ambuye wanu angakuchotserani machimo anu ndi kukulowetsani inu m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje. Tsiku limene Mulungu sadzalola kuti Mtumwi ndi iwo amene amamutsatira kuti azunzidwe, nyali yawo idzayaka patsogolo pawo ndi Buku ku dzanja lamanja lawo. Iwo adzati: “Ambuye wathu walitsani nyali yathu ndipo tikhululukireni. Ndithudi inu muli ndi mphamvu pa zinthu zonse.”
9oh iwe Mtumwi! Limbika kwambiri pogonjetsa anthu osakhulupirira ndi anthu a chinyengo ndipo chita nawo mwankhanza, malo awo ndi kumoto, omwe ndi malo oipa kwambiri kukhalako
10Mulungu ali kupereka chitsanzo kwa anthu osakhulupirira cha nkhani ya mkazi wa Nowa ndi mkazi wa Loti. Iwo adali akazi a Atumiki athu awiri a ngwiro, koma onse adanyenga amuna awo. Iwo sadalandire kuchokera kwa Mulungu chabwino china chilichonse chifukwa chamakhalidwe awo. Koma iwo adauzidwa kuti: “Lowani inu kumoto pamodzi ndi ena amene ali kulowako.”
11Ndipo Mulungu wapereka chitsanzo kwa anthu okhulupirira, nkhani ya mkazi wa Farao. Pamene iye adati: “oh Ambuye wanga! Ndimangireni pafupi ndi Inu, nyumba ya ulemu ku Paradiso, ndipo ndipulumutseni kwa Farao ndi ntchito zake ndipo ndipulumutseni ine kwa athu amene amachita zoipa.”
12Ndi Maria mwana wa Imran, amene adadzisunga wosadulaunamwaliwakendipo Ifetidauziram’thupimwake mzimu wathu ndipo Iye adachitira umboni wachilungamo cha Ambuye wake ndi chivumbulutso chake. Ndipo iye adali mmodzi wa odzipereka kwa Mulungu
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath