Chisilamu
kubwerera

48. Al-Fath

1Ndithudi Ife takupambanitsa iwe,kupambana kwenikweni

2Kuti Mulungu akukhululukire machimo ako akale ndi am’tsogolo omwe, ndi kumaliza ubwino wake pa iwe ndi kukutsogolera ku njira yoyenera

3Ndikuti Mulungu athe kukuthandiza ndi chithandizo chokwanira

4Ndiye amene adatumiza chisomo m’mitima mwa anthu okhulupirira kuti chikhulupiriro chawo chikhoza kukhala chokhazikika za Mulungu ndi zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha

5Kuti akhoza kulowetsa amuna ndi akazi okhulupirira ku minda imene pansi pake pali mitsinje yamadzi oyenda kuti akhale komweko mpaka kalekale ndi kuwakhululukira machimo awo ndipo pamaso pa Mulungu, ndiko kupambana kwenikweni kumeneku

6Ndipo akhoza kulanga anthu a chinyengo, aamuna ndi aakazi ndi anthu opembedza mafano, amuna ndi akazi amene amaganiza zoipa za Mulungu. Kwa iwo kudzadza mavuto ndipo mkwiyo wa Mulungu uli pa iwo. Iye wawatemberera iwo ndipo wakonzekera Gahena omwe ndi malo oipa kukhalako

7Mulungu zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi. Mulungu ndi wamphamvu ndi wa nzeru

8Ndithudi takutumiza iwe ngati Mboni, ngati Wolalikira uthenga wabwino ndiponso ngati Mchenjezi

9Ndi cholinga chakuti inu anthu mukhoza kukhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndi kuti mumuthandize ndi kumulemekeza iye ndipo kuti muzilemekeza Mulungu m’mawa ndi madzulo

10Ndithudi onse amene amalumbira kuti ali pambuyo pako, iwo amalumbira kuti ali pambuyo pa Mulungu. Ndipo dzanja la Mulungu ndi loposa manja awo. Ndipo aliyense amene aphwanya lonjezo lake, Iye akungodzipondereza yekha ndipo aliyense amene akwaniritsa lonjezo limene adachita ndi Mulungu, Iye adzamulipira iye mphotho yopambana

11Maarabu okhala m’chipululu amene adatsalira m’mbuyo adzati kwa iwe, “Ife tidatangwanika ndi chuma ndi mabanja athu, motero tipemphere chikhululukiro.” Iwo amangonena ndi milomo yawo zimene m’mitima mwawo mulibe. Nena, “Kodi ndani angakuyankhulireni inu kwa Mulungu ngati Iye atafuna kukuonongani kapena atafuna kuti akuchitireni zabwino? Iyayi, Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita.”

12Iyayi! Inu munali kuganiza kuti Mtumwi pamodzi ndi onse okhulupirira sadzabwerera ku mabanja awo ndipo zimenezo zinali zokusangalatsani inu ndipo inu munali kuganiza maganizo oipa ndipo inu munali anthu opanda pake opita ku chionongeko

13Ndipo aliyense amene sakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, Ife tawakonzera anthu osakhulupirira moto woyaka

14wa Mulungu ndi Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi. Iye amakhululukirira amene wamufuna ndipo amalanga aliyense amene wamufuna. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira nthawi zonse ndi Mwini chisoni chosatha

15Iwo amene adatsala m’mbuyo adzati, pamene adzaona inu muli kukonzeka kukatenga katundu amene mwapeza pa nkhondo, “Tiloleni kuti tipite nanu.” Iwo afuna kusintha mawu a Mulungu. Nena, “Ndikosatheka! Inu simudzapita nafe. Mulungu ananena kale za inu.” Ndipo iwo adzati, “Iyayi! Inu muli kutichitira ife nsanje.” “Iyayi! Koma iwo sazindikira koma pang’ono pokha.”

16Nena kwa iwo amene amakhala m’chipululu ndipo adakhalira m’mbuyo kuti, “Inu mudzaitanidwa, kuti mumenyane ndi anthu amphamvu kwambiri ndipo inu mudzamenyana nawo mpaka pamene adzagonja. Ndipo ngati inu mumvera, Mulungu adzakulipirani mphotho ya mtengo wapatali ndipo ngati inu muthawa, Iye adzakulangani inu ndi chilango chowawa.”

17Palibe cholakwa kapena mlandu kwa wakhungu, kapena cholakwa kapena mlandu kwa wopunduka ndipo palibe cholakwa kapena mlandu kwa wodwala ngati iwo sapita nawo. Aliyense amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake, Mulungu adzamulandira ku minda imene ili ndi mitsinje yoyenda madzi pansi pake ndipo aliyense amene athawa, Mulungu adzamulanga ndi chilango chowawa

18Ndithudi Mulungu adasangalala ndi anthu okhulupirira pamene iwo adakulonjeza patsinde pa mtengo kuti adzakhala ndi iwe ndipo Iye adadziwa zimene zidali m’mitima mwawo. Ndipo Iye adatumiza madalitso kwa iwo ndipo adawalipirira mwamsanga mphotho yopambana

19Ndipo iwo adzalanda katundu wambiri. Ndipo Mulungu ndi Wamphamvu ndi Waluntha

20Mulungu wakulonjeza katundu wambiri amene udzalandira ndipo wakupatsiratu, ndipo Iye wamanga manja ya anthu kuti asakukhudze, kuti chikhale chizindikiro kwa anthu okhulupirira ndipo kuti Iye akutsogolere ku njira yoyenera

21Ndi zina zomwe iwe siudazipeze ndithudi,Mulungu wazizungulira. Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

22Ngati anthu osakhulupirira amenyana nanu, ndithudi, iwo adzathawa, ndipo iwo sadzapeza wina aliyense wowateteza kapena kuwathandiza

23Amenewa ndiwo machitidwe a Mulungu kuyambira kalekale. Ndipo inu simudzapeza chosintha m’machitidwe a Mulungu

24Ndipo ndiye amene adamanga manja awo kuti asakukhudzeni inu ndipo manja anu kuti asawakhudze iwo m’kati mwa Makka pamene Iye adakupambanitsani inu. Ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita

25Iwo ndiwo amene sadakhulupirire ndipo adakutchingani kuti musalowe mu Mzikiti Wolemekezeka ndi kukuletsani kuti nyama za nsembe zisakafike pa malo operekerapo nsembe. Koma pakadakhala kuti panalibe anthu aamuna okhulupirira ndi aakazi okhulupirira, amene simuwadziwa, inu mukadawapondereza kotero kuti china chake choipa chikadadza pa inu chifukwa cha iwo, kuti Mulungu aonetse chisomo chake kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma iwo akadapatukana wina ndi mnzake, Ife ndithudi tikadalanga ndi chilango choopsa onse amene sadakhulupirire amene anali pakati pawo

26Pamene iwo osakhulupirira adasunga chidani m’mitima mwawo, chidani cha nthawi ya chikunja, ndipo Mulungu adatumiza chisomo chake kwa Mtumwi wake ndi kwa anthu okhulupirira. Ndipo adawachititsa iwo kukhala omvera malamulo odziletsa ndipo adakhazikitsa bata kukhala pa iwo chifukwa adali oyenera kulilandira batalo. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse

27Ndithudi Mulungu adzakwaniritsa masomphenya a Mtumwi wake. Ndithudi inu mudzalowa mu Mzikiti Wolemekezeka, ngati Mulungu afuna mopanda vuto ndipo ena adzameta mitu yawo ndiponso ena adzapungula tsitsi lawo ndipo mudzakhala opanda mantha. Iye adadziwa zimene inu simudadziwe ndipo adapereka moonjezera pa zimenezi, kupambana kwa msanga

28Ndiye amene adatumiza Mtumwi wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choonadi. Ndipo Iye wachipanga icho kuti chikhale chopambana zipembedzo zina zonse. Ndipo Mulungu ndi wokwana kukhala mboni

29Muhammad ndi Mtumwi wa Mulungu ndipo onse amene amamutsatira iye amakhala olimbika polimbana ndi anthu osakhulupirira koma amachitirana chisoni wokhaokha. Inu mumawaona ali nkupembedza pa mawondo awo ndi kugwetsa mphumi zawo kufunafuna chisomo chochokera kwa Mulungu ndi chisangalalo chake. Pamphumi pawo pali zizindikiro zimene zimadza chifukwa chakugunditsa mphumi zawo pansi. Awa ndi maonekedwe awo amene ali m’Chipangano Chakale. Koma maonekedwe awo amene ali mu Chipangano Chatsopano ali monga momwembewuimatulutsiransongayakendikuikhwimitsa. Ndipo iyo imalimba ndi kukhala yoimirira modabwitsa ndi kusangalatsa amene adaibzala. Kuti Iye akwiyitse osakhulupirira ndi izo. Mulungu walonjeza chikhululukiro ndi mphotho yaikulu kwa anthu okhulupirira ndiponso ochita ntchito zabwino

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath