Chisilamu
kubwerera

37. As-Saaffaat

1Pali iwo amene amasonkhana kukhala pa maudindo osiyanasiyana

2Pali iwo amene amayendetsa mitambo mwa ubwino

3Pali iwo amene amabweretsa m’Buku ndi Korani kuchokera kwa Mulungu kupita nalo kwa anthu ake

4Ndithudi Mulungu wanu ndi mmodzi yekha

5Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi wa zonse zimene zili m’menemo ndi Ambuye wa dera lililonse lotulukira dzuwa

6Ndithudi Ife tidakongoletsa mtambo woyandikira kwambiri ndi nyenyezi

7Ndi kulonda Satana wofukira

8Kotero iwo sangathe kumvetsera zokambidwa za gulu lapamwamba chifukwa iwo amapirikitsidwa kuchokera kumbali iliyonse

9Atapirikitsidwa, chawo chidzakhala chilango chosatha

10Kupatula yekhayo amene amakwatula zinthu mwakuba, ndipo amathamangitsidwa ndi moto woyaka ndi wowala kwambiri

11Ndipo tawafunsa, “Kodi iwo ndi a mphamvu kuposa zolengedwa zina zimene tidalenga?” Iwo tidawalenga kuchokera ku dothi lonyata la makande

12Iyayi, iwe udadabwa pamene iwo anali kunyoza

13Ndipo iwo akamaweruzidwa, iwo safuna kuweruzidwa

14Ndipo iwo akaona chizindikiro chochokera kwa Mulungu amachisandutsa ngati chinthu choseweretsa

15Ndipo amati, “Ichi si china ayi koma matsenga woonekera poyera.”

16“Chiyani! Ife tikafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tidzaukitsidwa?”

17“Ndiponso makolo athu amakedzana?”

18Nena, “Inde mudzachititsidwa manyazi.”

19Ndipo udzakhala mfuwu umodzi ndipo taona iwo adzakhala ali kupenyetsetsana

20Iwo adzati, “Tsoka kwa ife! Ili ndi tsiku lachiweruzo.”

21“Ili ndi tsiku lachiweruzo limene inu mumati ndi bodza.”

22(Kudzanenedwa kuti); “Bweretsani anthu ochimwa pamodzi ndi anzawo ndi zinthu zimene iwo anali kupembedza.”

23“Kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo atsogolereni ku njira ya kumoto.”

24“Ndipo aimitseni. Ndithudi, iwo ayenera kufunsidwa.”

25“Kodi mwatani? Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuli kuthandizana?”

26Iyayi! Koma iwo lero ndi odzipereka

27Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake

28Iwo adzati, “Ndinu amene munali kubwera kwa ife kuchokera kudzanja lamanja.”

29Iwo adzayankha kuti, “Iyayi, Inuyo simunali okhulupirira.”

30“Ndipo ife tidalibe ulamuliro pa inu. Iyayi! Inu mudali osamva.”

31“Kotero chiweruzo cha Ambuye wathu chadza pa ife. Ndithudi tsopano tidzachilawa.”

32“Choncho ife tidakusocheretsani chifukwa nafenso tidali osochera.”

33Ndipo, ndithudi, patsiku limeneli onse adzalandirana chilango pakati pa wina ndi mnzake

34Ndithudi mmenemo ndi mmene timachitira ndi anthu olakwa

35Ndithudi pamene iwo, adauzidwa kuti, “Kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni, iwo anali kudzitukumula.”

36Ndipo adanena kuti, “Kodi ife tisiye milungu yathu chifukwa cha Mlakatuli wamisala?”

37Iyayi. Iye wadza ndi choonadi ndipo ali kutsimikizira uthenga wa Atumwi amene adadza kale

38Ndithudi, inu mudzalangidwa kwambiri

39Ndipo inu mudzalandira mphotho molingana ndi ntchito zanu

40Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu

41Kwa iwo mphotho yawo ndi yodziwika

42Zipatso ndipo iwo adzalemekezeka kwambiri

43M’minda ya chisangalalo

44Atakhala pa mipando ya chifumu moyang’anizana

45Pakati pawo padzaperekedwa chikho cha vinyo wabwino

46oyera ndiponso okoma kwa iwo amene amamwa

47Simudzakhala mavuto mu icho ndipo sichidzawatopetsa

48Ndipo pakati pawo padzakhala akazi angwiro opanda chimasomaso

49Okhala ngati mazira osamalidwa bwino

50Ndipo adzadza kwa anzawo ndi kumafunsana wina ndi mnzake

51Wina wochokera pakati pawo adzayankhula nati, “Ndithudi ine ndinali ndi bwenzi langa.”

52“Amene amakonda kunena kuti; “Kodi ndiwe mmodzi mwa okhulupirira?”

53“Kodi ife tikafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, tidzatengedwa kupita ku chiweruzo

54Iye adati, “Kodi iwe ungaone pansi?”

55Motero adayang’ana pansi ndipo adamuona iye ali pakati pa moto wa ku Gahena

56Iye adati, “Pali Mulungu! Iwe udatsala pang’ono kundipweteka.”

57“Ndipo kukadapanda chisomo cha Ambuye wanga ine, ndithudi, ndikadakhala mmodzi wa iwo.”

58“Kodi ndiye kuti ife sitidzafa?”

59“Kupatula kufa koyamba, kodi ife sitidzalangidwa?”

60Ndithudi uku ndiko kupambana kwenikweni

61Pofuna kupeza zotere, alekereni alimbikire amene akufuna kuti alimbikirewo

62Kodi chimenechi ndi chabwino kapena mtengo wa Zaqqum

63Ndithudi tazipanga izi kukhala mayesero kwa anthu olakwa

64Ndithudi umenewu ndi mtengo umene umamera pansi pa Gahena

65Zipatso zake zili ngati mitu ya a Satana

66Ndithudi iwo adzadya zimenezi ndi kukhutitsa mimba zawo ndi zipatsozo

67Ndithudi iwo akadzadya, adzamwa chakumwa chokonzedwa ndi madzi owira

68Ndithudi iwo adzapita ku Gahena

69Ndithudi iwo adapeza makolo awo ali osochera

70Kotero iwo ali kutsatira mapazi awo

71Ndithudi makolo awo adasochera iwo asanadze

72Ndipo, ndithudi, ife tidatumiza Atumwi pakati pawo

73Ndipo taona zimene zidadza kwa iwo amene adachenjezedwa

74Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu omwe ndi anthu olungama

75Ndipo ndithudi Nowa adatipempha Ife ndipo Ife timayankha bwino pa amene amayankha

76Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi banja lake ku chilango choopsa

77Ndipo tidapulumutsanso ana ake

78Ndipo tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mitundu yonse yamtsogolo

79Mtendere ukhale kwa Nowa kuchokera kwa zolengedwa zonse

80Ndithudi mmenemo ndi mmene timalipirira anthu ochita zabwino

81Ndithudi iye adali mmodzi mwa akapolo athu okhulupirira

82Ndipo ena onse tidawamiza

83Ndithudi pakati pa iwo amene amatsatira njira yake adali Abrahamu

84Pamene iye adadza kwa Ambuye wake ndi mtima woyera

85Pamene iye adati kwa atate wake ndi anthu a mtundu wake, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”

86“Kodi mukufuna milungu yabodza kapena Mulungu weniweni?”

87“Kodi mukuganiza zotani za Ambuye wa zolengedwa zonse?”

88Ndipo iye adayang’ana nyenyezi

89Ndipo iye adati, “Ndithudi ndili kudwala.”

90Kotero iwo adamusiya ndi kubwerera

91Ndipoiyeadayang’anakwamilunguyawonati, “Kodi inu simudya?”

92“Kodi bwanji inu simuyankhula?”

93Ndipo iye adadza pafupi ndi iyo ndi kuigwetsa ndi dzanja lake lamanja

94Nthawi yomweyo wopembedza mafano adadza kwa iye mwamsangamsanga

95Iye adati, “Kodi mumapembedza zinthu zimene inu mwasema?”

96“Pamene Mulungu ndiye amene adakulengani inu pamodzi ndi zosemasema zanuzi!”

97Iwo adati, “Mupangireni ng’anjo ndipo muponyeni m’moto woyaka!”

98Iwo adachita chiwembu koma Ife tidawachititsa manyazi

99Ndipo iye adati, “Ine ndithawira kwa Ambuye wanga. Ndipo Iye adzanditsogolera ine.”

100“Ambuye wanga! Ndipatseni ana kuchokera kwa ochita ntchito zabwino.”

101Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wamwamuna wopirira

102Ndipo pamene iye adakula mofika pa msinkhu woti angathe kuthandiza abambo ake, iye adati: “Mwana wanga! Ndithudi ine ndalota ndili kukupha ngati nsembe. Taganiza zimene uli kuziona.” Iye adati, “Atate wanga! Inu chitani monga momwe mwalamulidwira. Ngati Mulungu afuna, mudzandipeza ine wopirira!”

103Ndipo pamene onse adadzipereka, ndipo adamugoneka iye chafufumimba

104Ndipo Ife tidamuitana ndipo tidati, “Iwe Abrahamu!”

105“Ndithudi wakwaniritsa maloto ako.” Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita zabwino

106Ndithudi awa adali mayesero oonekeratu

107Ndipo tidamupatsa iye nsembe yaikulu

108Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu pa iye pakati pa mibadwo yamtsogolo

109Mtendere ukhale pa Abrahamu

110Mmenemo ndi mmene timalipira mphotho kwa anthu ochita zabwino

111Ndithudi iye adali mmodzi wa akapolo athu okhulupirira

112Ndipo Ife tidamuuza nkhani yabwino ya Isake, Mtumwi, wochokera pakati pa anthu okhulupirira

113Ndipo Ife tidaika madalitso athu pa iye ndi pa Isake. Ndipo pakati pa ana awo pali ena ochita ntchito zabwino ndi ena amene ndi olakwa ndipo amadzipondereza okha

114Ndipo, ndithudi, Ife tidaonetsa chisomo chathu kwa Mose ndi Aroni

115Ndipo tidawapulumutsa onse pamodzi ndi anthu awo ku mavuto oopsa

116Ndipo Ife tidawathandiza kotero adali opambana

117Ndipo Ife tidawapatsa Buku Lopatulika limene limathandiza kufotokoza zinthu momveka bwino

118Ndipo Ife tidawatsogolera ku njira yoyenera

119Ndipo Ife tidakhazikitsa ulemu kwa iwo pakati pa mibadwo ya mtsogolo

120“Mtendere ukhale pa Mose ndi Aroni.”

121Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino

122Ndithudi onse adali akapolo athu okhulupirira

123Ndithudi Eliya anali mmodzi wa Atumwi

124Pamene, iye adati kwa anthu ake, “Kodi inu simungaope Mulungu?”

125“Kodi muli kupembedza Bala ndi kusiya kupembedza Namalenga?”

126“Mulungu, Ambuye wanu ndi Ambuye wa makolo anu akale?”

127Koma iwo adamukana iye ndipo ndithudi, iwo adzatengedwa

128Kupatula akapolo osankhidwa a Mulungu

129Ndithudi tidakhazikitsa ulemu kwa iye pakati pa mibadwo ya patsogolo

130“Mtendere ukhale ndi Eliya.”

131Ndithudi mmenemo ndi mmene timaperekera mphotho kwa anthu ochita ntchito zabwino

132Ndithudi iye adali mmodzi wa akopolo athu okhulupirira

133Ndipo Loti adali mmodzi wa Atumwi

134Pamene, Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi onse omutsatira

135Kupatula mayi mmodzi wokalamba amene adali m’gulu la anthu otsalira m’mbuyo

136Ndipo Ife tidawaononga onse

137Ndithudi inu mumawadutsa nthawi ya m’mawa

138Ndi nthawi yausiku, kodi inu simungazindikire

139Ndipo, ndithudi, Yona adali mmodzi wa Atumwi

140Pamene iye adathawa kupita ku chombo chodzadza kwambiri ndi katundu

141Iye adachita nawo mayere koma iye adali mmodzi wa olephera

142Ndipo nsomba idamumeza iye chifukwa adalakwa

143Koma kukadakhala kuti sadapemphe chikhululukiro cha Mulungu wolemekezeka

144Ndithudi iye akadakhalabe m’mimba mwa nsomba mpaka tsiku la kuuka kwa akufa

145Koma Ife tidakamuponya pa mtunda pamene iye anali kudwala

146Ndipo Ife tidameretsa chitsamba cha chipanda kuti chimere pamwamba pake

147Ndipo tidamutumiza kwa anthu zikwi makumi khumi kapena kuposa apa

148Ndipo onse adakhulupirira ndipo Ife tidawapatsa chisangalalo cha kanthawi kochepa

149Ndipo tsopano afunseni kuti, “Kodi Ambuye wako ali ndi ana

150Kapena kuti Ife tidalenga angelo kukhala akazi pamene iwo anali kuona

151Kodi iwo sanena zabodza pamene amati

152“Mulungu wabereka mwana?” Ndithudi iwo ndi abodza

153Kodi iye adasankha ana aakazi m’malo mwa ana aamuna

154Kodi mwatani? Kodi mumaweruza bwanji

155Kodi simungaganize bwino

156Kapena kodi inu muli ndi ulamuliro weniweni

157Kotero bweretsani Buku lanu ngati ndinu olungama

158Ndipo iwo akhazikitsa ubale pakati pa Mulungu ndi majini. Koma majini amadziwa kuti iwo adzatengedwa kupita kwa Iye

159Ulemerero ukhale kwa Mulungu. Iye ali pamwamba pa zimene amamuyerekeza nazo

160Kupatula akapolo a Mulungu, amene Iye amasankha

161Ndithudi inu pamodzi ndi zimene mupembedza

162Simungathe kusocheza wina aliyense

163Kupatula okhawo amene adzapita ku moto wa ku Gahena

164Aliyense wa Ife ali ndi malo ake ake

165Ndithudi ndife amene timaima pa mizere kupemphera

166Ndipo, ndithudi, ndife amene timamulemekeza

167Ndipo, ndithudi, iwo anali kunena kuti

168“Tikadakhala ndi chikumbutso monga chomwe chinali ndi anthu akale.”

169“Ife, ndithudi, tidakhala akapolo osankhidwa a Mulungu.”

170Koma iwo sakhulupilira mu izi komabe iwo adzadziwa

171Ndithudi mawu athu adatsogola kwa akapolo athu omwe ndi Atumwi athu

172Kuti iwo, ndithudi, adzathandizidwa

173Ndipo, ndithudi, gulu lathu lokha lidzakhala lopambana

174Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa

175Ndipo uwaone ndipo iwo adzadzioneranso

176Kodi iwo afuna kufulumizitsa chilango chathu

177Koma pamene icho chidzadza pa iwo, udzakhala m’mawa woipa kwa iwo amene adachenjezedwa

178Kotero uyambe wawasiya okha kwa kanthawi kochepa

179Ndipo uwaone ndipo nawo adzaona

180Ulemerero ukhale kwa Ambuye wako, Ambuye wolemekezeka ndi wamphamvu, kuposa zimene ali kumukundikira

181Ndipo mtendere ukhale kwa Atumwi onse

182Ndipo kuyamikidwa ndi kuthokoza konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengedwa zonse

gwero: Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

WEBREATH · 11:11

«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7

Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.

WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath