40. Ghafir
1Ha-Mim
2Chivumbulutso cha Buku ili ndi chochokera kwa Mulungu, wamphamvu ndi wodziwa zonse
3Iye ndi amene amakhululukira machimo ndipo amavomera kulapa. Iye ndi wankhanza popereka chilango ndi Mwini chinthu chilichonse, ndipo kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kwa Iye chilichonse chidzabwerera
4Palibe amene amatsutsa chivumbulutso cha Mulungu kupatula okhawo amene sakhulupirira. Kotero usanyengedwe ndi kuyendayenda kwawo kwa m’mizinda
5Anthu a Nowa ndi anthu a magulu ena amene adadza pambuyo pawo adakana Atumwi, ndipo mtundu uliwonse udachita chiwembu pa Mtumwi wawo, kuti amugwire koteroanalikutsutsananayepazinthuzabodzandicholinga choletsa choonadi. Koma Ine ndidawaononga iwo! Kodi chilango changa chidali chowawa bwanji
6Kotero mawu a Ambuye wako adakwaniritsidwa kwa osakhulupirira ndipo iwo ndi amene adzakhala ku Moto
7Iwo amene amasunga Mpando wachifumu ndiponso iwo amene amauzungulira iwo, amatamanda Ambuye wawo ndi kukhulupirira mwa Iye ndipo amapempha chitetezo m’malo mwa iwo amene akhulupirira. “Ambuye wathu! Chifundo ndi nzeru zanu zimakhudza aliyense kotero atetezeni onse amene adza kwa Inu ndi kutsatira njira yanu ndiponso apulumutseni iwo ku chilango cha ku Gahena!”
8“Ambuye wathu! Alowetseni ku minda ya Paradiso imene inu mudawalonjeza iwo ndiponso iwo amene amachita zabwino, pakati pa atate, akazi ndi ana awo. Ndithudi Inu ndinu wamphamvu ndi wanzeru kwambiri
9“Ndipo apulumutseni ku ntchito zoipa. Aliyense amene Inu mumupulumutsa ku zoipa tsiku lalero ndiye kuti Inu mwamuonetsa chisoni chanu ndipo kumeneko ndiko kupambana kwambiri
10Ndithudi iwo amene sakhulupirira adzamva mkuwo ukuti, “Ndithudi mkwiyo wa Mulungu pa inu ndi waukulu kuposa chidani chimene inuyo mumadzionetsera nokha poona kuti munali kuitanidwa kuti mukhulupirire koma inu munali kukana.”
11Iwo adzati, “Ambuye wathu mudatipha kawiri konse ndipo mudatipatsa moyo kawiri. Tsopano ife tivomereza kuchimwa kwathu. Kodi sitingathe kupulumutsidwa ku chilango cha ku Moto?”
12“Ichi ndi chifukwa chakuti pamene dzina la Mulungu lokha linali kupembedzedwa, inu simudakhulupirire koma pamene milungu ina inali kupembedzedwa, inu mudakhulupirira. Kotero Mwini wake wa chiweruzo ndi Mulungu Wapamwamba ndi Wamkulukulu.”
13Iye ndiye amene amakulangizani inu zizindikiro zake ndipo amakutumizirani chakudya kuchokera ku mitambo. Koma okhawo amene akumbukira ndiwo amene amabwererakwa Mulungu
14Moteropembedzani Mulungu mmodzi yekha, ngakhale kuti anthu osakhulupirira sasangalala
15Wokweza maudindo anthu okhulupirira ndi Mwini Mpando wachifumu. Iye amatumiza chikumbutso chake kwa aliyense wa akapolo ake amene Iye wamufuna kuti akhoza kuchenjeza anthu za tsiku lachiweruzo
16Tsiku limene onse adzadza pamodzi, sipadzakhala china chilichonse chobisika kwa Mulungu. Kodi ndani adzakhala ndi ulamuliro wamphamvu pa tsikuli? Ndi Mulungu, mmodzi yekha, Mwini mphamvu zonse
17Tsiku limeneli, mzimu uliwonse udzalandira malipiro ake. Pa tsiku limeneli sikudzakhala kuponderezana. Ndithudi Mulungu ndi wachangu pobwezera
18Achenjeze iwo za tsiku limene lili pafupi kudza, limene mitima idzadza mpaka pakhosi ndi kuwakomola. Palibe bwenzi la pamtima kapena mkhalapakati wa anthu ochita zoipa amene adzayankhulire
19Mulungu amadziwa chinyengo cha maso ndi zimene mitima imabisa
20Ndipo Mulungu amaweruza mwachilungamo pamene iwo amene amapembedzedwa oonjezera pa Iye sangathe kuweruza. Ndithudi Mulungu amamva ndiponso amaona
21Kodi iwo sadayende pa dziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira anthu a makedzana? Iwo adali a mphamvu kuposa awa. Koma Mulungu adawalanga chifukwa cha zoipa zawo. Ndipo iwo adalibe wina aliyense wowateteza kwa Mulungu
22Ichi ndi chifukwa chakuti Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka ndi maso koma iwo adakana Atumwiwo. Kotero Mulungu adawaononga iwo. Ndithudi! Iye ndi Wamphamvu ndipo chilango chake ndi chowawa kwambiri
23Ndipo, ndithudi, tidamutumiza Mose ndi uthenga wathu ndi ulamuliro wooneka
24Kwa Farawo, Hamani ndi Karuni koma iwo adati, “Munthu wamatsenga ndi wabodza.”
25Ndipo pamene iye adawauza choonadi chochokera kwa Ife, iwo adati, “Iphani ana onse aamuna a anthu amene akhulupirira ndi iye ndipo musunge ana awo aakazi.” Koma ziwembu za anthu osakhulupirira sizitha bwino chifukwa zilibe maziko enieni
26Ndipo Farawo adati, “Mundisiye ine kuti ndiphe Mose ndipo musiyeni iye kuti apemphe kwa Ambuye wake. Ndithudi ine ndiopa kuti iye adzasintha chipembedzo chanu ndi kuyambitsa chisokonezo m’dziko.”
27Ndipo Mose adati, “Ndithudi ine ndithawira kwa Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti anditeteze kwa aliyense wamwano amene sakhulupirira mu tsiku lachiweruzo.”
28Ndipo munthu wamwamuna wokhulupirira wa m’gulu la anthu a Farawo amene adabisa chikhulupiriro chake adati, “Kodi inu mudzapha munthu chifukwa chakuti wanena kuti Ambuye wanga ndi Mulungu pamene iye wadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka zochokera kwa Ambuye wanu? Ndipo ngati iye ndi wabodza tchimo likhale pa iye yekha koma ngati iye ali kunena zoona, tsoka limene anena lidzagwa pa inu. Ndithudi Mulungu satsogolera munthu woswa malamulo ndi wabodza.”
29“oh inu anthu anga!wanu ndi ufumu walero. Inu muli ndi ulamuliro m’dziko koma ndani amene adzatithandiza ife ku chilango cha Mulungu ngati icho chitagwa pa ife?” Farawo adati, “Ine ndili kungokuuzani zinthu zimene ndimaona ndiponso ndili kukutsogolerani ku njira yoyenera.”
30Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh anthu anga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti inu mudzaona zimene zidadza pa anthu akale.”
31“Monga zimene zidadza kwa anthu a Nowa, a Aad ndi a Thamoud ndi iwo amene adadza iwo atachoka. Koma Mulungu safuna kupondereza akapolo ake.”
32“oh inu anthu anga! Ine ndichita mantha pa zimene zidzaoneka kwa inu pa tsiku louka kwa akufa.”
33Tsiku limene inu mudzabwerera ndi kuthawa. Inu simudzakhala ndi wokutetezani kwa Mulungu. Ndipo aliyense amene Mulungu amusiya kuti asochere palibe wina amene angamutsogolere
34Ndithudi Yosefe adadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka, koma inu munali kukayika pa zimene iye adabweretsa mpaka pamene iye adafa ndipo inu mudati, “Mulungu sadzadzutsanso Mtumwi wina pambuyo pa iye. Mmenemondimmene Mulunguamamusocheretsamunthu woononga ndi okayika
35Iwo amene amakana uthenga wa Mulungu popanda ulamuliro umene udapatsidwa kwa iwo, zochita zawo ndi zodedwa pamaso pa Mulungu ndi pamaso pa iwo okhulupirira. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaphimbira mtima wa munthu wonyada ndi wamwano
36Ndipo Farawo adati, “oh Hamani! ndimangire nsanja kuti ndikwere.”
37“Ndikwere kuti ndikafike kumwamba kuti ndimpeze Mulungu wa Mose koma ine, ndithudi, ndiganiza kuti iye ndi wonama.” Kotero ntchito zoipa za Farao zidaoneka zomusangalatsa, ndipo iye adasocheretsedwa ku njira yoyenera ndipo zochita zake sizinamuthandizechinachilichonseayikomachionongeko
38Ndipo iye amene adakhulupirira adati, “oh inu anthu anga! Nditsateni ine. Ine ndidzakutsogolerani ku njira yabwino.”
39“Oh inu anthu anga! Moyo wa pa dziko lino ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wosatha.”
40Aliyense amene achita zoipa adzalandira dipo loipa ndipo aliyense amene achita zabwino kaya ndi wamwamuna kapena wamkazi ndipo ndi wokhulupirira, otere adzalowa ku Paradiso kumene adzapatsidwa madalitso opanda muyeso
41“oh inu anthu anga! Kodi mwatani! Ine ndili kukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu muli kundiitanira ku moto?”
42“Inu muli kundiitana kuti ndisakhulupirire mwa Mulungu ndipo kuti ndizimufanizira Iye ndi zinthu zina zimene sindizidziwa pamene ine ndili kukuitanani kuti mudze kwa Mwini mphamvu ndi Mwini chikhululukiro.”
43“Mosakayika chimene muli kundiitanira chilibe dzina m’dziko lino ndi m’dziko limene lili nkudza ndipo kuti tidzabwerakwa Mulungu. Ndipoonseoswamalamulo, malo awo adzakhala ku moto.”
44“Ndipo inu mudzakumbukira zimene ndili kukuuzani ndipo ine ndiika chikhulupiriro changa mwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amaona akapolo ake.”
45Kotero Mulungu adamuteteza ku chiwembu chimene iwo adakonza ndipo anthu a Farawo chilango chonyansa chidawagwera
46Ku moto iwo adzasonkhanitsidwa m’mawa ndi madzulo ndipo chiweruzo chawo chidzagamulidwa pa tsiku limene ola lidzakwaniritsidwa ndi kuti, “Alangeni kwambiri anthu a Farawo.”
47Ndipo pamene iwo adzakangana wina ndi mnzake ku moto, anthu ochepa mphamvu adzati kwa iwo amene anali kuchita mwano, “Ndithudi ife tidali otsatira anu. Kodi simungatichotserepo chilango cha moto?”
48Iwo amene adali a mwano adzati, “Tonse tili kumoto. Zoonadi Mulungu waweruza pakati pa akapolo ake.”
49Ndipo iwo amene adzakhala kumoto adzati kwa iwo osunga Gahena, “Pemphani kwa Ambuye wanu kuti atichepetsere chilango chathu tsiku limodzi.”
50Iwo adzati, “Kodi kwa inu sikudabwere Atumwi anu ndi zizindikiro zooneka?” Iwo adzayankha kuti, “Inde.” Ndipo iwo adzati, “Kotero pemphani ngati mufuna koma pemphero la iwo amene alibe chikhulupiriro ndi lopanda pake.”
51Ndithudi Ife tidzapambanitsa Atumwi athu pamodzi ndi iwo amene amakhulupirira m’dziko lino ndi tsiku limene mboni zidzaitanidwa
52Tsikuli ndi limene madandaulo a anthu ochita zoipa adzakhala opanda ntchito. Ndipoiwo adzakhala kumalo oipa
53Ndipo Ife, ndithudi ,tidamupatsa Mose langizo. Ndipo tidapereka Buku loti lisungidwe ndi ana a Israyeli
54Ma langizo ndi chikumbutso kwa anthu ozindikira
55Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Ndipo pempha chikhululukiro cha machimo ako ndipo lemekeza Ambuye wako madzulo ndi m’mawa
56Ndithudi iwo amene amatsutsa mawu a Mulungu wopanda lamulo limene ladza kwa iwo, alibe china chilichonse m’mitima mwawo kupatula chilakolako choti akhale a pamwamba koma iwo sadzakhala. Kotero funafuna chitetezo cha Mulungu. Ndithudi Iye amamva ndipo amaona
57Ndithudi chilengedwe cha kumwamba ndi dziko lapansi ndi choposa chilengedwe cha anthu. Koma anthu ambiri sadziwa
58Ndithudi anthu a khungu ndi anthu openya siofanana ndiponso amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino ndi anthu ochita zoipa (safanana). Ndi zochepa zomwe mumakumbukira
59Ndithudi ola lidzadza, mosakayika, koma anthu ambiri sakhulupirira
60Ndipo Ambuye wako adati, “Ndipempheni Ine ndipo ndidzayankha pemphero lanu. Ndithudi! Koma iwo amene ndi amwano pondipembedza Ine, ndithudi, adzaponyedwa ku Gahena mochititsa manyazi.”
61Ndi Mulungu amene adalenga usiku kuti inu muzipumula ndi usana kuti ukupatseni kuwala. Ndithudi Mulungu amaonetsa chisomo chake kwa anthu koma anthu ambiri sathokoza ayi
62Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu, Namalenga wa zinthu zonse. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Nanga ndi chifukwa chiyani inu mumanyengedwa ndi kusiya choonadi
63Mmenemo ndi mmene adasiyira choonadi iwo amene adakana uthenga wa Mulungu
64Ndi Mulungu amene adalenga dziko lapansi kukhala malo anu okhalamo ndi mtambo ngati chotchinga. Iye ndiye amene adaumba matupi anu ndipo adawaumba ndi maonekedwe abwino ndipo wakupatsani inu zinthu zabwino. Ameneyu ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Ulemerero ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse
65Iye ndi wamuyaya. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mupempheni Iye ndipo mudzipereke kwathunthu kwa Iye yekha. Ulemerero wonse ukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse
66Nena, “Ine ndinaletsedwa kupembedza iwo amene inu mumapembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni pamene malangizo abwino anadza kwa ine kuchokera kwa Ambuye wanga. Ndipo ine ndalamulidwa kuti ndizimvera Ambuye wa zolengedwa zonse
67Ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo kuchokera ku dontho la umuna losakanizana ndi ukazi ndi kuchokera ku magazi oundana ndipo amakutulutsani kukhala mwana ndipo amakukuzani kufika pa msinkhu wanu ndi kukhala wamphamvu, ndipo Iye amakukalambitsani. Ngakhale ena a inu amafa msanga, Iye amakusiyani inu kuti mufike patsiku loikidwa kuti mukhoza kuzindikira
68Iye ndiye amene amapereka moyo ndi imfa ndipo pamene Iye afuna chinthu, Iye amangonena kwa icho kuti, “Khala” ndipo chimakhala
69Kodi siudawaone iwo amene amatsutsa uthenga wa Mulungu? Kodi iwo amabwezedwa bwanji ku choonadi
70Iwo amene amakana Buku ndi uthenga umene tidatumiza ndi Atumwi athu, koma posachedwapa iwo adzadziwa
71Pamene magoli ndi unyolo udzakhala pa khosi pawo, iwo adzaduduluzidwa
72M’madzi owira ndipo iwo adzatenthedwa ku moto
73Ndipo zidzanenedwa kwa iwo, “Kodi zili kuti izo zimene munali kuzipembedza?”
74“Poonjezera Mulungu?” Iwo adzati, “Zatithawira. Iyayi ife sitimapembedza zina zake.” Kotero Mulungu amasocheretsa anthu osakhulupirira
75Ichi ndi chifukwa chakuti inu munali kusangalala ndi zinthu zachabechabe padziko ndipo munali ndi mwano
76Lowani m’zipata za ku Gahena kuti mukhale m’menemo. Iwowo ndi malo oipa omwe anthu onyada adzakhaleko
77Kotero pirira. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kaya tikuonetsa gawo la zimene tili kuwaopseza nazo kapena tikupha, komatu kwa Ife iwo adzabwerera
78Ndithudi Ife tidatumiza Atumwi iwe usanabadwe. Alipo ena amene takuuza za iwo ndipo alipo ena amene sitidakuuze za iwo ndipo sichidali choyenera kuti Mtumwi abweretse chizindikiro kupatula ndi chilolezo cha Mulungu. Koma pamene ulamuliro wa Mulungu udadza, chiweruzo chidaperekedwa mwachilungamo. Ndipo onse, amene ankati ndi zabodza, adatayika
79Mulungu ndiye amene adakulengerani nyama kuti mukhoza kukwera zina za izo ndi kudya zina za izo
80Ndipo muli zambiri zabwino mu nyamazo kuti inu mukhoza kukwaniritsa zofuna zanu zimene zili m’mitima mwanu.Ndipopaizondim’masitimainumumanyamulidwa
81Ndipo Iye amakuonetsani zizindikiro zake. Kodi ndi ziti za zizindikiro za Mulungu zimene mumakana
82Kodi inu simudayende m’dziko ndi kuona zimene zidawachitikira anthu ena amene adalipo iwo asanabadwe? Iwo adali ambiri kuposa awa ndipo adali ndi mphamvu zambiri. Ndipo mwa zinthu zomwe iwo adazisiya pa dziko lapansi ndi zomwe anali kuchita, zonsezi sizidawathandize
83Pamene Atumwi awo adadza kwa iwo ndi zizindikiro zooneka, iwo adadzitama chifukwa cha nzeru zimene adali nazo. Ndipo chimene anali kutsutsa chidagwa pa iwo
84Koma pamene iwo adaona chilango chathu, iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Mulungu mmodzi yekha ndipo tili kuzikana zonse zimene tidali nazo zoonjezera pa Iye.”
85Koma chikhulupiriro chawo sichidawathandize china chilichonse pamene adaona chilango chathu. Ili ndi lamulo la Mulungu limene amaweruzira akapolo ake. Ndipo pamenepo, anthu okana Mulungu adatayika kwambiri
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath