64. At-Taghaabun
1Chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi chimatamanda ndi kulemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini ufumu ndipo kwake ndi kuyamikidwa ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse
2Ndiye amene adakulengani inu ndipo ena a inu ndi osakhulupirira pamene ena ndi okhulupirira. Mulungu amaona zonse zimene mumachita
3Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwa chilungamo ndipo Iye adakulengani ndi kukupatsani maonekedwe abwino ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera
4Iye amadziwa chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndipo amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zimene mumaulula. Ndithudi Mulungu amadziwa bwino lomwe zinsinsi za m’mitima mwanu
5Kodi inu simudamve za iwo amene sadakhulupirire kale? Ndipo iwo adalawa chilango chifukwa chosakhulupilira, ndipo chawo chidzakhala chilango chowawa kwambiri
6Ichi ndi chifukwa chakuti kunadza kwa iwo Atumwi amene adali ndi zizindikiro zooneka koma iwo adati: “Kodi ife tizitsogozedwa ndi anthu anzathu?” Kotero iwo sanakhulupilire ndipo anabwerera m’mbuyo. Koma Mulungu sasowa kanthu. Ndithudi Mulungu ndi Mwini wa chilichonse ndi Mwini ulemerero wonse. Al Taghabun
7Anthu osakhulupirira amaganiza kuti sadzaukitsidwa kwa akufa. Nena: “Inde! Pali Ambuye wanga! Inu, ndithudi, mudzaukitsidwa kwa akufa ndipo mudzauzidwa zimene mudachita. Zimenezo ndi za pafupi ndi Mulungu.”
8Motero khulupirirani mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake ndi mu Muuni umene Ife tatumiza. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita
9Patsiku limene Iye adzakusonkhanitsani inu nonse, tsiku losonkhana, tsiku limeneli lidzakhala tsiku la mavuto ndi la mtendere kwa ena a inu. Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, Iye adzawakhululukira machimo awo ndipo adzawaika m’minda imene imathiriridwa ndi mitsinje yoyenda madzi pansi pake kuti akhale m’menemo mpaka kalekale. Kumeneko ndiko kupambana kwenikweni
10Koma iwo amene sakhulupirira ndipo amakana ulangizi wathu, iwo adzakhala ku moto nthawi zonse omwe ndi malo oipitsitsa kukhalako
11Palibe vuto limene limadza popanda chilolezo cha Mulungu ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu, Iye amatsogolera mtima wake ndipo Mulungu amadziwa chilichonse
12Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake. Koma ngati inu mukana, udindo wa Mtumwi wathu ndi kukuuzani uthenga wathu momveka ndi poyera
13Mulungu! Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo mwa Mulungu onse okhulupirira aike chikhulupiriro chawo
14Oh inu okhulupirira! Ndithudi pakati pa akazi ndi ana anu alipo ena amene ndi adani anu, motero chenjerani! Koma ngati inu muwakhululukira ndipo simulabadira zoipa zawo, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha
15Chuma chanu ndipo ana anu ndi mayesero pamene Mulungu ndiye amene ali ndi mphotho yaikulu
16Kotero kwaniritsani udindo wanu kwa Mulungu ndipo muopeni Iye kwambiri. Mverani ndipo mumvere. Ndipo perekani chopereka chaulere. Chimenecho ndi chabwino kwa inu. Ndipo aliyense amene asiya umbombo adzakhala wopambana
17Ngati mukongoza Mulungu ngongole yabwino, Iye adzaichulukitsa ndipo adzakukhululukirani machimo anu. Ndipo Mulungu ndi wokonzeka kuyamika ndi kulipira ndipo ndi wopilira kwambiri
18Wodziwa zonse zobisika ndi zooneka ndipo ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath