Chisilamu
kubwerera

45. Al-Jaathiya

1Ha Mim

2Chivumbulutso cha Buku ndi chochokera kwa Mulungu, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru

3Ndithudi kumwamba ndi dziko lapansi kuli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

4M’chilengedwe chanu nyama zimapezeka paliponse pa dziko lapansi ndipo ndi zizindikiro kwa iwo amene ali okhulupirira kwenikweni

5Ndi m’kasinthidwe ka usiku ndi usana ndi m’chakudya chimene amatumiza kuchokera ku mitambo ndipo amapereka moyo ku nthaka imene idali yakufa ndipo m’kasinthidwe ka mphepo, muli zizindikiro kwa anthu ozindikira

6Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Mulungu chimene tili kulakatula kwa iwe mwachoonadi. Nanga ndi uthenga uti wa Mulungu ndi chivumbulutso chake chiti chomwe iwo akhoza kukhulupirira

7Tsoka kwa wochimwa aliyense wabodza

8Amene amamva mawu a Mulungu amene ali kunenedwa kwa iye ndipo amapitirizabe kunyada ngati iye sanamve. Motero muuze iye za chilango chowawa

9Ndipo pamene iye akamva mawu a Mulungu, amawasandutsa kukhala masewera. Ndipo kwa otere kudzakhala chilango chochititsa manyazi

10Kutsogolo kwawo kuli Gahena, ndipo sadzapeza phindu lina lililonse pa ntchito zawo kapenakwaiwoameneadawasandutsakukhalawowasamala poonjezera pa Mulungu. Ndipo iwo adzalandira chilango chowawa

11Ichi ndi chilangizo choona. Ndipo iwo amene amakana zizindikiro za Ambuye wawo, adzalandira chilango chapadera chowawa

12Ndi Mulungu amene adachepetsa mphamvu ya nyanja kuti masitima aziyenda mwaulamuliro wake ndipo kuti inu mukhoza kufuna chisomo chake kuti muzimuthokoza

13Ndipo Iye adachepetsa mphamvu ya chinthu chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi. Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amaganiza mofatsa

14Auze iwo amene amakhulupirira kuti akhululukire iwo amene sakhulupirira m’masiku a Mulungu kuti Iye akhoza kulipira anthu chimene amachita

15Aliyense amene amachita zabwino amachitira mzimu wake ndipo aliyense amene amachita zoipa adzilakwira yekha. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu

16Ndithudi Ife tidawapatsa ana a Israyeli Buku ndi luntha lozindikira mawu a Mulungu ndi Utumwi ndipo tidawapatsa zinthu zokoma ndipo tidawakonda iwo kuposa mitundu ina yonse

17Ndipo Ife tidawapatsa zizindikiro zooneka za chipembedzo. Ndipo iwo adayamba mipatuko pamene nzeru zidaperekedwa kwa iwo chifukwa cha njiru pakati pawo. Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku lachiweruzo pa nkhani zimene anali kutsutsana

18Ndipo iwe takuika pa njira yoyenera. Motero tsatira yoyenerayo ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene sadziwa chilichonse

19Ndithudi iwo sangakuthandize chilichonse ku mkwiyo wa Mulungu. Ndi anthu oipa okha okha omwe amakhala ngati atetezi a wina ndi mnzake koma Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amalewa zoipa

20Uwu ndi umboni womveka kwa anthu ndi langizo ndi chisomo kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro chokhazikika

21Kodi anthu amene amachita zoipa amaganiza kuti Ife tidzawasamala monga mmene tidzasamalire anthu amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino zofanana ndi moyo wawo ndiponso imfa yawo? Iwo amaweruza molakwa

22Ndipo Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi kuti mzimu uliwonse ukhoza kupeza dipo lake molingana ndi zimene udachita ndipo palibe amene adzaponderezedwa

23Kodi wamuona iye amene amasandutsa zilakolako zake kukhala mulungu wake? Mulungu wamusocheretsa iye ndipo wakhazikitsa chophimba m’makutu mwake ndi mu mtima mwake. Ndipo waika chophimba m’maso mwake? Kodi ndani amene akhoza kumutsogolera iye kupatula Mulungu? Kodi tsopano simudzakumbukira

24Ndipo iwo amati, “Kulibe china chilichonse kupatula moyo wathu wa pa dziko lapansi. Ife timakhala ndi moyo ndipo timafa ndipo palibe chimene chimationonga ife koma nthawi yokha ndiyo.” Ndipo iwo sadziwa chilichonse cha izo koma amangonena zongoganiza

25Ndipo pamene chivumbulutso chathu chomveka chimanenedwa kwa iwo, mtsutso wawo siukhala wina koma kuti, “Bweretsa makolo athu akale ngati zimene ukunena ndi zoonadi.”

26Nena: “Mulungu amakupatsani inu moyo, amakuphani ndipo Iye adzakusonkhanitsani pa tsiku la kuuka kwa akufa limene lilibe chikayiko. Koma ambiri sadziwa zimenezi.”

27Mulungu! Wake ndi ufumu wakumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo patsiku limene ola lidzadza, onse amene amanenazinthuzabodzaadzatayachilichonse

28Ndipoiwe udzaona mtundu uliwonse utagwada pansi ndipo mtundu uliwonse udzaitanidwa monga mmene zidalembedwera. Lero mudzalipidwa molingana ndi zimene mudachita

29Buku lathuli lili kunena za inu mwachilungamo. Ndithudi timalemba zonse zimene mumachita

30Ndipo iwo amene adakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, Ambuye wawo adzawalowetsa m’chisomo chake. Kumeneku ndiko kupambana kwenikweni

31Koma iwo amene sadakhulupirire adzauzidwa kuti, “Kodi chivumbulutso changa sichidalakatulidwe kwa inu? Koma inu munali onyada ndipo munali anthu ochita zoipa.”

32Ndipo pamene zidanenedwa kuti, “Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo palibe zokayikitsa za kudza kwa Ola”, inu mudati, “Ife sitidziwa kuti Ola ndi chiyani ndipo ife sitiliganiza kupatula kuti ndi maganizo opanda pake ndipo ife sitilikhulupirira ayi.”

33Ndipozoipazonsezimeneadachitazidaonekerapoyera kwa iwo ndipo zonse zimene anali kunyoza zidzawapeza

34Ndipo kudzanenedwa kuti, “Lero takuiwalani inu monga momwe inu mudaiwalira za tsiku lanuli. Ndipo malo anu okhala ndi ku Moto ndipo kumeneko sikudzakhala wina wokuthandizani.”

35“Ichi ndi chifukwa chakuti mudatenga chivumbulutso cha Mulungu ngati chinthu choseweretsa ndipo moyo wa padziko lino lapansi udakunyengani inu.” Motero patsiku limeneli, iwo sadzachotsedwa ndipo sadzaloledwa kukonza zolakwa zawo

36Motero kuyamikidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa Kumwamba ndi Ambuye wa padziko lapansi ndi Ambuye wa zolengedwa zonse

37Ndipo wake ndi Ufumu wakumwamba ndi padziko lapansi ndipo Iye ndi Wopambana ndi Wanzeru zonse

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath