61. As-Saff
1Chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi, chimalemekeza Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru
2oh inu okhulupirira! Kodi bwanji mumanena zinthu zimene simuchita
3Ndithudi ndi chinthu chonyansa kwambiri pamaso pa Mulungu kuti muzinena chinthu chimene simuchita
4Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amamenya nkhondo ndi cholinga chokhazikitsa ulamuliro wake molimba, m’magulu, ngati chipupa cha miyala
5Ndi pamene Mose adanena ndi anthu ake: “oh inu anthu anga! Kodi bwanji mukundikwiyitsa pamene muli kudziwa kuti ine ndine Mtumwi wa Mulungu kwa inuyo?” Ndipo pamene iwo adalakwa, Mulungu adalola kuti mitima yawo ilakwe. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ophwanya malamulo
6Ndi pamene Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, adati: “oh inu ana a Israyeli! Ine ndine Mtumwi wa Mulungu amene ndatumidwa kwa inu, kutsimikizira za Buku la Chipangano chakale limene lidadza ine ndisanadze, ndi kuulula nkhani yabwino ya Mtumwi Ahmad amene adzabwera ine nditachoka.” Koma pamene iye adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adati: “Awa ndiwo matsenga enieni.”
7Kodi amalakwa kwambiri ndani kuposa As-Saff 597 iye amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ngakhale pamene ali kuitanidwa kuti alowe Chisilamu? Ndipo Mulungu satsogolera iwo amene amachita zoipa
8Cholinga chawo ndikufuna kuzimitsa nyali ya Mulungu ndi milomo yawo. Koma Mulungu adzateteza nyali yake ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo
9Ndiye amene watumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi kuti chikhale chapamwamba pa zipembedzo zina zonse ngakhale kuti anthu osakhulupirira sakondwera nazo
10Oh inu anthu okhulupirira! Kodi ndikulangizeni malonda apafupi amene angakuomboleni ku chilango choopsa
11Kuti mukhulupirire mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, kuti mudzipereke kwathunthu mu njira ya Mulungu pogwiritsa ntchito chuma chanu ndi inu eni ake. Chimenechi ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu mukadadziwa
12Iyeadzakukhululukiraniinumachimoanu ndi kukulandirani m’minda imene pansi pake pamayenda mitsinje, ndipo adzakulowetsani m’nyumba zokongola ndi zaulemu za m’Paradiso. Kumeneko, ndithudi, ndiko kupambana kwenikweni
13Ndipo Iye adzakupatsani madalitso ena amene mumakonda. Chithandizo chochokera kwa Mulungu ndi kupambana mwamsanga. Kotero auze nkhani yabwino anthu okhulupirira
14oh inu okhulupirira! Khalani otumikira Mulungu monga momwe ananenera Yesu, mwana wa mwamuna wa Maria, kwa ophunzira ake: “Kodi ndani andithandiza ine potumikira Mulungu?” Iwo adayankha: “Ife ndife othandiza Mulungu.” Kotero ena mwa ana a Israyeli adakhulupirira pamene ena sadakhulupirire. Motero Ife tidawapatsa mphamvu iwo amene adakhulupirira zopambana adani awo ndipo iwo adapambanadi
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath