Chisilamu
kubwerera

49. Al-Hujuraat

1Oh inu anthu okhulupirira! Musadzikweze pamaso pa Mulungu ndi pa Mthenga wake, koma opani Mulungu chifukwa Iye ndiye amene amamva ndi kudziwa chinthu china chilichonse

2Oh inu anthu okhulupirira! Musakweze mawu anu kuposa a Mtumwi ndipo musayankhule ndi mawu okweza kwa iye monga momwe mumachitira mukamayankhulana nokhanokhanu chifukwa ntchito zanu zingasanduke zopanda pake pamene inu simuli kudziwa

3Ndithudi iwo amene amayankhula motsitsa pamaso pa Mtumwi wa Mulungu ndiwo amene Mulungu wayesa mitima yawo kuti ndi yabwino, ndipo iwo adzalandira chikhululukiro ndi mphotho yaikulu

4Ndithudi iwo amene amafuulira iwe kunja kwa zipinda, onse alibe nzeru

5Iwo akadapirira mpaka pamene iwe udza kwa iwo, ndithudi, zikadakhala bwino ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha

6oh inu anthu okhulupirira! Ngati munthu wochita zoipa adza kwa inu ndi nkhani, ifufuzeni poyamba chifukwa mwina mukhoza kupweteka anthu mosadziwa ndi kuyamba kumva chisoni pambuyo pake chifukwa cha zimene mwachita

7Ndipo dziwani kuti pakati panu pali Mtumwi wa Mulungu ndipo iye akamachita zimene Al Hujurat 553 mufuna, ndithudi, inu mukadavutika kwambiri. Koma Mulungu wakusungitsani inu chipembedzo chake ndipo wachipanga icho kukhala chokongola m’mitima mwanu, ndi kupanga kusakhulupirira kukhala chinthu choipa ndiponso kuswa malamulo ndi kusamvera. Awa ndiwo amene amatsatira njira yoyenera

8Chisomo ndi chifundo chochokera kwa Mulungu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse ndipo ndi wanzeru kwambiri

9Ngati magulu awiri ochokera kwa anthu okhulupirira amenyana, khazikitsa mtendere pakati pawo. Koma ngati gulu lina liswa malamulo mopyola muyeso, nonse menyanani nalo gulu lotero mpaka pamene limvera lamulo la Mulungu. Ndipo ngati ilo limvera, khazikitsani mtendere pakati pawo mwachilungamo. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amachita chilungamo

10Onse okhulupirira ali pachibale. Kotero khazikitsani mtendere ndi kukhululukirana ndi abale anu ndipo opani Mulungu kuti mulandire chisomo chake

11oh inu anthu okhulupirira! Musalole kuti anthu ena aziseka anzawo. Mwina kungatheke kuti gulu limene lisekedwa likhoza kukhala labwino kuposa limene likuseka. Ndiponso musalole akazi kuti aseke anzawo chifukwa mwina kungatheke kuti osekedwawo akhoza kukhala abwino kuposa osekawo. Musafunirane zifukwa wina ndi mnzake kapena kuitanana ndi mayina a mchedzera. Mayina a mchedzera ndi oipa kwa amene wakhulupirira. Ndipo aliyense amene sasiya kuitana anzake ndi maina a mchedzera , ameneyo ndiye wopanda chilungamo

12oh inu anthu akhulupirira! Pewani kukaikirana chifukwa kukhala ndi chikayiko ndi tchimo. Ndipo musachite ukazitape pakati panu kapena amiseche. Kodi wina wa inu angakondwere kudya mnofu wa mnzake amene ndi wakufa? Kodi koma inu mumakana kudya.. Kotero opani Mulungu. Ndithudi Mulungu amabwezera chisoni chifukwa ndiye Mwini Chisoni Chosatha

13oh anthu inu inu! Ndithudi Ife tidakulengani inu mwamuna ndi mkazi ndipo tidakupangani inu kukhala mitundu ya anthu ndi mabanja muzidziwana, Ndithudi wopambana kwambiri pakati panu ndiponso pamaso pa Mulungu ndi amene amaopa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wodziwa chinthu china chilichonse

14Anthu okhala m’midzi amati, “Ife timakhulupirira.” Nena, “Inu mulibe chikhulupiriro. Koma nenani kuti, “Tadzipereka kwa Mulungu chifukwa chikhulupiriro sichidakhazikike m’mitima mwanu. Ndipo ngati inu mumvera Mulungu ndi Mtumwi wake, Iye sadzachepetsa ntchito zanu, ngakhale m’pang’ono pomwe. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha.”

15okhulupirira ndi okhawo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo sakayika ngakhale ndi pang’ono pomwe. Iwo amadzipereka kwathunthu pamodzi ndi chuma chawo m’njira ya Mulungu. Ndipo iwo ndiwo olungama

16Nena, “Kodi inu mungamuphunzitse Mulungu za chipembedzo chanu? Pamene Mulungu amadziwa chilichonse chili mlengalenga ndi padziko lapansi. Ndipo Mulungundi wodziwa chilichonse

17Iwo amaganiza kuti ali kukuchitira iwe chisoni pamene alowa Chisilamu. Nena, “Inu simuli kundichitira ine chisoni polowa chisilamu. Iyayi, koma ndi Mulungu amene wakuchitirani inu chisoni pokulangizani njira yoyenera ngati inu, muli anthu olungama.”

18Ndithudi Mulungu amadziwa zobisika zonse zimene zili mlengalenga ndi padziko lapansi ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath