50. Qaaf
1Qaf. Pali Buku lolemekezeka la Korani
2Koma iwo alikudabwa kuti kwa iwo kwadza mchenjezi wochokera pakati pawo. Motero anthu osakhulupirira amati, “chimenechi ndi chinthu chachilendo!”
3“Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi, kubwerera kotero ndi kosatheka.”
4Ife timadziwa onse amene adamezedwa ndi nthaka ndipo Ife tili ndi Buku la mbiri yawo
5Iyayi, koma iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo. Kotero iwo, tsopano, asokonezeka
6Kodi iwo sayang’ana kumwamba ndi kuona mmene tidakukonzera ndi kukukongoletsera ndi kuona kuti kulibe mipata
7Ndipo dziko lapansi Ife talipanga kukhala losalala ndi kuikamo mapiri ndipo tidameretsa mu dzikolo mbewu zokongola zosiyanasiyana
8Choonetsa ndi chikumbutso kwa kapolo aliyense amene amatembenukira nthawi zonse kwa Mulungu
9Ndipo timatumiza kuchokera ku mitambo mvula yodalitsika ndipo timameretsa m’minda mbewu zimene zimakololedwa
10Ndi mitengo italiitali ya tende yolemedwa ndi zipatso
11Chakudya cha akapolo. Ndipo Ife timapereka moyo kunthaka imene idali yakufa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa
12Adakana iwo asanadze, anthu a Nowa ndi iwo amene anali kukhala ku Ar-rass ndi Thamoud
13Anthu a mtundu wa Aad ndi Farawo ndi abale ake a Loti
14Ndi iwo amene anali kukhala m’nkhalango ndi anthu a ku Tuba, aliyense wa iwo adakana Atumwi ndipo chenjezo langa lidakwaniritsidwa
15Kodi Ife tidatopa ndi chilengedwe choyamba? Iyayi. Iwo asokonezeka ndi nkhani zokhudza chilengedwe chatsopano
16Ndithudi Ife tidamulenga munthu ndipo timadziwa zimene mtima wake umamuuza. Ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wa moyo wake
17Pamene asungi awiri amulandira, wina atakhala kudzanja lamanja ndi wina ku dzanja lamanzere
18Palibe mawu amene amayankhula amene samveka kwa Msungi wa tcheru
19Ndipo ululu wa imfa udzadza pa iye mwachoonadi. Ichi ndicho chimene iwe unali kuyesetsa kuchithawa
20Ndipo lipenga lidzaombedwa ndipo limeneli lidzakhala tsiku loopseza
21Ndipo mzimu uliwonse udzadza pamodzi ndi mngelo wouyendetsa ndi mngelo wochitira umboni
22(Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochimwa) kuti, “Ndithudi inu simudafune kuchenjezedwa za chimenechi ndipotsopano Ifetavundukulachimenechimakuphimbani. Ndipo lero maso anu ali kuona zenizeni.”
23Ndipo mnzake adzati, “Uwu ndi umboni umene ndili nawo.”
24“Ponyani ku Gahena aliyense wosathokoza ndiponso wosamvera.”
25“Woletsa kuchita ntchito zabwino, woswa malamulo ndiponso wokayika.”
26“Iye amene anali kukhazikitsa milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, motero mponyeni ku chilango chowawa.”
27Mnzake adzanena kuti, “Ambuye wathu! Ine sindidamuuze kuti aziswa malamulo ayi koma iye adadzisocheretsa yekha.”
28Mulungu adzati, “Musakangane pamaso panga. Ine ndidakutumizirani chenjezo lokwanira.”
29Chilango sichisintha ayi ndipo Ine sindionetsa chinyengo kwa akapolo anga
30Patsiku limene Ife tidzaifunsa Gahena kuti, “Kodi mwadzadza?” Ndipo iyo idzati, “Kodi akanalipobe ena?”
31Ndipo Paradiso idzabweretsedwa kufupi kwa anthu olungama
32Ichi ndicho chimene mudalonjezedwa ndipo ndi mphotho kwa iye amene amadzipereka kwa Mulungu nthawi zonse nasunga malamulo ake
33Ndiponso kwa iye amene amaopa Mwini chisoni chosatha wosaoneka ndipo amadza kwa Iye ndi mtima wodzichepetsa
34Lowani m’menemo mwamtendere ndi mosaopa ayi. Ili ndi tsiku la moyo wosatha
35M’menemo mudzakhala chilichonse chimene iwo adzafuna ndipo Ife tili ndi zinthu zambiri
36Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaiononga iwo asanabadwe amene adali ndi mphamvu zoposa iwo ndipo iwo adafuna chitetezo padziko? Kodi iwo anali ndi kwina kothawira
37Ndithudi muli chikumbutso mu zimenezi kwa iye amene ali ndi mtima kapena amatchera khutu pamene achenjezedwa
38Ndithudi Ife tidalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi ndipo sitidatope ayi
39Kotero pirira pa zonse zimene amanena ndipo lemekeza Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe
40Ndipo mulemekeze Iye usiku ndipo utatha kupemphera
41Ndipo udzamve patsiku limene woitana adzaitana kuchokera pafupi
42Tsiku limene iwo adzamva kulira kwa mfuwu woona. Limeneli lidzakhala tsiku louka kwa akufa
43Ndithudi ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo ndi kwa Ife kumene zonse zidzabwerera
44Tsiku limene dziko lidzang’ambika ndipo iwo adzatuluka mofulumira. Kumeneko ndiko kudzakhala kusonkhanitsidwa pamodzi
45Ife timadziwa zonse zimene amanena ndipo iwe si ndiwe wankhanza ayi. Koma muchenjeze ndi Korani kwa aliyense amene aopa chilango changa
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath