34. Saba
1Kuyamikidwa konse ndi kwa Mulungu Mwini wa chilichonse chakumwamba ndi dziko lapansi ndipo kuyamikidwa konse ndi kwake m’dziko limene lili nkudza. Ndipo Iye ndi waluntha ndi wozindikira
2Iye amadziwa chilichonse chimene chimalowa m’nthaka ndi chilichonse chimene chimatuluka mu iyo ndi chilichonse chimene chimatsika kuchokera kumwamba ndi chimene chimakwera kunka kumwamba. Ndipo Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini kukhululukira
3Ndipoiwoamenesakhulupiriraamati,“Olasilidzabwera kwaife.” Nena,“Inde! PaliAmbuyewanga, ameneamadziwa zinthu zosaoneka. Ndithudi, olalo lidzadza kwa inu.” Palibe chinthu cholemera ngati mbewu ya mpiru chimene chimabisika kwa Iye kumwamba kapena pa dziko lapansi kapena chochepera kuposa ichi kapena chachikulu kuposa ichi chifukwa zonse ndi zolembedwa bwino m’Buku
4KoterokutiIyeakhozakulipiraonseameneamakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Awa ndiwo amene adzakhululukidwa ndiponso adzalandira malipiro abwino
5Ndipo iwo amene amalimbikira kutsutsa chivumbulutso chathu, awa ndiwo amene chilango chowawa ndi chonyansa chili kuwadikirira
6Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru amaona kuti chimene chapatsidwa kwa iwe kuchoka kwa Ambuye wako ndi choonadi ndipo chimatsogolera ku njira ya Mwini mphamvu ndi Mwini kuyamikidwa
7Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Kodi tingakulangizeni amene amakuuzani kuti pamene inu musanduka dothi mudzalengendwanso kukhala m’badwo watsopano?”
8Kodi iye wapeka bodza lokhudza Mulungu kapenaiyendiwamisala? Iyayi! Iwondiamenesakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ndipo ali mu chilango chachikulu m’maganizo ndiponso ndi olakwa kwambiri
9Kodi iwo saganiza za chimene chili patsogolo pawo ndi chimene chili pambuyo pawo chokhudza zinthu za kumwamba ndi pa dziko lapansi? Ngati Ife titafuna, tidzawachotsa pa dziko kapena kuwabweretsera gulu lochokera kumwamba. Ndithudi muli chiphunzitso mu chimenechi kwa kapolo aliyense amene amatembenukira kwa Mulungu
10Ndithudi tidamupatsa Davide zabwino zochokera kwa Ife. Oh inu mapiri! Imbani nyimbo zotamanda pamodzi ndi iye ndipo pamodzi ndi mbalame. Ndipo tidapanga chitsulo kukhala chofewa kwa iye
11Tidati, “Panga majasi okwanira ndipo khazikitsa nthawi yopangira zovala ndipo chita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndili kuona chilichonse chimene umachita.”
12Ndipo tidalenga mphepo kukhala yoleza kwa Solomoni imene inali kuyenda ulendo wa mwezi umodzi masana ndi ulendo wa mwezi umodzi usiku. Ndipo tidalenga kasupe amene anali kumutulutsira mkuwa. Ndipo padali majini amene anali kumugwirira ntchito ndi chilolezo chaAmbuye wake ndipo aliyense amene sanali kumvera malamulo athu, tinali kumulanga ndi moto
13Iwo adamuchitira zonse zimene ankazifuna, malinga ndi zithunzithunzi ndi mbiya zazikulu zothirira maluwa ndi zophikiramo zokhazikika. Thokozani a m’banja la Davide! Koma ochepa mwa akapolo anga ndiwo amathokoza
14Ndipo pamene tidalamula kuti afe, palibe china chilichonse chimene chidawadziwitsa kuti wafa koma mphutsi imene inali kudya ndodo yake ndipo pamene iye adagwa, majini adadziwa kuti iwo akadadziwa za zinthu zobisika, sakadapitirira kugwira ntchito yowawa yodikira
15Ndithudi kunali chizindikiro kwa onse a Saba m’chikhalidwe chawo. Minda iwiri ku dzanja lamanja ndi minda iwiri kudzanja lamanzere. Idyani zabwino zochokera kwa Ambuye wanu ndipo mumuyamike Iye. Kwa iye kuli dziko labwino ndiponso ndi Ambuye wokhululukira
16Koma iwo sadamvere ayi. Kotero ife tidawatumizira madzi osefukira kuchokera ku madamu amene sadathe kuwatseka ndipo m’malo mwa minda yawo iwiri, Ife tidawapatsa minda iwiri yobereka zipatso zowawa ndi mitengo ina ya minga
17Ife tidawalanga chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo Ife sitilanga wina aliyense koma anthu osathokoza
18Ndipo tidakhazikitsa pakati pawo mizinda imene tidaidalitsa ndi mizinda ina imene imaoneka msanga ndipo tidawakonzera ulendo wosavuta. Yendani mwamtendere usiku ndi usana
19Ndipo iwo adati, “oh Ambuye wathu! Titalikitsireni mitunda yoti tiziyendamo.” Ndipo iwo adzipondereza okha. Kotero Ife tidawasandutsa kukhala nkhaniimeneimakambidwakambidwandipotidawamwaza m’magulumagulu. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa aliyense amene amapirira ndi kuthokoza
20Ndithudi Satana adakwanitsa zofuna zake pa iwo ndipo iwo adamutsatira iye kupatula gulu limene lidakhulupirira
21Koma iye adalibe ulamuliro pa iwo kupatula kuti Ife tikhoza kuyesa munthu amene amakhulupirira za moyo umene uli nkudza ndi iye amene sakhulupirira za moyowo. Ndipo Ambuye wako amayang’ana chinthu china chilichonse
22Nena, “Itanani onse amene mumawapembedza kuonjezera pa Mulungu. Iwo alibe ulamuliro pa chinthu ngakhale chaching’ono cha kumwamba kapena padziko lapansi ndipo iwo alibe gawo lililonse mu izo. Ndipo iye alibe wina aliyense womuthandiza kuchokera pakati pawo
23Palibe dandaulo limene lingamveke kwa Iye kupatula lokhalo lochokera kwa iye amene walandira chilolezo chake. Mpaka pamene mantha adzachotsedwa m’mitima mwawo, iwo adzati, “Kodi ndi chiyani chimene Ambuye wanu walamulira?” Iwo adzati, “Choonadi. Ndipo Iye ndi wapamwamba ndi wamkulu.”
24Nena, “Kodi ndani amene amakupatsani zabwino kuchokera kumwamba ndi pa dziko lapansi?” Nena: “Mulungu.” Ndithudi mwina ife kapena inu muli pa njira yachilungamo kapena ochimwa zedi
25Nena “Inu simudzafunsidwa za machimo athu ndiponso ife sitidzafunsidwa za zimene mudachita.”
26Nena, “Ambuye wathu adzatisonkhanitsa tonse pamodzi ndipo pomaliza adzaweruza pa mikangano yathu mwa choonadi ndi mwachilungamo. Iye ndiye amene adzaweruza. Ndipo Iye amadziwa zinthu zonse.”
27Nena, “Ndilangizeni zimene inu muli kuzipembedza kuonjezera pa Mulungu. Iyayi! Iye ndi Mulungu, Mwini mphamvu ndi Mwini nzeru.”
28Takutumiza iwe kwa anthu a mitundu yonse kuti uwauze uthenga wabwino ndi kuwachenjeza. Koma anthu ambiri sadziwa zimenezi
29Iwo amati, “Kodi lonjezo ili lidzakwaniritsidwa liti ngati uli kunena zoonadi?”
30Nena, “Tsiku lanu lidakhazikika kale ndipo inu simungaonjezere kapena kubwezera m’mbuyo ngakhale ola limodzi.”
31Ndipo iwo amene sakhulupirira amati, “Ife sitidzakhulupirira mu Buku la Korani kapena mu icho chimene chidadza kale. Ndipo iwe ukadaona pamene anthu ochita zoipa adzaimirira pamaso pa Ambuye wawo ali kudzudzulana wina ndi mnzake! Iwo amene ankati ndi ofoka adzanena kwa anthu opulupudza kuti, “Pakadapanda inu, ndithudi, ife tikadakhala okhulupirira!”
32Iwo amene adali onyada adzati kwa iwo amene ankati ndi ofoka kuti, “Kodi ife tinakukanizani kutsatira langizo pamene lidadza kwa inu? Iyayi. Nokha mudachimwa.”
33Iwo amene ankati ndi ofoka adzati kwa iwo amene adali onyada, “Iyayi! Inu munkakonza chiwembu usiku ndi usana ndipo mumatiuza ife kuti tisakhulupirire mwa Mulungu koma kukhazikitsa mafano kuonjezera pa Iye.” Ndipo iwo adzabisa kukhumudwa kwawo pamene adzaone chilango ndipo Ife tidzaika magoli m’makosi mwa iwo amene sadakhulupirire. Iwo sadzakhululukidwa pa zimene adachita
34Ife sitidatumizepo Mchenjezi ku mzinda wina uliwonse umene anthu ake opeza bwino sadanenepo mawu oti, “Ndithudiifesitikhulupirirauthengaumenewatumizidwa.”
35Ndipo iwo adati, “Ife tili ndi chuma chambiri ndiponso ana, kotero ife sitidzalangidwa ayi.”
36Nena, “Ndithudi Ambuye wanga amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndi monyalapsa kwa aliyense amene Iye wamufuna. Koma anthu ambiri sadziwa.”
37Si chuma kapena ana anu amene adzakufikitsani kufupi ndi Ife koma okhawo amene amakhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino. Otere ndiwo amene ali ndi malipiro odzala manja awiri chifukwa cha ntchito zawo ndipo adzakhala mwamtendere pamalo olemekezeka
38Ndipo onse amene amalimbikira kutsutsa chiphunzitso chathu adzalangidwa
39Nena, “Ndithudi Ambuye wanga amapereka moolowa manja kwa aliyense wa akapolo ake amene wamufuna ndipo amachepetsa za aliyense amene wamufuna. Ndipo chilichonse chimene mupereka, Iye amalipira mowirikiza ndipo Iye ndiye amapereka kwambiri.”
40Patsiku limene adzawasonkhanitsa onse pamodzi ndi kuwafunsa Angelo kuti, “Kodi ndinu amene anthu awa anali kupembedza?”
41Angelo adzati, “Ulemerero ukhale kwa Inu! Inu ndinu Mtetezi wathu osati iwo ayi. Iyayi! Iwo anali kupembedza majini ndipo ambiri a iwo anali kukhulupirira mwa iwo.”
42Kotero patsiku limeneli, iwo sadzakhala ndi mphamvu zothandizana kapena kupwetekana wina ndi mnzake. Ndipo Ife tidzati kwa anthu ochimwa. “Lawani chilango cha moto chimene inu munali kuchikana.”
43Pamene chiphunzitso chathu chomveka chimalalikiridwa kwa iwo, iwo amati, “Uyu ndi munthu amene afuna kukuletsani chipembedzo cha makolo anu.” Ndipo iwo amati, “Ili ndi bodza limene wapeka.” Ndipo anthu osakhulupirira, pamene choonadi chidza kwa iwo amati, “Awa ndi matsenga.”
44Ife sitidawatumizire mabuku kuti awaphunzitse kapena kuwatumizira Atumwi iwe usanadze ngati wowachenjeza
45Ndipo iwo amene analipo kale iwo asanadze adakana choonadi. Awa sadalandire, ngakhale gawo la chikhumi la zimene tidawapatsa iwo. Komabe pamene iwo adakana Atumwi anga, kodi chilango changa chinali chowawa bwanji
46Nena, “Ine ndili kukufunsani kuti muchite chinthu chimodzi choti muime pamaso pa Mulungu awiriawiri kapena aliyense payekha ndipo muganize painu nokha. M’bale wanu si wamisala ayi. Iye ali kungokuchenjezani chilango chowawa chisanadze.”
47Nena, “Malipiro ena aliwonse amene ndidakufunsani ndi anu chifukwa malipiro anga ali ndi Mulungu ndipo Iye ndi mboni pa zinthu zonse.”
48Nena, “NdithudiAmbuye wanga amanena zoona ndipo ndi Mwini wodziwa zinthu zobisika.”
49Nena, “Choonadi chadza ndipo bodza latha ndipo silidzabwereranso.”
50Nena, “Ngati ine ndilakwa, ndilakwira mzimu wanga ndipo ngati ndatsatira njira yolungama ndi chifukwa cha zimene Ambuye wanga amavumbulutsa kwa ine. Ndithudi Iye amamva ndipo ali pafupi.”
51Ndipo iwe ukadangoona nthawi imene adzachite mantha komabe iwo sadzathawa ndipo iwo adzagwidwa asanapitepatali
52Ndipoiwoadzati,“Ifetilikukhulupirira.” Kodi kukhulupirira kwawo kudzawathandiza bwanji kuchokera kutali
53Ndipo iwo sadakhulupirire kale ndipo amanena kuti ndi nkhani za m’maluwa kuchokera kutali
54Ndipo chipupa chidzakhazikitsidwa pakati pawo ndi zofuna zawo monga momwe adachitira ndi anthu ena a kale. Ndithudi iwo ndi okayika kwambiri
WEBREATH · 11:11
«If you are thankful, I will give you more» — Quran 14:7
Breath is one for all: everyone lives by it, whoever they are and whatever they believe. Every day at 11:11 local time people stop for sixty seconds, breathe, and thank GOD for the breath — each in their own words, each within themselves. In that minute we are One Breath.
WEBREATH — the Minute at 11:11, your own local time — we are One Breath