57. Al-Hadid
1Chilichonse chimwe chili kumwamba ndi padziko lapansi chimalemekeza Mulungu. Iye ndiye Mwini mphamvu, Mwini nzeru
2Wake ndi Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndiye amene amapereka moyo ndi imfa ndipo ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
3Iye ndi woyamba ndi womaliza, wapamwamba mwamba ndi wapafupi. Ndipo Iye amadziwa zinthu zonse
4Ndiye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi ndipo adabuka pa mwamba pa mpando wake wa Chifumu. Iye amadziwa chilichonse chimene chimalowa m’nthaka ndi chilichonse chimene chimatuluka mu iyo, zonse zimene zimadza pansi kuchokera kumwamba ndi zonse zimene zimakwera kumwamba. Ndipo Iye ali nanu kulikonse kumene mungakhale. Ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita
5Wake ndi Ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo ndi kwa Iye kumene zonse zimabwerera
6Iye amapanga usiku kulumikizana ndi usana ndi kupanga usana kulumikizana ndi usiku. Iye amadziwa zinsinsi zonse zili m’mitima
7Khulupirirani mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Perekani zopereka zaulere kuchokera ku zinthu zimene Mulungu wakupatsani kuti zikhale zanu. Iwo a inu amene akhulupilira ndipo apereka chaulere, yawo idzakhala mphotho yaikulu
8Kodi ndi chifukwa chiyani kuti inu simukhulupirira mwa Mulungu? Pamene Mtumwi ali kukuitanani kuti mukhulupirire mwa Ambuye wanu ndipo Iye, ndithudi, walandira lonjezo lanu ngati inu ndinu anthu okhulupirira
9Ndiye amene amatumiza kwa kapolo wake zizindikiro zooneka kuti akhoza kukutsogolerani inu kuchoka ku mdima waukulu kupita kowala. Ndipo, ndithudi, Mulungu, kwa inuyo, ndi wachifundo ndi wachisoni
10Kodi ndi chifukwa chiyani inu simufuna kupereka m’njira ya Mulungu? Mulungu ndiye Mwini wa zonse zili kumwamba ndi padziko lapansi. Palibe ofanana, pakati panu, ndi iwo amene amapereka chaulere ndipo adamenya nawo nkhondo poyamba kupambana kusanadze. Amenewa ndi a pamwamba kuposa iwo amene adapereka chaulere ndi kumenya nkhondo pambuyo pake. Koma kwa onsewa, Mulungu walonjeza mphotho yokoma. Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
11Kodi ndani amene adzakongoza Mulungu ngongole yabwino kuti Iye aipindulitse ndipo kuti iye adzakhale ndi mphotho ina yapamwamba
12Patsiku limeneli inu mudzaona amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira, nyali zawo zili kuyaka patsogolo pawo ndi kudzanja lawo lamanja, kulonjerana kwawo kudzakhala nkhani yabwino kwa inu lero lino! Minda imene pansi pake pamayenda madzi mudzakhala m’menemo mpaka kalekale. Kumeneko ndiko kupambana kwenikweni
13Patsiku limene amuna a chinyengo ndi akazi a chinyengo adzanena kwa iwo okhulupirira:“Tidikirirenikutitikhozakulandirachilangali kuchokera ku muuni wanu.” Koma kudzanenedwa kuti: “Bwererani m’mbuyo kuti mukafune muuni wanu. Ndipo chipupa chidzakhazikitsidwa pakati pawo chokhala ndi khomo. Mbali ina ya chipupachi kudzakhala chisomo pamene mbali ina kudzakhala chilango.”
14Iwo adzalira kwa iwo. “Kodi inu sitinali kukhalira limodzi?” Okhulupilira adzayankha kuti: “Zoonadi koma inu mudadzisocheretsa nokha. Inu mudanyengedwa, mudakayikira ndipo zilakolako zanu zidakunyengani inu mpaka pamene chilango cha Mulungu chinachitika. Ndipo wonyenga adakunyengani inu pa nkhani zokhudza Mulungu.”
15Motero lero palibe chiphuphu chimene chidzalandiridwa kuchokera kwa inu kapena iwo amene adakana Mulungu. Malo anu okhala ndi kumoto, amenewo ndiwo malo okhawo amene mudzalandiridwako ndipo ndi malo oipitsitsa kukhalamo
16Kodi nthawi siinakwane yoti okhulupirira enieni apereke mitima yawo modzichepetsa ndipo kuti azikumbukira Mulungu ndi choonadi chimene chavumbulutsidwa kwa iwo ndipo kuti asakhale ngati iwo amene adapatsidwa Buku nthawi ya kale? Koma patapita nthawi, mitima yawo idalimba. Ndipo ambiri a iwo ndi ophwanya malamulo
17Dziwani kuti Mulungu amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi taonetsa chivumbulutso chathu poyera kwa inu kuti mukhoza kuzindikira
18Ndithudi iwo amene amapereka chopereka chaulere, amuna kapena akazi, iwo amasunga gawo lawo kwa Mulungu lomwe lidzaonjezeredwa mopitiriza muyeso ndipo adzakhala ndi mphotho yolemekezeka
19Ndipo iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi mwa Mtumwi wake, iwo ndi olungama ndi okhulupirira pamaso pa Ambuye wawo. Iwo adzalandira mphotho yawo pamodzi ndi muuni. Ndipo iwo amene sakhulupirira ndipo amakana chivumbulutso chathu, amenewa ndiwo a ku moto wa ku Gahena
20Dziwani kuti moyo wa padziko lino lapansi ndi masewera ndi wotailako nthawi, chionetsero ndi kunyada ndi mpikisano pakati pa wina ndi mnzake wofuna chuma ndi ana. Fanizo lake lili ngati mvula ndi zomera zimene zimadza chifukwa cha zimene zimabweretsa chisangalalo kwa ozilima. Pasanapite nthawi izo zimafota ndi kuoneka za chikasu. Ndipo zimauma ndi kugwa pansi. Koma m’moyo umene uli kudza, kuli chilango chowawa kwa anthu ogona m’machimo ndi chikhululukiro chochokera kwa Mulungu ndiponso chisangalalo chake kwa iwo amene amadzipereka kwa Mulungu. Kodi moyo wa padziko lino lapansi ndi chiyani kupatula chinyengo chabe
21Kotero fulumirani kupeza chikhululukiro cha Mulungu ndi munda wa Paradiso umene kutalika kwake kuli ngati kukula kwa kumwamba ndi dziko lapansi umene udakonzedwera iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Atumwi ake. Chimenechi ndicho chisomo cha Mulungu chimene amapereka kwa amene Iye wamufuna. Mulungu ndi Ambuye wa chisomo chosatha
22Palibe vuto limene limadza padziko kapena pa inu limene silinakhazikitsidwe kale Ife tisanalibweretse. Ndithudi chimenechi ndi chosavuta kwa Mulungu
23Kuti inu musakhumudwe chifukwa cha zinthu zabwino zimene simudazipeze kapena kunyada chifukwa cha zokoma zimene zaperekedwa kwa inu. Mulungu sakonda anthu odzikundikira
24Ndiponso anthu a umbombo amauza anzawo kuti nawonso azikhala a umbombo. Ngati wina abwerera m’mbuyo kuchokera ku njira ya Mulungu, ndithudi, Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi wolemekezeka
25Ndithudi tidatumiza kale Atumwi athu ndi zizindikiro zooneka ndipo tidatumiza pamodzi ndi iwo Buku ndi muyeso kuti anthu akhoza kukhala ndi makhalidwe abwino. Ndipo Ife tidapanga chitsulo chimene m’kati mwake muli mphamvu ndi zinthu zambiri zabwino kwa anthu. Kuti Mulungu akhoza kuyesa iwo amene amamuthandiza Iye ndi Mtumwi wake mwamseri. Ndithudi Mulungu ndi wolimba ndi wamphamvu
26Ndithudi Ife tidatumiza Nowa ndi Abrahamu ndipo tidapereka kwa ana awo mphatso ya Utumwi ndi Buku ndipo ena pakati pawo ndi otsogozedwa bwino koma ambiri ndi ophwanya malamulo
27Ndipo tidawapanga Atumwi athu kuti atsatire m’mapazi mwawo; Ndipo tidatumiza Yesu, mwana wa Maria, pambuyo pake ndipo tidamupatsa Uthenga wabwino. Ndipo tidaika m’mitima mwa iwo amene adali kumutsatira iye kukoma mtima ndi chisoni. Ukakhala unsembe iwo adapeka okha, chifukwa Ife sitidawalamulire kuti akhazikitse kupatula kuti azifunafuna chisangalalo cha Mulungu koma iwo sadazilabadire ayi. Kotero tidawapatsa mphotho iwo amene adakhulupirira koma ambiri a iwo ndi oswa malamulo
28oh inu anthu okhulupirira! Samalani udindo wanu kwa Mulungu ndipo mukhulupilire mwa Mtumwi wake. Iye adzakupatsani magawo awiri a chisomo chake ndikukonzerani muuni umene muzidzayenda nawo ndi kukukhululukirani machimo anu. Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
29Kuti anthu a m’Buku adziwe kuti iwo alibe mphamvu ina iliyonse pa chisomo cha Mulungu ndipo kuti chisomo chake chili m’manja mwake mokha ndipo amachipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu ndiye Mwini mphatso zosatha
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath