65. At-Talaaq
1Oh iwe Mtumwi! Ngati usudzula akazi ako, asudzule potsatira nthawi zawo. Ndipo werenga bwino bwino masiku awo. Ndipo opani Mulungu Ambuye wanu ndipo musawapirikitse m’nyumba zawo ndipo iwo asachoke pokhapokha ngati iwo apalamula mlandu wachigololo. Amenewa ndiwo malamulo amene akhazikitsidwa ndi Mulungu. Ndipo aliyense amene aphwanya malamulo a Mulungu, ndithudi, amapondereza mzimu wake. Inu Al Talaq 605 simudziwa kuti, mwina, Mulungu adzakukumanizaninso
2Ndipo ngati iwo ali pafupi kukwaniritsa nthawi yawo, mukhoza kuwasunga mwaubwino kapena kuwasiya mwaulemu. Ndipo itanani mboni ziwiri za chilungamo kuchokera pakati panu. Ndipo perekani umboni wanu chifukwa cha Mulungu. Limeneli ndi langizo limene laperekedwa kwa iye amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamupulumutsa
3Ndipo Iye adzamupatsa zinthu kuchokera ku mbali imene sanali kuyembekeza. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye adzamupatsa chili chonse. Mulungu, ndithudi, adzamupatsa iye zofuna zake zonse. Ndithudi Mulungu adakhazikitsa muyeso wa chilichonse
4Ndipo ena akazi anu amene adasiya kupita kumwezi, kwa iwo nthawi yawo yodikira, ngati inu mukaika, ndi miyezi itatu ndipo iwo amene anasiyiratu, nthawi yawo idzakhala chimodzimodzi. Ndipo iwo amene ali ndi akazi odwala pakati, nthawi yawo idzakhala mpaka pamene abereka. Ndipo aliyense amene amaopa Mulungu, Iye adzamuchepetsera mavuto ake
5Uwu ndi ulamuliro wa Mulungu umene wakutumizirani inu. Ndipo aliyense amene aopa Mulungu, Iye adzamuchotsera zoipa zake. Ndipo Iye adzamuchulukitsira mphotho yake
6Khalani nawo monga momwe inu muli kukhalira, molingana ndi kupeza kwanu. Musawazunze ndi cholinga chowasowetsa mtendere. Ngati iwo ali ndi pakati, asamalireni mpaka pamene iwo abereka. Ndipo ngati iwo ali kuyamwitsa, apatseni malipiro awo ndipo lemekezanani. Ndipo ngati pali mavuto oti simuli kugwirizana m’banja, pezani Mayi wina kuti ayamwitse mwana m’malo mwake
7Mulekeni munthu wolemera kuti apereke molingana ndi chuma chake ndipo munthu wosauka molingana ndi mmene Mulungu adamupatsira iye. Mulungu sakhazika mtulo wolemera pa munthu umene sangathe kuunyamula. Mulungu adzapereka mtendere mavuto akatha
8Ndipo ndi mizinda yambiri imene idaukira malamulo a Mulungu ndi Atumwi ndipo Ife tidayilanga iyo ndipo tidzailanga ndi chilango choopsa zedi
9Motero iyo idalawa mphotho ya kusakhulupilira kwake ndipo mapeto a kusakhulupilira adali chionongeko
10Mulungu wawakonzeraiwochilangochoopsa. Moteroopani Mulungu oh inu anthu ozindikira! Inu amene mwakhulupirira, ndithudi, Mulungu watumiza chikumbutso kwa inu
11Mtumwi amene ali kukuuzani zizindikiro zooneka za Mulungu ndi cholinga choti atsogolere onse amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku mdima kupita kowala. Ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzamulowetsa m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje kuti adzakhaleko mpaka kalekale. Ndithudi Mulungu wawapatsa iwo mphotho yabwino kwambiri
12Ndi Mulungu amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri ndi dziko lapansi lolingana nayo. Malamulo ake amatsatiridwa ndi izo kuti inu mukhoza kudziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse ndipo kuti Mulungu amadziwa chilichonse
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath