54. Al-Qamar
1Ola lachiweruzo lili pafupi ndipo mwezi wagawanika pakati
2Koma iwo akaona chozizwitsa, sakhulupirira ndipo amati, “Ichi sichina ayi koma matsenga ozama.”
3Iwo amakana choonadi koma amatsatira zilakolako zawo. Koma chinthu chilichonse chili ndi kumaliza kwake
4Ndithudi uthenga waperekedwa kale kwa iwo umene uli ndi chenjezo
5Wodzadzidwa ndi nzeru koma machenjezo ake sawathandiza iwo china chilichonse
6Kotero iwe, asiye okha. Patsiku limene woitana adzawaitana kudza ku chinthu choopsa
7Iwo adzadza kumeneko ndi nkhope zogwa pansi, kuchokera kumanda awo monga dzombe louluka ponseponse
8Adzadza mofulumira kwa oitana anthu osakhulupirira adzati, “Ili ndi tsiku lovuta kwambiri.”
9Asanadze iwo, anthu a Nowa adakana kapolo wathu ndipo adati, “Uyu ndi munthu wamisala.” Ndipo iwo adamuthamangitsa iye ndi kumunyoza kwambiri
10Ndipo iye adadandaula kwa Ambuye wake nati, “Ndagonjetsedwa kotero idzani kuti mundithandize.”
11Motero Ife tidatsekula makomo a kumwamba, ndipo mvula idagwa nthawi yomweyo
12Ndipo tidatumphutsa a kasupe padziko lapansi kotero madzi onse adakumana monga mwa lamulo lathu
13Ndipo tidamunyamula iye m’chombo chopangidwandimatabwandichokhomedwandimisomali
14Chidanyamuka potsogozedwa ndi Ife. Mphotho kwa iye amene adakanidwa
15Ndithudi tidachisiya icho ngati chizindikiro koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
16Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zalikulu bwanji
17Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulidziwa ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
18Anthu a Aad adakana. Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
19Ndithudi Ife tidatumiza mphepo yamkhuntho pa tsiku latsoka losasimbika
20Kugwetsa anthu ngati kuti adali mathunthu a mitengo ya mgwalangwa yozulidwa
21Kodi chilango changa ndipo chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
22Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
23Anthu a Thamoud adakana machenjezo
24Iwo adati, “Munthu! Mmodzi yekha wochokera ku mtundu wathu kuti timutsatire? Ndithudi ife tikhala olakwa kwambiri ndiponso a misala.”
25“Kodi ndiye kuti uthenga waperekedwa kwa iye yekha pakati pa ife tonse? Iyayi! Iye ndi wabodza ndi wodzikweza.”
26Mawa iwo adzadziwa kuti wabodza ndi wodzikweza ndani
27Ndithudi Ife titumiza ngamira yaikazi ngati mayesero kwa iwo. Motero iwe uwapenyetsetse ndipo ukhale wopirira
28Ndipo uwauze kuti azigawana madzi. Ndipo nthawi yomwera madzi idzakhazikitsidwa
29Ndipo iwo adaitana m’bale wawo ndipo iye adatulutsa lupanga ndi kuipha
30Kodi chilango changa ndi chenjezo langa zidali zoopsa bwanji
31Ndithudi tidawatumizira mfuwu umodzi ndipo onse adali ngati nkhuni zodula zimene munthu womanga mpanda amatola
32Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Koma kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
33Anthu a Loti adati chenjezo lathu ndi labodza
34Ndithudi Ife tidawatumizira mphepo yonyamula miyala kupatula a pa banja la Loti amene tidawapulumutsa mu ola lomaliza la usiku
35Monga chisomo chochokera kwa Ife, motero ndi mmene timalipirira anthu oyamika
36Ndithudi iye adawachenjeza za chilango chathu choopsa koma iwo adakana chenjezo lathu
37Ndipo, ndithudi, iwo adafuna kuchititsa manyazi alendo ake. Motero Ife tidawachititsa khungu. Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga
38Ndithudi chilango chowawa chidadza pa iwo nthawi yam’mawa
39Kotero inu lawani chilango changa ndi machenjezo anga
40Ndithudi talipanga Buku la Korani kukhala losavuta kulizindikira ndi kulikumbukira. Kodi alipo ena amene adzachenjezedwa
41Ndipo, ndithudi, machenjezo adadza kwa anthu a Farawo
42Iwo adati machenjezo athu onse ndi abodza motero tidawaononga ndi chilango champhamvu yochuluka
43Kodi anthu anu osakhulupirira ndi abwino kuposa awa? Kapena inu muli ndi chitetezo mu m’mawu a Mulungu
44Kodi kapena iwo amati, “Ife ndife ambiri ndipo tidzapambana?”
45Tsopano magulu awo ali kupirikitsidwa ndipo iwo ali kuthawa
46Iyayi, koma ola lachiweruzo ndi nthawi imene iwo adalonjezedwa ndipo ola limeneli lidzakhala loopsa kwambiri
47Ndithudi anthu osakhulupirira ndi olakwa adzapsya
48Tsiku limene iwo adzaduduluzidwa pa nkhope zawo kunka ku moto, (zidzanenedwa) “Lawani ululu wa ku Moto.”
49Ndithudi tidalenga chilichonse molingana ndi muyeso wake
50Ndipo ulamuliro wathu ndi umodzi monga kuphenira kwa diso
51Ndithudi Ife tidaononga kale anthu onga inu koma kodi alipo amene anga chenjezedwe
52Ndipo zonse zimene adachita zidalembedwa
53Ndipo chilichonse chaching’ono ndi chachikulu chidalembedwa kale
54Ndithudi onse amene amalewa zoipa adzakhala m’kati mwa minda ndi mitsinje
55Ku Paradiso kufupi ndi Mfumu yamphamvu zonse
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath