Chisilamu
kubwerera

55. Ar-Rahmaan

1Mwini Chifundo Chosatha

2Ndiye amene adamphunzitsa munthu Korani

3Ndiye amene adalenga munthu

4Wamuphunzitsa iye mawu anzeru

5Dzuwa ndi mwezi zimayenda m’misewu imene zinalamulidwa

6Zomera (kapena nyenyezi) ndi mitengo zonse zimagwada pomulambira Iye

7Iye adakweza kumwamba ndi kukhazikitsa muyeso

8Kuti inu musaphwanye muyeso

9Kotero khazikitsani muyeso wachilungamo ndipo musayese monyenga

10Ndiye amene adalenga dziko lapansi kuti zolengedwa zake zizikhalamo

11Mu ilo muli zipatso ndi mitengo ya tende yobereka phava la zipatso zambiri

12Ndi chimanga chimene masamba ndi mapesi ake amadyedwa ndi ziweto. Ndi mitengo yonunkhira

13Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

14Iye adalenga munthu kuchokera ku dothi monga dothi la mbiya

15Ndipo adalenga majini kuchokera kumoto wopanda utsi

16Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

17Ambuye wa kum’mawa kuwiri ndi Ambuye wa kumadzulo kuwiri

18Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

19Iye adasiya nyanja ziwiri kuti zikumane

20Pakati pawo pali malire amene madzi a uku sangathe kudutsa kupita uko

21Kodi ndi zokoma ziti za Rahman 573 Ambuye wanu zimene mudzakana

22Mu zonse muli nkhombe zazikulu ndi zazing’ono

23Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

24Ndipo zake ndi zombo zimene zimayenda pa nyanja, zazikulu ngati mapiri

25Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

26Zonse zimene zili pa dziko zidzatha

27Ndipo nkhope ya Ambuye wako mu Ufumu ndi mu Ulemerero idzakhalabe mpaka kalekale

28Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

29Zonse zimene zimakhala kumwamba ndi padziko lapansi zimapempha kwa Iye. Tsiku lililonse Iye amakhala ndi chochita

30Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

31Ife tidzadza kwa inu, Oh inu magulu awiri

32Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

33oh inu gulu la Majini ndi Anthu! Ngati muli ndi mphamvu zodutsa malire a kumwamba ndi dziko lapansi, dutsani. Komatu inu simungadutse popanda chilolezo

34Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

35Malawi a moto ndi utsi zidzaponyedwa kwa inu nonse awiri ndipo simudzatha kudziteteza nokha

36Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

37Ndi pamene thambo lidzagawanika pakati ndikukhala lofiira ngati mafuta osungunuka

38Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

39Motero patsiku limeneli, sipadzakhala mafunso kuchokera kwa Munthu kapena Majini okhudza machimo awo

40Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

41ochimwa adzadziwika ndi zizindikiro ndipo adzawagwira tsumba ndi pamapazi pawo

42Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye

43Iyi ndi Gahena imene anthu ochimwa amati ndi bodza

44Iwo adzalowa m’kati mwake ndi m’kati mwa madzi ogaduka

45Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

46Ndipo kwa iye amene aopa kuima pamaso pa Ambuye wawo, kudzakhala minda iwiri

47Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

48Zokhala ndi mphanda zotambasuka

49Kodi ndi zokoma ziti zaAmbuye wanu zimene mudzakana

50Monse mudzakhala a kasupe awiri otumphuka

51Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

52M’menemu mudzakhala zipatso ziwiriziwiri za mitundumitundu

53Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

54Iwo adzagona pa makama amene nsalu yake ya m’kati idzakhala yasilika ndipo zipatso za m’minda iwiriyi zidzakhala pafupi pawo

55Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

56M’menemo mudzakhala wodzisunga ndi ogwetsa nkhope zawo pansi amene Munthu kapena Majini sadawakhudze

57Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

58olingana ndi miyala ya rubiya ndi ndolo

59Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

60Kodi dipo la ntchito yabwino lingakhale lina loposa ubwino

61Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

62Ndipo poonjezera pa minda iwiri pali minda ina iwiri

63Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

64Yooneka mobiriwira

65Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

66Monse mudzakhala a kasupe awiri otulutsa madzi ochuluka

67Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

68Monse mudzakhala zipatso, tende ndi chimanga chachizungu

69Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

70Mmenemo mudzakhala zinthu zokongola

71Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

72Angwiro ndi okhala m’mahema

73Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

74Amene Munthu kapena Majini sadawakhudze

75Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

76Atakhala pa mipando yawofowofo, yobiriwira ndi mabedi okongola

77Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana

78Lidalitsike dzina la Ambuye wako, Mwini ulemerero, chuma ndi ulemu

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath