Chisilamu
kubwerera

51. Adh-Dhaariyat

1Pali mphepo imene imamwaza fumbi

2Ndi mitambo imene ili yolemedwa ndi madzi

3Ndi zombo zimene zimayenda mosavutika ndi mwabata

4Ndipo pali iwo amene amagawa madalitso ndi chilolezo chathu

5Ndithudi chimene mwalonjezedwa, ndithudi, ndi choona

6Ndithudi chiweruzo chidzakwaniritsidwa

7Pali kumwamba kumene kuli njira zambiri

8Ndithudi inu muli ndi maganizo osiyana

9Amene abwezedwa ku icho ndiye amene wabwezedwa

10wotembereredwa akhale amene amanama

11Amene akutidwa ndi kusamvera

12Iwo amafunsa kuti, “Kodi tsiku lachiweruzo lidzadza liti?”

13Tsiku limene iwo adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku Zariat 559 moto

14Lawani chilango chanu! Ichi ndicho chimene munali kufuna kuti chidze msanga

15Ndithudi iwo amene amalewa machimo adzakhala m’minda imene ili ndi a kasupe

16Kulandira zimene Ambuye wawo awapatsa. Ndithudi kale iwo anali kuchita zinthu zabwino

17Iwo anali kugona nthawi yochepa usiku

18Ndipo m’bandakucha anali kupempha chikhululukiro

19Ndipo mu chuma chawo mudali gawo limene linali kuperekedwa kwa anthu opempha ndi osowa

20Ndipo m’dziko muli zizindikiro kwa iwo okhulupirira

21Ndi mizimu yanu kodi simungaone

22Ndipo kumwamba ndiko kuli chakudya chanu ndi zimene muli kulonjezedwa

23Ndiye, pali Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chimenechi ndi cholinga ndi choonadi chomwe inu mumayankhula

24Kodi udamva nkhani ya alendo olemekezeka a Abrahamu

25Pamene iwo adadza kwa iye, iwo adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Inu ndinu alendo kwa ine.”

26Ndipo iye atapita ku banja lake adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha

27Motero iye adadza nayo kwa iwo nati, “Kodi simufuna kudya?”

28Motero iye adayamba kuchita mantha mu mtima mwake. Ndipo iwo adati, “Usaope.” Ndipo iwo adamuuza nkhani yabwino yakubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe adzakhala wanzeru kwambiri

29Ndipo mkazi wake adadza modzichepetsa ndipo adamenya pa mphumi pake nati, “Nkhalamba yaikazi yosaberekapo!”

30Iwo adati, “Ngakhale ndi choncho, Ambuye wako wayankhula. Iye ndi wodzala ndi luntha ndiponso nzeru.”

31Iye adati, “Kodi inu Atumwi uthenga wanu ndi wotani?”

32Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu ochimwa.”

33“Kuti tigwetse pa iwo miyala yamakande.”

34“Idakonzedwa ndi Ambuye wako kudza kwa anthu oswa malamulo.”

35Ndipo Ife tidatulutsa anthu okhulupirira amene adali momwemo

36Koma sitidapezemo mabanja a Chisilamu kupatula banja limodzi lokha basi

37Ndipo Ife tidasiyamo chizindikiro kwa iwo amene amaopa chilango chowawa

38Ndi mwa Mose. Pamene tidamutumiza kwa Farawo ndi zizindikiro zooneka

39Koma Farawo adakana pamodzi ndi mafumu ake nati, “Ndiwe munthu wamatsenga kapena munthu wa misala.”

40Motero tidamugwira pamodzi ndi gulu la asirikali ake ndi kuwamiza onse m’nyanja pamene iye ndiye adali wolakwa

41Ndipo mwa a Aad pamene tidawatumizira mphepo yoononga

42Imene sidasiye chilichonse chimene idalimbana nacho kupatula kuchiononga ndi kuchisandutsa phulusa

43Ndipo mwa anthu a Thamoud. Pamene adauzidwa kuti, “Basangalalani kanthawi kochepa.”

44Koma iwo adaphwanya lamulo la Ambuye wawo mwamwano, kotero mabingu adawaononga iwo ali kuona

45Kotero iwo adalibe mphamvu zodzuka kapena zodzitetezera

46Ndi anthu a Nowa iwo asanadze. Ndithudi iwo adali anthu oswa malamulo

47Ife tidakonza kumwamba mwamphamvu ndiponso mwaluso. Ndipo, ndithudi, ndife amene timapanga kukula kwa mlengalenga

48Ndipo dziko, tidamwaza. Kodi ndife omwaza bwino bwanji

49Ndipo zonse zimene tidalenga tidazilenga ziwiriziwiri kuti mukhoza kukumbukira

50Kotero thawirani kwa Mulungu. Ndithudi Ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye

51Ndipo musapange fano kukhala lopembedzedwa pamodzi ndi Mulungu. Ndithudi ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye

52Chimodzimodzi palibe Mtumwi amene adadza kwa anthu amene sadamunenere mawu ofanana monga akuti: “Wamatsenga kapena munthu wopenga!”

53Kodi uwu ndi mwambo umene akhala ali kusiyirana wina ndi mnzake? Iyayi, iwo ndi anthu amene ali kuswa malamulo mopyola muyeso

54Kotero uwaleke chifukwa iwe ulibe mlandu

55Ndipo kumbutsa chifukwa chikumbutso chimathandiza anthu okhulupirira

56Ndipo Ine ndidalenga majini ndi anthu kuti azindipembedza Ine

57Ine sindiwapempha chakudya ndipo sindiwafunsa kuti azindidyetsa Ine

58Ndithudi ndi Mulungu yekha amene amapereka chakudya chonse, Mwini mphamvu zonse ndi wolimba kwambiri

59Ndithudi anthu onse olakwa adzalandira gawo longa limene anzawo olakwa akale adalandira, kotero asandifunse Ine kuchita mofulumira

60Kotero tsoka kwa onse osakhulupirira kuchokera ku tsiku lomwe iwo alonjezedwa

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath