60. Al-Mumtahana
1oh inu anthu amene mwakhulupirira! Musasandutse adani anga ndi adani anu kukhala abwenzi anu powaonetsa chikondi chanu pamene iwo akana choonadi chimene chadza kwa inu ndipo amupirikitsa Mtumwi pamodzi ndi inu nomwe kuchokera ku nyumba zanu, chifukwa chakuti inu mumakhulupirira mwa Mulungu Ambuye wanu. Ngati inu mwadza ndi cholinga chogwira ntchito m’njira yanga ndi kufunafuna chisangalalo changa(musachite nawo ubwenzi). Ndipo ngati inu mumaonetsa chikondi kwa iwo mwamseri, ndithudi, mukatero mwasochera. Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita mseri
2Ngati iwo akupambanani, ndithudi, adzakuonetsani kuti ndi adani anu ndipo adzagwiritsa ntchito manja awo ndi malirime awo pa inu pokuchitirani zoipa. Iwo afunitsitsa kuti nanu mukhale anthu osakhulupirira
3Abale anu kapena ana anu sadzakhala a phindu kwa inu patsiku la chiweruzo. Iye adzaweruza pakati panu chifukwa Mulungu amaona zonse zimene mumachita
4Muli chitsanzo chabwino kwa inu mwa Abrahamu ndi mwa iwo amene adali naye pamene iwo ananena kwa anthu awo kuti: “Ife sitili m’gulu lanu ndipo sitipembedza zimene inu mumapembedza pozifanizira ndi Mulungu. Ife takukanani ndipo pabuka pakati pa ife ndi inu udani ndi chidani chosatha kupatula ngati inu mukhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Iye yekha.” Kupatula zonena za Abrahamu kwa Abambo ake kuti: “Ine ndidzapempha chikhululukiro chanu chifukwa ine ndilibe mphamvu pa chilichonse cha inu kuchokera kwa Mulungu. Ambuye wathu, mwa Inu ife takhulupirira ndi kwa Inu ndiko timapempha chikhululukiro, ndipo kwa Inu ndiko kumene tonse tidzabwerera pomaliza.”
5“Ambuye wathu, musatisandutse ife kukhala mayesero a anthu osakhulupirira koma tikhululukireni Ambuye wathu. Ndithudi Inu ndinu Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.”
6Ndithudi, mwa iwo mudali chitsanzo chabwino kwa inu kuti mutsatire, makamaka iwo amene amaika chikhulupiriro chawo mwa Mulungu ndi m’tsiku la chiweruzo. Ndithudi Mulungu ndi wolemera ndipo ndiye yekha amene ayenera kulemekezedwa
7Mwina Mulungu angakhazikitse chikondi pakati pa inu ndi iwo amene inu mumawaganizira kuti ndi adani anu. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa china chilichonse ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
8Mulungu sali kukuletsani kuti muonetse chilungamo ndi chisoni kwa iwo amene sadamenyane nanu chifukwa cha chikhulupiliro chanu ndipo sanakuthamangitseni mu nyumba zanu. Ndithudi, Mulungu amakonda iwo amene amachita zolungama
9Mulungu wakuletsani kuchita ubwenzi ndi anthu amene munamenyana nawo chifukwa cha chikhulupiriro ndipo anakuthamangitsani ku nyumba zanu kapena adathandiza anthu ena kuti amenyane ndi kukupirikitsani inu. Ndipo aliyense amene achita ubwenzi ndi anthu otere ndi ochimwa
10Oh inu anthu okhulupirira! Pamene akazi okhulupirira adza kwa inu ngati othawa mavuto, afufuzeni bwinobwino. Mulungu yekha ndiye amene adziwa bwino bwino chikhulupiriro chawo. Ngati inu mukhutitsidwa kuti ndi okhulupirira m’choonadi, musawabwezere kwa anthu osakhulupirira chifukwa iwo saloledwa kukwatiwa ndi anthu osakhulupirira monga momwe amuna osakhulupirira saloledwa kukwatira akazi okhulupirira. Koma abwezereni anthu osakhulupirira ziwongo zimene apereka. Ndipo sikulakwa ngati inu muwakwatira akazi okhulupirirawa ngati mwapereka chiwongo. Musapitilize ukwati wanu ndi akazi wosakhulupirira. Itanitsani zimene mwaononga ngati chiwongo cha ukwati ndipo aloleni osakhulupirira kuti nawonso aitanitse zimene aononga pa akazi okhulupirira amene adza kwa inu. Ili ndi lamulo la Mulungu. Iye amaweruza mwachilungamo pakati panu. Mulungu ndi wa nzeru ndi luntha
11Ndipo ngati ena, mwa akazi anu, athawa ndi kukakwatiwa ndi osakhulupirira, ndipo inu mupeza mwayi wolandira akazi wochokera kwa anthu osakhulupirira abwezereni chiwongo ndi china chilichonse chimene iwo adapereka anthu amene akazi awo awathawa. Ndipo opani Mulungu amene inu mumamukhulupirira
12Oh iwe Mtumwi! Ngati akazi okhulupirira adza kwa iwe kudzalumbira lonjezo lakuti sadzamufanizira Mulungu ndi wina wake akamapembedza, kuti sadzaba, sadzachita chigololo, sadzapha ana awo, sadzalankhula mawu ojeda, sadzapeka nkhani zabodza ndipo kuti adzakumvera iwe pa nkhani ina iliyonse, iwe uyenera kulandira lonjezo lawo ndipo pempha kwa Mulungu kuti awakhululukire machimo awo chifukwa Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
13Oh inu okhulupirira! Musapalane ubwenzi ndi anthu amene adalandira mkwiyo wa Mulungu. Ndithudi iwo ali ndi mantha ndi zimene zidzawachitikira m’moyo umene uli nkudza monga momwe anthu osakhulupirira amachitira mantha ndi iwo amene adaikidwa m’manda
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath