53. An-Najm
1Ndi pali nyenyezi pamene ili kulowa
2M’bale wanu sadasochere kapena kuti ndi wolakwa
3Ndipo iye sayankhula zofuna zake
4Icho ndi chochita kuuzidwa kwa iye
5Iye adaphunzitsidwa ndi Iye amene ali ndi mphamvu
6Wopanda chilema chilichonse, kotero adadzuka ndi kukhala wokhazikika
7Pamene iye anali patali kwambiri mu mlengalenga
8Ndipo adasendera ndi kudza pafupi
9Ndipo adali pa mtunda wolingana kuponya mipaliro iwiri kapena kucheperapo
10Motero Iye adaulula Uthenga kwa kapolo wake kudzera mwa Gabriyele
11Mtima wake wa Mtumwi siudaname ponena zimene iye adaona
12Kodi inu mudzatsutsana naye pa zimene iye adaona
13Ndithudi iye adamuona iye pamene anali kutsika kachiwiri
14Pafupi ndi mtengo wa Sidrah
15Pafupi pake pali munda womwe ndi malo opumirako
16Ndipo chimene chimaphimba chidakuta mtengo wa Sidrah
17Maso ake sadayang’ane kumbali kapena kupyola muyeso
18Ndithudi iye adaona zizindikiro zazikulu kwambiri za Ambuye wake
19Kodi inu maganiza za Lat ndi Uzza
20Ndi Manat wachitatu wamkazi
21Kwa inu amuna ndipo kwa Iye akazi
22Ndithudi kumeneku ndiko kugawa kosalungama
23Awa ndi mayina chabe amene inu mwapeka, inu ndi atate anu, amene Mulungu sadakulamuleni ndi pang’ono pomwe. Iwo amangotsatira nkhani zakumva chabe zimene mitima yawo imafuna pamene, ndithudi, kwadza kale kwa iwo ulangizi wochokera kwa Ambuye wawo
24Kodi munthu angapeze zonse zimene amafuna
25Koma Mulungu ndiye Mwini moyo umene uli nkudza ndi moyo wakale
26Ndipo kuli angelo ambiri amene ali kumwamba amene kukhala pakati kwawo sikudzathandiza chilichonse kupatula pokhapo pamene Mulungu apereka chilolezo kwa amene Iye wamufuna ndi kukondweretsedwa naye
27Ndithudi iwo amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza, amatcha angelo ndi mayina achikazi
28Pamene iwo sadziwa chilichonse cha izo. Iwo satsatira china chilichonse koma nkhani zabodza ndipo, ndithudi, nkhani zabodza si mlowam’malo wa choonadi
29Motero mupewe wina aliyense amene salabadira chikumbutso chathu ndipo safuna china chilichonse koma moyo wa padziko lino lapansi
30Uko ndiko kuchuluka kwa nzeru zawo. Ndithudi Ambuye wako ndiye amadziwa bwino onse amene amasochera ku njira yoyenera ndipo amadziwa kwambiri iye amene amatsata njira yoyenera
31Ndipo Mulungu ndiye mwini wake wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo akhoza kulanga onse amene amachita zoipa molingana ndi ntchito zawo ndiponso kuti akhoza kulipira onse amene amachita zabwino ndi mphotho yabwino kwambiri
32Iwo amene amapewa machimo a akuluakulu ndi chigololo kupatula machimo a ang’onoang’ono, ndithudi, Ambuye wako ndi Mwini chikhululukiro. Iye amakudziwani bwino pamene amakulengani kuchokera ku dothi ndi pamene mukutidwa m’mimba mwa amayi anu. Motero musadziyeretse nokha. Al Najm 567 Iye amadziwa bwino kwambiri aliyense amene amalewa zoipa
33Kodi iwe wamuona amene amabwerera m’mbuyo
34Amene adapereka pang’ono ndipo anasiya kupereka
35Kodi iye amadziwa za zinthu zobisika kuti akhoza kuziona
36Kodi kapena iye sadauzidwe za mawu amene ali m’mabuku a Mose
37Ndiponso za Abrahamu amene adakwaniritsa malamulo
38Kuti palibe munthu amene adzasenza katundu wa mnzake
39Ndipo kuti munthu sadzapeza chilichonse kupatula chimene wachigwirira ntchito
40Ndipo kuti ntchito zake zidzaoneka
41Pamenepo iye adzalipidwa malipiro ake oyenera
42Ndipo kuti kwa Ambuye wanu ndi kumene nonse mudzapita
43Ndipo kuti Ndiye amene amawachititsa anthu kuseka ndi kuwaliritsa
44Ndipo kuti Ndiye amene amapereka imfa ndi moyo
45Ndiponso kuti Iye adalenga zinthu ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi
46Kuchokera ku madontho a umuna umene umatuluka
47Ndipo kuti kwa Iye kuli chilengedwe chachiwiri
48Ndipo kuti Ndiye amene amapereka chuma ndi chisangalalo
49Ndipo kuti Iye ndiye Ambuye wa nyenyezi yamphamvu yotchedwa Sirius
50Kuti ndiye amene adaononga anthu akale a mphamvu kwambiri a mtundu wa a Aad kale
51Ndi anthu a mtundu wa a Thamoud. Ndipo Iye sadasiye wina aliyense
52Ndi anthu a Nowa amakedzana ndithudi iwo adali osalungama ndi oswa malamulo mwamwano
53Ndipo iye adaononga mizinda yomwe idali yogonjetsedwa
54Kotero iwo adawavundikira nd chimene chidawavundikira
55Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wako zimene udzazikayikira
56Uyu ndi mchenjezi wotsatizana ndi achenjezi a makedzana
57Tsiku louka kwa akufa lili pafupi
58Palibe wina kupatula Mulungu amene akhoza kulipherera
59Kodi inu mulikudabwa pa zimene zili kulakatulidwa
60Ndipo inu muli kuseka m’malo mwakulira
61Ndi kumapitirizabe kuchita zinthu zopanda pake
62Motero gunditsani nkhope zanu pansi ndipo pembedzani Mulungu mmodzi yekha
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath