Chisilamu
kubwerera

52. Pa-Tur

1Ndi pali phiri

2Ndi pali Buku lolemekezeka

3Lili chikopa chosapinda

4Ndi pali Bait – Ul-Ma’mur (Nyumba imene ili kumwamba yolingana ndi Kaaba imene ili ku Makka ndipo imaonedwa ndi angelo pafupipafupi)

5Ndi pali denga lonyamuka

6Ndi pali nyanja yodzadzidwa ndi madzi ambiri

7Ndithudi chilango cha Ambuye wako chidzakwaniritsidwa

8Palibe wina amene angachiletse

9Pa tsiku limeneli, kumwamba kudzagwedezeka koopsa

10Ndipo mapiri adzagudubuzika osakhalanso china chake

11Kotero tsoka, patsiku limeneli kwa anthu abodza

12Amene amatangwanika ndi mabodza

13Patsikuli iwo adzatengedwa ndi kuponyedwa mwamphamvu ku moto wa ku Gahena

14Uwu ndi moto umene mumati ndi bodza

15Kodi amenewa ndi matsenga kapena simutha kuona

16Lawani kutentha kwake ndipo kaya inu mupirira kapena ayi, kwa inu ndi chimodzimodzi; inu muli kulandira malipiro a ntchito zomwe mumachita

17Ndithudi iwo amene ali olungama, adzakhala m’minda mwamtendere

18Kusangalala chifukwa cha zimene Ambuye wawo wawapatsa ndipo Ambuye wawo wawapulumutsa ku chilango cha ku Gahena

19“Idyani ndi kumwa mwachisangalalo chifukwa cha ntchito zanu zabwino zomwe mudachita.”

20Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo, yoikidwa m’mizere. Ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa amene ali ndi maso akuluakulu ndi okongola

21Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo ana awo amawatsatira m’chipembedzo, oterewa tidzawakumaniza ndi mabanja awo ndipo Ife sitidzawachotsera chilichonse cha malipiro a ntchito zawo zabwino. Munthu aliyense adzafunsidwa malinga ndi ntchito zake

22Ndipo tidzawapatsa zipatso ndi nyama zimene iwo afuna

23Kumeneko iwo adzapatsana wina ndi mnzake chikho chimene mulibe zinthu zopanda pake kapena uchimo

24Iwo adzazunguliridwa ndi kutchingidwa bwino ndi anyamata awoawo amene adzawatumizira ngati kuti iwo anali ndolo zobisika

25Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake ndi kuyankhulitsana

26Iwo adzati, “Kale ife tidali a mantha ndi mabanja athu.”

27“Koma Mulungu wationetsera chisomo chake ndipo watipulumutsa ife ku chilango cha kumoto.”

28“Ndithudi ife tinali kumupempha Iye yekha. Ndithudi Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”

29Motero pitiriza kukumbutsa ndi kulalikira. Chifukwa cha chisomo cha Ambuye wako, iwe si ndiwe munthu wonyenga kapena wamisala

30Kapena iwo amati, “Ndi Mlakatuli, ife tili kuyembekezera kuti choipa chidze pa iye.”

31Nena, “Yembekezerani! Nanenso ndili mmodzi wa oyembekezera.”

32Kodi ndi maganizo awo amene ali kumawauza izi kapena iwo ndi anthu amene amaswa malamulo mosadodoma

33Kodi kapena iwo amati, “Iye wapeka yekha uthengawu? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro.”

34Alekeni nawo abweretse mawu olingana ndi awa ngati iwo ali kunena zoona

35Kodi iwo adalengedwa popanda china chake kapena iwo ndiwo a Namalenga

36Kapena ndiwo amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro chokhazikika

37Kodi ndiwo amene amasunga chuma cha Ambuye wako? Kapena iwo ndiwo a nkhanza amene ali ndi ulamuliro wonena chilichonse chimene afuna

38Kodi kapena iwo ali ndi njira yomvetsera zomwe zinali kunenedwa? Motero mulekeni kazitape wawo kuti apereke umboni wokwanira

39Kodi kapena Iye ali ndi ana aakazi okha pamene inuyo muli ndi ana aamuna

40Kodi kapena iwe uli kuwafunsa malipiro kotero kuti iwo apanikizidwa kwambiri ndi ngongole

41Kodi kapena ali ndi zobisika ndipo amazilemba

42Kodi kapena ali kukonza chiwembu? Koma iwo amene sakhulupirira ndiwo amene ali ndi chiwembu

43Kodi kapena ali ndi mulungu wina kupatula Mulungu weniweni? Mulungu alemekezeke kuposa zimene iwo amamufanizira nazo

44Ndipo iwo akadaona gawo lina la kumwamba lili kugwa pansi ndipo iwo akadati, “Ndi mitambo youndana.”

45Motero alekeni mpaka pamene iwo akumana ndi tsiku lawo limene iwo adzakomoka ndi mantha

46Tsiku limene chiwembu sichidzawathandiza china chilichonse ndipo chithandizo sichidzaperekedwa kwa iwo

47Ndipo, ndithudi, onse amene amachita zoipa, kuli chilango china pa chilango ichi koma ambiri a iwo sadziwa

48Motero pirira podikira chiweruzo cha Ambuye wako, chifukwa ndithudi iwe uli kusamalidwa ndi Ife ndipo lemekeza Ambuye wako pamene uuka ku tulo

49Nthawi ya usiku, lemekeza ulemerero wake ndi pa nthawi yolowa nyenyezi

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath