Chisilamu
kubwerera

56. Al-Waaqia

1Pamene ola la chiweruzo lidza

2Ndipo palibe mzimu umene udzakana kudza kwake

3Kutsitsa gulu lina ndikukweza gulu linzake

4Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chigwedezo choopsya

5Ndi pamene mapiri adzafumbutuka kukhala fumbi lokhalokha

6Motero iwo adzakhala fumbi louluzika paliponse

7Ndipo inu mudzagawidwa m’magulu atatu

8Iwo a ku dzanja la manja. Kodi a ku dzanja la manja adzakhala ndani

9Iwo akudzanja la mazere. Kodi akudzanja la mazere adzakhala ndani

10Ndipo gulu la iwo amene adzakhala kutsogolo m’chikhulupiriro adzakhala kutsogolo m’moyo umene uli nkudza

11Awa ndiwo amene adzakhala kufupi ndi Mulungu

12M’minda ya Paradiso

13Gulu lalikulu lidzachokera ku mibadwo ya kale

14Ndi gulu lochepa lidzachokera ku mibadwo ya m’mbuyo mwake

15Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo yomatidwa golide ndi miyala ya mtengo wapatali

16Atakhala pa iyo ndi kumayang’anizana

17Iwo adzatumikiridwa ndi anyamata a muyaya

18Ndi mabakuli, miphika ndi zikho za vinyo wabwino

19Amene sadzawawitsa mitu yawo kapena kuwatopetsa

20Ndi zipatso zimene adzasankhepo

21Ndi nyama ya nkhuku imene angafune

22Ndipo padzakhala anzawo okongola, a maso akulu ndi ochititsa kaso

23Monga ndolo zosamalidwa bwino

24Malipiro a ntchito zimene adachita kale

25Palibe nkhani zopanda pake kapena zolaula zimene adzamva

26Kupatula mawu akuti Mtendere, Mtendere

27Iwo a kudzanja lamanja, kodi akudzanja lamanja adzakhala ndani

28Iwo adzakhala pakati pa m’mithunzi ya mitengo ya Sidrah

29Ndi m’mapata a nthochi zokhala ndi mikoko wina pamwamba pa unzake

30M’mithunzi yotambasuka

31Pambali pa madzi osefukira

32Ndi zipatso zochuluka

33Zimene nyengo yake sikutha ndipo kuchuluka kwake kudzakhalabe

34Ndi pa mipando yawofowofo yokwezedwa

35Ndithudi Ife tawalenga iwo mu chilengedwe cha padera

36Ndi kuwapanga kukhala a Namwali abwino

37A chikondi pa anzawo olingana nawo zaka

38A iwo amene adzakhala kudzanja lamanja

39Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo yoyamba, yakale

40Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo ya pambuyo pake

41Gulu la anthu a kudzanja lamanzere. Kodi anthu a kudzanja la manzere adzakhala otani

42M’katikati mwa malawi a moto ndi m’madzi ogaduka

43Ndi m’mithunzi ya utsi wakuda

44Yosazizira kapena yabwino

45Ndithudi iwo kale adali kukhala m’moyo wosavutika ndi opeza zinthu zambiri

46Ndipo adapitirira kuchita zoipa zikulu zikulu

47Ndipo iwo anali kukonda kunena kuti: “Pamene ife tafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tingadzaukitsidwenso?”

48“Ndi makolo athu a nthawi ya makedzana?”

49Nena: “Ndithudi onse oyambirira ndi otsiriza.”

50“Ndithudi onse adzasonkhanitsidwa pamodzi pa tsiku lokhazikitsidwa.”

51“Kuphatikiza inu nonse amene muchimwa ndi kukana choonadi.”

52“Ndithudi inu mudzadya zipatso za mtengo wa Zaqqoom.”

53“Ndipo mudzakhutitsa mimba zanu ndi izo.”

54“Ndi kumwa madzi ogaduka.”

55“Ndi kumwa monga momwe ngamira yodwala ndi yaludzu imamwera.”

56Kumeneko ndiko kudzakhala kusangalala kwawo patsiku lachiweruzo

57Ndife amene tidakulengani inu nanga ndi chifukwa chiyani simukhulupilira

58Ndiuzeni za umuna umene mumatulutsa

59Kodi ndinu amene mumaulenga kapena Ife ndife timaulenga

60Ife tidalamulira imfa kukhala pakati panu ndipo Ife sitingagonjetsedwe ayi

61Kukusinthani inu ndi kukulengani kukhala china chake chimene inu simuchidziwa

62Ndithudi inu mumadziwa za chilengedwe choyamba. Nanga ndi chifukwa chiyani simulabadira

63Kodi mudayamba mwaganiza za mbewu imene mumabzala

64Kodi ndinu amene mumaimeretsa kapena ndife amene timameretsa

65Ngati titafuna, Ife tikadaiphwanya m’timagawomagawo touma ndipo inu mukadayamba kudandaula

66Ndithudi ife tapatsidwa chingongole cholemera

67Iyayi. Koma tamanidwa

68Kodi inu mumawaona madzi amene mumamwa

69Kodi ndinu amene mumawagwetsa kuchokera ku mitambo kapena ndife

70Chikadakhala chifuniro chathu tikadawapanga iwo kukhala a mchere. Nanga ndi chifukwa chiyani simuthokoza

71Kodi inu mumaganizira za moto umene mumasonkha

72Kodi ndinu amene mumameretsa mtengo umene umayaka moto kapena ndife amene timaumeretsa

73Ife taupanga iwo kukhala chikumbutso ndi chinthu chothandiza anthu amene ali paulendo

74Kotero lemekezani dzina la Ambuye wanu Wamkulu

75Ndipo ndilumbira pali nyenyezi zimene zili kugwa

76Ndithudi ili ndi lonjezo lalikulu inu mukadadziwa

77Ndithudi ndi Buku lolemekezeka la Korani

78Limene lili m’Buku lotetezedwa

79Palibe amene adzalikhudza kupatula oyeretsedwa okha

80Chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse

81Kodi muli kunyozabe uthenga uwu

82Mmalo mothokoza chifukwa cha zinthu zimene amakupatsani inu mumamukana Iye

83Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuthandiza pamene mzimu wa munthu amene ali kufa ufika pa khosi pake

84Pamene panthawiyo, inu mumangoyang’ana

85Koma Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu koma inu simutiona

86Nanga ndi chifukwa chiyani simutero ngati inu simudzaweruzidwa patsogolo pake

87Bwezerani mzimuwo ngati ndinu anthu a choonadi

88Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa anthu amene ali kufupi ndi Mulungu

89Iye adzapeza mpumulo ndi chakudya ndi munda wa chisangalalo

90Ndipo ngati iye ndi wam’gulu la anthu akudzanja la manja

91Kotero kuli mtendere kwa iwo a kudzanja lamanja

92Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa iwo okana choonadi ndi amene amalakwa

93Motero kulandiridwa kwake kudzakhala kwa madzi otentha kwambiri

94Ndi kulowetsedwa ku Gahena

95Ndithudi ichi ndi choonadi chosakayikitsa

96Motero lemekezani dzina la Ambuye wanu, Wamkulu

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath