47. Muhammad
1Iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu, Iye adzasandutsa ntchito zawo kukhala zopanda pake
2Koma iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, ndipo amakhulupirira mu chivumbulutso chimene chatumizidwa kwa Muhammad, chifukwa icho ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wawo, Iye adzawachotsera zoipa ndi kulongosola machitidwe awo
3Ichi ndi chifukwa chakuti onse amene sakhulupirira amatsatira zabodza pamene iwo amene amakhulupirira amatsatira choonadi chochokera kwa Ambuye wawo. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaonetsera zitsanzo zake kwa anthu
4Motero pamene inu mukumana ndi anthu osakhulupirira pa nkhondo, thyolani makosi awo, mpaka pamene mukupha ndi kuvulaza ambiri ndipo muwagwire kukhala akaidi ndipo pambuyo pake mukhoza kuwamasula powaonetsa chisoni kapena akhale ngati chigwiriro mpaka pamene nkhondo itatha. Motero inu mwalamulidwa. Koma chikadakhala chifuniro cha Mulungu, ndithudi, Iye Mwini wake akadawapatsa chilango chowayenera. Koma Iye wafuna kuti inu mumenyane nawo ndi cholinga chokuyesani wina ndi mnzake. Koma iwo amene aphedwa m’njira ya Mulungu, Iye sadzalola kuti ntchito zawo zipite pachabe
5Iye adzawatsogolera ndi kulemekeza malo awo
6Iye adzawalowetsa ku Paradiso kumene adawalonjeza kale
7Oh inu anthu okhulupirira! Ngati inu muthandiza m’ntchito za Mulungu, Iye adzakuthandizani inu ndipo adzakulimbikitsani
8Koma iwo amene sakhulupirira, kwa iwo kuli chionongeko ndipo Mulungu adzapanga kuti ntchito zawo zonse zikhale zopanda phindu
9Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amadana ndi chivumbulutso cha Mulungu, ndipo Iye wapanga ntchito zawo kukhala zopanda pake
10Kodi iwo sadayende padziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira iwo amene adalipo kale? Mulungu adaponya chionongeko pa iwo ndipo onse osakhulupirira adzaona mavuto a mtundu womwewo
11Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amakhulupirira pamene anthu osakhulupirira alibe wowateteza
12Ndithudi Mulungu adzalowetsa ku minda imene pansi pake pamayenda mitsinje yamadzi onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Pamene onseamenesakhulupirirandipoamadzisangalatsandikudya ngati momwe zimadyera nyama kumoto ndiko kudzakhala malo awo okhala
13Ndi mizinda yambiri imene idali ndi mphamvu zoposa Mzinda umene wakupirikitsa iwe imene Ife tidaiononga. Ndipo padalibe wina wowathandiza
14Kodi iye amene watsogozedwa bwino ndi Ambuye wake ndi wofanana ndi iwo amene ntchito zawo zoipa zimaoneka ngati zabwino ndipo amatsatira zilakolako zawo zopanda pake
15Mwaonekedwe amunda umene iwo amene amalewa zoipa alonjezedwa ndi akuti m’menemo muli mitsinje yamadzi amene sakuphwa ndi mitsinje yamkaka umene siusintha kukoma kwake, ndipo mitsinje ya vinyo ndi mitsinje ya uchi wabwino. Imo muli zipatso zosiyanasiyanandichikhulupirirochochokerakwaAmbuye wawo. Kodi awa ali ngati iwo amene adzakhala kumoto mpaka kalekale ndipo amapatsidwa madzi ogaduka amene amaboola m’matumbo
16Ndipo pakati pawo pali iwo amene amamva zimene iwe umanena, mpaka pamene akusiya iwe, iwo amati kwa amene adapatsidwa nzeru, “Kodi ndi chiyani chimene wanena posachedwapa?” Awa ndiwo amene mitima yawo yatsekedwa ndi Mulungu ndipo amatsatira zilakolako zopanda pake
17Pamene iwo amene amatsatira njira yoyenera, Iye amawatsogolera ndi kuwonjezera chikhulupiriro chawo
18Kodi iwo akudikira china kuposa Ola kuti lidze kwa iwo mwadzidzidzi? Koma zizindikiro zina zadza kale, ndipo chitadza pa iwo, kodi iwo adzapindula chiyani ndi chikumbutso
19Motero dziwani kuti kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni ndipo pempha chikhululukiro chako ndi cha amuna ndi akazi amene amakhulupirira. Ndipo Mulungu amadziwa mmene inu mumayendera ndi mmene mumakhalira m’nyumba zanu
20Iwo amene amakhulupirira amati, “Kodi bwanji Mutu wina siudavumbulutsidwe?” Koma pamene mutu wotsimikiza uvumbulutsidwa ndipo kumenya nkhondo kulamulidwa mmenemo iwe udzaona iwo amene m’mitima mwawo muli matenda ali kukuyang’ana iwe ngati munthu amene ali kukomoka pamene imfa ili kudza kwa iye. Koma zinali bwino kwa iwo
21Kumvera ndi mau abwino (zikadakhala zinthu zabwino). Ndipo pamene nkhani iweruzidwa, ndipo iwo akadadzipereka mwachoonadi kwa Mulungu, ndithudi, zikadakhala zabwino kwa iwo
22Kodi ngati inu mukadapatsidwa udindo wolamulira, mukadachita zinthu zoipa padziko ndi kuphwanya ubale wanu ndi anthu a mtundu wanu
23Amenewa ndiwo amene Mulungu wawatemberera ndipo Iye wawapanga iwo kukhala osamva ndi akhungu
24Kodi iwo sangaganize za uthenga wa m’Korani? Kodi kapena mitima yawo ndi yotsekedwa
25Ndithudi iwo amene amabwerera m’mbuyo ndi kukhalanso osakhulupirira pamene atalandira kale ulangizi, amatsogozedwa ndi Satana amene amawanamiza ndi zinthu zopanda pake
26Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amanena kwa iwo amene amadana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa kuti, “Ife tidzakumverani mu zina za nkhani zimenezi.” Koma Mulungu amadziwa zinsinsi zawo zonse
27Kodi iwo adzachita chiyani pamene angelo adzalanda miyoyo yawo ndi kuwamenya pa nkhope ndi m’misana yawo
28Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amatsatira zinthu zimene zimakwiyitsa Mulungu ndipo amadana ndi zimene zimamukondweretsa Iye. Kotero Mulungu adasandutsa ntchito zawo kukhala zinthu zopanda pake
29Kodi iwo amene m’mitima mwawo muli matenda amaganiza kuti Mulungu sadzaulula zoipa zawo zonse
30Ife tikadafuna tikadakuonetsa iwe ndipo iwe ukadawadziwa chifukwa cha zizindikiro zawo ndipo, ndithudi, udzawadziwa chifukwa cha mayankhulidwe awo. Mulungu amadziwa ntchito zanu
31Ndithudi Ife tidzakuyesani mpaka pamene tiyesa onse amene amalimbikira kwambiri ndi iwo amene opirira ndipo Ife tidzayesa ntchito zanu
32Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anthu kutsata njira ya Mulungu ndipo amatsutsana ndi Mtumwi pamene atalandira kale langizo loyenera, iwo sangathe kugonjetsa Mulungu mwanjira ina iliyonse. Koma Iye adzafafaniza ntchito zawo zonse ndi kuzisandutsa kukhala zopanda pake
33Oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake ndipo musasandutse ntchito zanu kukhala zopanda pake
34Ndithudi onse amene sakhulupirira ndipo amaletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu, ndipo amafa ali osakhulupirira Mulungu sadzawakhululukira
35Motero inu musafoke ndipo musafunse kuti kukhale mtendere pamene muli kupambana. Mulungu ali ndi inu ndipo Iye sadzapungula mphotho ya ntchito zanu zabwino
36Moyo wa pa dziko lino ndi masewera enieni ndiponso kotayira nthawi koma ngati inu mukhulupirira ndi kulewa machimo, Iye adzakulipirani inu ndipo sadzakufunsani za katundu amene muli naye
37Ngati Iye akadakufunsani za katundu wanu ndi kukuumirizani, ndithudi, inu mukadachita umbombo ndipo Iye adzaulula zinsinsi zanu zonse
38Taonani! Inu ndinu amene mwaitanidwa kupereka m’njira ya Mulungu koma pakati panu pali anthu omwe ndi mbombo. Ndipo aliyense amene achita umbombo amadzimana yekha. Mulungu sasowa kanthu pamene inu ndinu osauka. Ndipo ngati inu mubwerera m’mbuyo Iye adzaika m’malo mwanu anthu ena ndipo sadzakhala olingana ndi inu
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath